Ngakhale kuti Pasika siinali kucitila cithunzi Cikumbutso, zinthu zina za pa Pasika zili na tanthauzo kwa ise. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anachula Yesu kuti “nsembe yathu ya Pasika.” (1 Akor. 5:7) Monga mmene magazi a nkhosa amene anawazidwa pa zitseko anapulumutsila miyoyo, nawonso magazi a Yesu amapulumutsa miyoyo. (Eks. 12:12, 13) Cina, panalibe fupa la nkhosa ya pa Pasika imene inathyoledwa. Mofananamo, palibe ngakhale fupa limodzi la Yesu limene linathyoledwa, olo kuti panthawiyo unali mwambo kuthyola mafupa a munthu amene wapacikiwa.—Eks. 12:46; Yoh. 19:31-33, 36.