LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsa. 7
  • Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Cilango Ni Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Mmene Mungalangile Ana Anu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • “Mvelani Malangizo Kuti Mukhale Anzelu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Cilango—Umboni Wakuti Yehova Amatikonda
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 May tsa. 7
Makolo aimilila pakhomo ndipo akulila pamene aona mwana wawo wosalapa akucoka panyumba.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova

Cilango nthawi zambili cimatanthauza kupeleka malangizo na kuphunzitsa. Koma cingaphatikizeponso uphungu na cibalo kapena kuti mkwapulo. Yehova amatilanga n’colinga cakuti tizimulambila m’njila yovomelezeka. (Aroma 12:1; Aheb. 12:10, 11) Nthawi zina cilango cimakhala cowawa, koma cimabala cilungamo na kubweletsa madalitso. (Miy. 10:7) Kodi wopeleka cilango na wocilandila ayenela kukumbukila ciani?

Wopeleka cilango. Akulu, makolo, na ena amayesetsa kupeleka cilango mokoma mtima komanso mwacikondi monga mmene Yehova amacitila. (Yer. 46:28) Ngakhale uphungu wamphamvu uyenela kupelekedwa mogwilizana na mmene mikhalidwe ilili, ndiponso mosonkhezeledwa na cikondi.—Tito 1:13.

Wolandila cilango. Kaya cilango capelekedwa motani, sitiyenela kucikana koma tiyenela kugwililapo nchito mwamsanga. (Miy. 3:11, 12) Monga anthu opanda ungwilo tonsefe timafunikila cilango. Cilango cimabwela m’njila zosiyana-siyana. Tingacilandile kupitila m’zimene timaŵelenga m’Baibo kapena zimene timamvetsela pa misonkhano ya mpingo. Nthawi zina ena amafunikila cilango ca komiti ya ciweluzo. Ngati tilandila cilango na kucitapo kanthu, tidzakhala na umoyo wabwino komanso tidzapeza moyo wosatha.—Miy. 10:17.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI “YEHOVA AMALANGA ALIYENSE AMENE IYE AMAMUKONDA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.’ Ali mwana, Canon akulalikila pamodzi na makolo ake.

    Kodi umoyo wa m’bale Canon unali bwanji poyamba? Nanga unasintha bwanji?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.’ Ali wacinyamata, Canon akuonana na akulu.

    Ni cilango cotani cacikondi cimene analandila kucokela kwa Yehova?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.’ Patapita zaka, Canon akukambilana na acicepele pa msonkhano wa mpingo.

    Phunzilani kukonda cilango ca Yehova

    Taphunzilapo ciani pa citsanzo cake?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani