LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsa. 16
  • Muzipanga Zosankha Mwanzelu pa Nkhani ya Moŵa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzipanga Zosankha Mwanzelu pa Nkhani ya Moŵa
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Nkhani ya Kumwa Moŵa Akhristu Ayenela Kuiona Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Yendelani Malangizo a Mulungu pa Nkhani ya Moŵa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 May tsa. 16

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Muzipanga Zosankha Mwanzelu pa Nkhani ya Moŵa

Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Ganizilani Zotulukapo za Kumwa Moŵa.’ Cinjoka ca mano aatali catuluka m’botolo la moŵa limene munthu wanyamula.

Akhristu onse ayenela kudziletsa pankhani ya kumwa zakumwa zoledzeletsa. (Miy. 23:20, 29-35; 1 Akor. 6:9, 10) Ngati Mkhristu wasankha kumwako moŵa, ayenela kucita zimenezo mwacikatikati. Ayenelanso kupewa kudalila moŵa pocita zinthu. Komanso, ayenela kupewa kukhumudwitsa ena. (1 Akor. 10:23, 24; 1 Tim. 5:23) Conco, tiyenela kupewa kukakamiza aliyense kumwa moŵa, maka-maka acinyamata.

ONETSANI VIDIYO YA ZITHUNZI ZOJAMBULA PAMANJA YAKUTI GANIZILANI ZOTULUKAPO ZA KUMWA MOŴA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’cifukwa ciani Akhristu onse ayenela kutsatila malamulo a boma okhudza kumwa moŵa?—Aroma 13:1-4

  • N’cifukwa ciani sitiyenela kulola ena kutikakamiza kumwa moŵa?—Aroma 6:16

  • Pankhani ya moŵa, kodi mungapewe bwanji zocitika zimene zingakugwetseleni m’mavuto?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani