LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 February tsa. 3
  • Kodi Mungaphunzile Ciani mu Nyimbo Zopekedwa Koyamba?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mungaphunzile Ciani mu Nyimbo Zopekedwa Koyamba?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Nyimbo Zimene Zimatiyandikizitsa kwa Mulungu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Muziimba Mosangalala Nyimbo Zotamanda Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 February tsa. 3
Abale na alongo akuimba nyimbo panja na gitala.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mungaphunzile Ciani mu Nyimbo Zopekedwa Koyamba?

Kodi mumakonda nyimbo ziti zopekedwa koyamba? Cifukwa? Kodi mumaona kuti zosonyezedwa m’mavidiyo ake n’zothandizadi pa umoyo wa tsiku na tsiku? Pa nkhani zosiyana-siyana za m’nyimbozo, ndiponso maimbidwe ake osiyana-siyana, aliyense amapezapo ya pamtima. Koma colinga cake si kungotisangalatsa cabe ayi.

Nyimbo yopekedwa koyamba iliyonse imatiphunzitsa mfundo zofunikila zimene tingaseŵenzetse mu umoyo na utumiki wathu wacikhristu. Nyimbo zina zimakamba pa kuceleza, mgwilizano, ubwenzi, kulimba mtima, cikondi, komanso cikhulupililo. Zina zimatilimbikitsa kubwelela kwa Yehova, kukhululuka, kusunga umphumphu nthawi zonse, ndiponso kukhala na zolinga zauzimu. Kulinso nyimbo ina yopekedwa koyamba yokamba za kuseŵenzetsa bwino mafoni. Ni mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza mu nyimbo zopekedwa koyamba?

TAMBITSANI VIDIYO YA NYIMBO YOPEKEDWA KOYAMBA YAKUTI DZIKO LATSOPANO ILI PAFUPI KWAMBILI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni madalitso ati akutsogolo amene banja lacikulile likuganizila?—Gen. 12:3

  • Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu cakuti Yehova angathe kukwanilitsa malonjezo ake?

  • Kodi tidzakondwela kuonananso na ndani m’dziko latsopano limene layandikila?

  • Kodi kuyembekezela Ufumu kumatithandiza bwanji kupilila mavuto amene timakumana nawo?—Aroma 8:25

ZIMENE MUNGACITE PA KULAMBILA KWA PABANJA

Tambani mavidiyo otsatilawa a nyimbo zopekedwa koyamba, ndiyeno yankhani mafunso yaŵili aya: Kodi ni mfundo ziti zothandiza zimene vidiyoyi ikuphunzitsa? Kodi mfundozi ningaziseŵenzetse bwanji mu umoyo wanga?

  • Musayope

  • Tizikhululukilana

  • Tikhale Oceleza Alendo

  • Tithamange, Tisatsalile

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani