CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 106-109
“Yamikani Yehova”
N’cifukwa ciani Aisiraeli anaiŵala mwamsanga zimene Yehova anacita powapulumutsa?
106:7, 13, 14
Analeka kuika maganizo awo pa Yehova ndipo anayamba kuganizila kwambili zofuna zawo
N’ciani cingakuthandizeni kukhalabe ndi mtima woyamikila?
106:1-5
Muziganizila zinthu zosiyanasiyana zimene Mulungu wakucitilani
Muziganizila kwambili za ciyembekezo canu
Muzipeleka pemphelo loyamikila kwa Yehova, ndipo muzichula mwacindunji zimene wakucitilani