CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 12-14
Cipangano Cimene Cimakukhudzani
12:1-3; 13:14-17
Yehova anacita cipangano na Abulahamu, cimene cinakhala maziko a Ufumu wa kumwamba
Cipangano cimeneco ciyenela kuti cinayamba kugwila nchito mu 1943 B.C.E. pamene Abulahamu anawoloka Mtsinje wa Firate ali pa ulendo wopita ku Kanani
Cipanganoco cidzagwilabe nchito mpaka pamene Ufumu wa Mesiya udzawononga adani a Mulungu na kubweletsa madalitso ku mabanja onse pa dziko lapansi
Yehova anadalitsa Abulahamu cifukwa ca cikhulupililo cacikulu. Ngati tikhulupilila malonjezo a Yehova, kodi tidzalandila madalitso otani cifukwa ca cipangano ca Abulahamu?