CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 8-9
Yesu Anali Kukonda Anthu
Macaputa 8 na 9 a Mateyu amakamba za utumiki wa Yesu m’cigawo ca Galileya. Pamene Yesu anacilitsa anthu, anaonetsa mphamvu zake, koma koposa zonse anaonetsa cikondi cake na cifundo cake kwa anthu.
Yesu anacilitsa munthu wakhate.—Mat. 8:1-3
Yesu anacilitsa kapolo wa kapitawo wa asilikali.—Mat. 8:5-13
Anacilitsa apongozi a Petulo.—Mat. 8:14, 15
Anatulutsa viŵanda na kucilitsa anthu osamvela bwino m’thupi.—Mat. 8:16, 17
Yesu anatulutsa viŵanda voopsa n’kuvitumiza m’cigulu ca nkhumba.—Mat. 8:28-32
Yesu anacilitsa munthu wakufa ziwalo.—Mat. 9:1-8
Anacilitsa mkazi amene anagwila covala cake, ndipo anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo.—Mat. 9:18-26
Anacilitsa munthu wosapenya na wosakamba.—Mat. 9:27-34
Yesu anali kupita m’mizinda na m’midzi, kucilitsa matenda a mtundu uliwonse na zofooka zilizonse.—Mat. 9:35, 36
Ningacite ciani kuti nizionetsa kwambili cikondi na cifundo kwa anthu amene nimakhala nawo?