CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AKOLOSE 1-4
Vulani Umunthu Wakale, Muvale Watsopano
3:5-14
Kodi munasintha kwambili umunthu wanu mutabwela m’coonadi? Mosakayikila Yehova anakondwela cifukwa ca kuyesetsa kwanu kuti musinthe. (Ezek. 33:11) Komabe, kulimbikila n’kofunika kuti munthu asabwelelenso ku makhalidwe akale, na kuti apitilize kuvala umunthu watsopano. Yankhani mafunso otsatilawa kuti muone mbali zimene mungafunike kuwongolela:
Kodi pali amene n’nasungila cakukhosi cifukwa conilakwila?
Kodi nimakhalabe woleza mtima ngakhale pamene nili wofulumila kapena wolema?
Kodi malingalilo osayenela akabwela m’maganizo mwanga nimayacotsa mwamsanga?
Kodi nimaipidwa nawo anthu a mtundu wina kapena ocoka ku maiko ena?
Kodi posacedwa n’nazazilapo munthu aliyense kapena kumukwiyila?