CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 15-16
Tamandani Yehova mwa Kuimba Nyimbo
15:1, 2, 11, 18, 20, 21
Nyimbo zimakhudza kwambili maganizo athu na mmene timamvelela mumtima. Ndipo kuimba nyimbo ni mbali yofunika kwambili pa kulambila kwathu Yehova.
Mose na Aisiraeli anaimbila zitamando Yehova cifukwa cakuti anawapulumutsa mozizwitsa pa Nyanja Yofiila
Mfumu Davide anaika amuna 4,000 kuti azicita utumiki woimba nyimbo pa kacisi
Usiku wakuti aphedwa maŵa, Yesu pamodzi na atumwi ake okhulupilika anaimba nyimbo zotamanda Yehova
Kodi ni mipata iti imene ningamaiseŵenzetse poimba nyimbo zotamanda Yehova?