LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 October tsa. 6
  • Anapatsidwa Nzelu Kuti Agwile Nchito ya Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anapatsidwa Nzelu Kuti Agwile Nchito ya Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amaona Nchito Yanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mmene Mzimu Woyela Umatithandizila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 October tsa. 6
Bezaleli ndi Oholiabu akupanga zinthu zagolide za pa cihema. Mwamuna mmodzi akupanga phiko la mkelubi mwaluso, ndipo wina akukonza lata lagolide.

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 35–36

Anapatsidwa Nzelu Kuti Agwile Nchito ya Yehova

35:25, 26, 30-35; 36:1, 2

Mzimu woyela wa Yehova unathandiza Bezaleli na Oholiabu kutsatila mosamala malangizo onse omangila cihema amene Mulungu anapeleka. Mzimu woyela wamphamvu wa Yehova umathandizanso atumiki ake lelolino. Kodi tingacite ciani kuti tilandile thandizo la mzimu woyela?

  • Tifunika kupempha mzimu woyela kuti uwonjezele luso limene tili nalo potumikila Yehova

  • Tifunika kumaŵelenga mwakhama Mawu a Mulungu ouzilidwa

  • Tifunika kucita na mtima wonse utumiki uliwonse umene tapatsidwa

Zithunzi: Mboni za Yehova zikucita zinthu zosiyana-siyana m’gulu la Mulungu. 2. M’bale akukonzekela kukatsogoza Phunzilo la ‘Nsanja ya Mlonda.’ 3. M’bale akulalikila munthu wogulitsa m’shopu pamene m’bale mnzake akuyang’ana ngati kubwela anthu otsutsa. 4. Mwamuna na mkazi wake akucita Sukulu ya Alengezi a Ufumu.

Kodi Yehova angakupatseni mphamvu na nzelu kuti mukwanitse kucita utumiki uti?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani