LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 April tsa. 3
  • Limbikitsani Ena ndi Mau Abwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Limbikitsani Ena ndi Mau Abwino
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amakondwela Tikamapemphelela Ena
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • “Yembekezela Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 April tsa. 3

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 16-20

Limbikitsani Ena ndi Mau Abwino

Zokamba zathu ziyenela kulimbikitsa ena

16:4, 5

  • Yobu anali wopsinjika maganizo ndi wothedwa nzelu, cakuti anafuna thandizo ndi cilimbikitso kwa ena

  • Anzake atatu a Yobu sanakambe mau alionse omulimbikitsa. M’malomwake, anamuimba mlandu ndi kuonjezela nkhawa zake

Mau oipa a Bilidadi anacititsa Yobu kulila mosautsidwa mtima

19:2, 25

  • Yobu analilila kwa Mulungu kuti amuthandize, ngakhale kum’pempha kuti afe

  • Yobu anali ndi ciyembekezo cakuti adzaukitsidwa, ndipo anapitiliza kupilila mokhulupilika

Elifazi akukamba ndi Yobu pamene Bilidadi ndi Zofari akuwayang’ana

ANTHU AMENE ANAIMBA MLANDU YOBU

Elifazi

Elifazi:

  • Mwina anali kucokela ku Temani, m’dziko la Edomu. Pa Yeremiya 49:7 pamafotokoza kuti Temani linali likulu la anthu anzelu a ku Edomu

  • N’kutheka kuti ndiye anali wamkulu pa “otonthoza” anzake, ndipo ndiye anayambilila kukamba. Iye anakamba ndi Yobu katatu konse ndipo anakamba kwa nthawi yaitali kuposa anzake

Zimene anamuneneza:

  • Anakaikila kukhulupilika kwa Yobu, ndipo anakamba kuti Mulungu sakhulupilila atumiki ake (Yobu 4, 5)

  • Anauza Yobu kuti anali wonyada ndi woipa, ndiponso kuti sanali kuopa Mulungu (Yobu 15)

  • Anaimba mlandu Yobu wakuti anali wadyela ndi wopanda cilungamo, ndipo anakamba kuti munthu ndi wacabecabe kwa Mulungu (Yobu 22)

Bilidadi

Bilidadi:

  • Anali mbadwa ya ku Shuwa. Ayenela kuti anali kukhala pafupi ndi Mtsinje wa Filate

  • Anali waciŵili kukambapo. Katatu konse, iye anakamba mau aafupi koma opweteka mtima kuposa a Elifazi

Zimene anamuneneza:

  • Bilidadi anatanthauza kuti ana a Yobu anacimwa ndipo anafunikadi kulangidwa ndi kufa, ndiponso kuti Yobu iye mwini sanali kuopa Mulungu (Yobu 8)

  • Zokamba zake zinaonetsa kuti Yobu anali kucita zoipa (Yobu 18)

  • Iye anaonetsa kuti kukhulupilika kwa munthu kulibe phindu (Yobu 25)

Zofari

Zofari:

  • Anali wa ku Naama, mwina kumpoto ca kumadzulo kwa Arabiya

  • Anali wacitatu kukambapo ndipo mau ake anali opweteka mtima kuposa a anzake. Iye anakambapo kaŵili cabe

Zimene anamuneneza

  • Anaimba mlandu Yobu wokamba zinthu zopanda pake, ndipo anamuuza kuti aleke kucita zinthu zoipa (Yobu 11)

  • Iye anatanthauza kuti Yobu anali woipa ndipo anacita chimo (Yobu 20)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani