CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOWELI 1-3
“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenela”
2:28, 29
Akhristu odzozedwa amatengako mbali m’nchito yolosela. Iwo amakamba za “zinthu zazikulu za Mulungu” na kulengeza “uthenga wabwino . . . wa Ufumu.” (Mac. 2:11, 17-21; Mat. 24:14) A nkhosa zina amawacilikiza pa nchitoyi.
2:32
Kodi ‘kuitanila pa dzina la Yehova’ kumatanthauza ciani?
Kulidziŵa dzinalo
Kulilemekeza dzinalo
Kudalila na kukhulupilila Mwini wake wa dzinalo
Dzifunseni kuti: ‘Ningawacilikize bwanji odzozedwa pa nchito yawo yolosela?’