UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mwana Woloŵelela
TAMBANI VIDIYO YAKUTI MWANA WOLOWELELA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
N’ciani cinaonetsa kuti David wayamba kupatuka pa njila ya coonadi? Nanga a m’banja mwake na akulu anayesa kumuthandiza bwanji?
Kodi M’bale na Mlongo Barker, monga makolo, anali citsanzo cabwino motani?
Kodi vidiyoyi yatiphunizitsa ciani ponena za . . .
kudzipeleka pa nchito zakuthupi?
mayanjano oipa?
kumvela uphungu?
kulapa na kukhululuka?