CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 6–7
“Tsopano Uona Zimene Ndicite kwa Farao”
6:1, 6, 7; 7:4, 5
Akalibe kubweletsa milili pa Aiguputo komanso kulanditsa Aisiraeli ku ukapolo, Yehova anali kuŵauzilatu Aisiraeli zimene anali kufuna kucita. Iwo anali kudzaona mphamvu za Yehova m’njila imene sanazionepo. Komanso Aiguputo anali kudzadziŵa kuti Yehova ndani. Pamene malonjezo a Mulungu anakwanilitsidwa, cikhulupililo ca Aisiraeli cinalimba, ndipo izi zinawathandiza kupewa cisonkhezelo ca cipembedzo conama cimene cinali cofala mu Iguputo.
Kodi nkhaniyi ya m’Baibo imalimbitsa bwanji cikhulupililo canu cakuti malonjezo a Mulungu a kutsogolo adzakwanilitsidwa?