LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 August tsa. 8
  • Kampeni Yapadela Yogaŵila Nsanja ya Mlonda mu September

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kampeni Yapadela Yogaŵila Nsanja ya Mlonda mu September
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Mulungu Amatitonthozela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Kulimbikitsa Amene Anacitilidwapo Zolaula
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Mau Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Itanilani Aliyense m’Gawo Lanu ku Cikumbutso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 August tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Kampeni Yapadela Yogaŵila Nsanja ya Mlonda mu September

Nsanja ya Mlonda Na. 5 2016 | Kodi Tingapeze Kuti Citonthozo?

Anthu padziko lapansi afunika kutonthozedwa. (Mlal. 4:1) M’mwezi wonse wa September, tiyesetse kugaŵila magazini yapadela ya Nsanja ya Mlonda, imene ikamba za citonthozo. Tiyeni tonse tigaŵile magazini imeneyi kwa anthu ambili. Popeza tifuna kukamba ndi anthu mwacindunji n’colinga cakuti tiwalimbikitse, sitiyenela kusiya magaziniyi pa nyumba imene sitinapezepo anthu.

ZIMENE MUNGAKAMBE

“Aliyense amafuna citonthozo nthawi zina. Kodi n’kuti kumene tingacipeze? [Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.] Magazini iyi ya Nsanja ya Mlonda ifotokoza mmene Mulungu amatitonthozela.”

Ngati munthu wacita cidwi ndi kulandila magazini, . . .

MUONETSENI VIDIYO YAKUTI N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KUPHUNZILA BAIBULO?

Ndiyeno m’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo.

YALANI MAZIKO A ULENDO WOBWELELAKO

Siyani funso limene mudzayankha pa ulendo wobwelelako monga lakuti, “N’cifukwa ciani Mulungu amalolela kuti anthu azivutika?”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani