CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 34-37
Khulupililani Yehova ndi Kucita Zabwino
“Usapse mtima [ndi] . . . anthu ocita zosalungama”
37:1, 2
Musaleke kutumikila Yehova cifukwa coona kuti anthu oipa zinthu zikuwayendela bwino. Ikani maganizo anu pa madalitso ndi zolinga za kuuzimu
“Khulupilila Yehova ndipo cita zabwino”
37:3
Khulupililani Yehova kuti adzakuthandizani mukakhala ndi nkhawa. Adzakuthandizani kukhalabe wokhulupilika
Khalani wotangwanika mwa kuuzako ena za Ufumu wa Mulungu
“Sangalala mwa Yehova”
37:4
Pezani nthawi yoŵelenga ndi kusinkhasinkha Mau a Mulungu kuti mum’dziŵe bwino Yehova
“Lola kuti Yehova akutsogolele panjila yako”
37:5, 6
Khulupililani kwambili Yehova kuti adzakuthandizani kuthetsa vuto lililonse
Pitilizani kukhala ndi khalidwe labwino pamene mutsutsidwa kapena kuzunzidwa
“Khala cete pamaso pa Yehova, ndipo umuyembekezele ndi mtima wako wonse”
37:7-9
Pewani kucita zinthu mopupuluma, zimene zingakuonongeleni cimwemwe ndi citetezo canu cauzimu
“Anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi”
37:10, 11
Khalani ofatsa, ndipo yembekezelani Yehova kuti acotsepo mavuto onse amene mukumana nao
Muzithandiza Akristu anzanu ndi kutonthoza amene akuvutika maganizo, mwa kuwauza lonjezo la Mulungu la dziko latsopano, limene lili pafupi kwambili
Ufumu wa Mesiya udzabweletsa madalitso osaneneka