CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 19-20
“Mukhale Chelu ndi Kuyang’anila Gulu Lonse la Nkhosa”
20:28, 31, 35
Akulu amadyetsa nkhosa, kuziteteza na kuzisamalila. Amakumbukila kuti nkhosa iliyonse inagulidwa na magazi a mtengo wapatali a Khristu. Abale na alongo amakonda na kuyamikila akulu amene amadzipeleka mofunitsitsa kuti asamalile nkhosa, monga mmene Paulo anacitila.