UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi . . . ”
Cilamulo ca Mose cinali kufuna kuti mwamuna amene anali kuganizila zosudzula mkazi wake azilemba kalata yacilekanilo yovomelezeka mwalamulo. Izi zinali kuthandiza kuti anthu asamasudzulane mwacisawawa. Komabe, atsogoleli a cipembedzo a m’nthawi ya Yesu anali kulola anthu kusudzulana mwacisawawa. Amuna anali kusudzula akazi awo pa cifukwa ciliconse. (nwtsty mfundo zounikila pa Maliko 10:4, 11) Yesu anakumbutsa anthu mfundo yakuti Yehova ndiye anayambitsa cikwati. (Maliko 10:2-12) Mwamuna na mkazi afunika kukhala “thupi limodzi” kwa moyo wawo wonse. Pa nkhani imeneyi, Mateyu analemba kuti cifukwa cimodzi cokha ca m’Malemba cothetsela cikwati ni “cigololo.”—Mat. 19:9.
Masiku ano, anthu ambili saona cikwati mmene Yesu anali kucionela. Amacipeputsa monga Afarisi. Anthu a m’dzikoli akakumana na mavuto m’banja, amathamangila kuthetsa cikwati. Koma Akhristu okwatilana amalemekeza kwambili malumbilo awo a cikwati, ndipo amayesetsa kuthetsa mavuto mwa kutsatila mfundo za m’Baibo. Pambuyo potamba vidiyo yakuti; Cikondi na Ulemu Zimagwilizanitsa Banja, yankhani mafunso aya:
Kodi mungaseŵenzetse bwanji mfundo ya pa Miyambo 15:1 m’cikwati canu? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezo n’kofunika?
Kodi kuseŵenzetsa mfundo ya pa Miyambo 19:11 kungakuthandizeni bwanji kupewa mavuto?
Ngati cikwati canu cili pa mavuto aakulu, m’malo moganiza kuti, ‘Tingosudzulana cabe,’ mungadzifunse mafunso abwanji?
Kodi kuseŵenzetsa mfundo ya pa Mateyu 7:12 kungakuthandizeni bwanji kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino?