CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 9-11
Fanizo la Mtengo wa Maolivi
Kodi mbali zosiyana-siyana za mtengo wophiphilitsa wa maolivi ziimila ciani?
Mtengo: kukwanilitsidwa kwa colinga ca Mulungu cokhudza cipangano ca Abulahamu
Thunthu: Yesu, mbali yaikulu ya mbewu ya Abulahamu
Nthambi: a 144,000 amene apanga mbali yaciŵili ya mbewu ya Abulahamu
Nthambi ‘zodulidwa’: Ayuda amene anakana Yesu
Nthambi ‘zolumikizidwa’: Akhristu odzozedwa na mzimu ocokela m’mitundu yonse
Monga mwa ulosi, mbewu ya Abulahamu, kutanthauza Yesu na a 144,000, adzabweletsa madalitso kwa “anthu a mitundu.”—Aroma 11:12; Gen. 22:18
Niphunzilapo ciani pa mmene Yehova anakwanilitsila colinga cake cokhudza mbewu ya Abulahamu?