UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mungapeleke Nthawi na Mphamvu Zanu?
Monga mmene Yesaya analosela, gawo la gulu la Yehova la padziko lapansi likukula kuposa na kale lonse. (Yes. 54:2) Conco, pakufunika kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano, Mabwalo a Misonkhano, komanso ma Ofesi a Nthambi. Pambuyo pakuti zamangidwa, zimango zimenezi zimafunika kuzisamalila, ndipo m’kupita kwa nthawi zina zimafunika kukonzedwanso. Zimenezi zimatipatsa mwayi wopeleka nthawi na mphamvu zathu kwa Yehova. Motani?
Tingacite zimenezi mwa kutengako mbali yoyeletsa pa Nyumba ya Ufumu pamene kagulu kathu ka ulaliki kakuyeletsa
Tingadzipeleke kuti ticiteko maphunzilo a mmene tingasamalile Nyumba ya Ufumu
Tingadzaze fomu ya Local Design/Construction Volunteer (DC-50) kuti tizithandizilako mwa apo ndi apo pa nchito yomanga na kusamalila zimango zili kufupi na kumene tikhala
Tingadzaze fomu yochedwa Application for Volunteer Program (A-19) na kudzipeleka kuti tizithandizila kwa wiki imodzi kapena kuposelapo m’gawo la Nthambi yathu kapena ku Nthambi ina
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KUKONZEKELA KUMANGA CIMANGO CATSOPANO—KAMBALI KAKE NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi pakhala cionjezeko cotani pankhani yoseŵenzetsa mavidiyo kungoyambila mu 2014?
Kuti tipitilizebe kukhala na mavidiyo pa kulambila kwathu, kodi pakulinganizidwa yanji, ndipo nchitoyo idzatenga utali wotani?
Nanga anchito odzipeleka angacilikize bwanji nchitoyo?
Ngati tifuna kuthandizako nchito yomanga ya ku Ramapo, n’cifukwa ciani tifunika kusaina fomu ya DC-50 komanso kuthandizila m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga (LDC) ya kwanuko?
Kodi pali umboni wotani woonetsa kuti Yehova akutsogolela nchito imeneyi?
Kodi tingacilikize bwanji nchito imeneyi olo kuti sitingakwanitse kupita kukamanga nawo?