LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 March tsa. 8
  • Kodi Nidzaitanila Ndani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Nidzaitanila Ndani?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Yehova Amadalitsa Kuyesetsa Kwathu Kuti Ticite Cikumbutso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Nchito Yogaŵila Tumapepala Toitanila Anthu ku Msonkhano Wacigawo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kodi Mwalikonzekela Tsiku Lofunika Kwambili M’caka?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 March tsa. 8
Pamene akuceza m’khichin, m’bale akupatsa wacibululu amene si Mboni kapepa koitanila anthu ku Cikumbutso. Ndipo cakumbuyo kwawo azikazi awo akuceza pokonza cakudya.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Nidzaitanila Ndani?

Caka ciliconse timayesetsa kuitanila anthu a m’gawo lathu kuti akacite nafe Cikumbutso. Ambili a iwo ni anthu amene sitiŵadziŵa. Tiyenelanso kuitanila anthu amene timaŵadziŵa. Anthu amene amalandila ciitano kucokela kwa anthu amene amaŵadziŵa, kambili amapezeka ku cikumbutso. (yb08 11 ¶3; 14 ¶1) Ni anthu ena ati amene mungaitanile?

  • Acibululu

  • Anzanu a kunchito kapena a kusukulu

  • Maneba

  • Anthu amene munapangako maulendo obwelelako na maphunzilo a Baibo akale komanso atsopano

Kuwonjezela apo, akulu adzaitanila anthu ozilala. Nanga bwanji ngati munthu amene mudziŵana naye sakhala m’dela lanu? Mungafufuze nthawi na malo kumene Cikumbutso cidzacitikila kumene munthuyo akhala, mwa kutinika pa mbali yakuti ZOKHUDZA IFE imene ili pamwamba pa peji yoyamba pa jw.org. Kenako sankhani polemba kuti ““Cikumbutso.” Pokonzekela cikumbutso ca caka cino, ganizilani anthu amene mungaitanile, ndipo mukawapatsedi ciitanilo.

Zithunzi: 1. M’bale alalikila munthu wina pa nthawi yopuma ku nchito. 2. M’bale akutambitsa vidiyo munthu woseŵenza m’lesitilanti.
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani