CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EKSODO 29–30
Kupatsa Yehova Copeleka
30:11-16
Pamene cihema cinapangidwa, munthu aliyense anali na mwayi wopeleka ndalama kuti acilikize kulambila Yehova, mosasamala kanthu kuti anali wolemela kapena wosauka. Kodi tingacite bwanji copeleka kwa Yehova masiku ano? Njila imodzi ni mwa kupeleka ndalama zocilikiza Nyumba za Ufumu, Mabwalo a Misonkhano, ma Ofesi Omasulila Mabuku, komanso malo a Beteli, kuphatikizapo zimango zina zimene zimagwilitsidwa nchito polambila Yehova.
Tiphunzilapo ciani pa malemba otsatilawa pa nkhani yocita copeleka cocilikiza kulambila koona?
1 Mbiri 29:5