LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 September tsa. 5
  • Pitilizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pitilizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikila
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Khalani ndi Cikhulupililo Ndipo Muzipanga Zosankha Mwanzelu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Pangani Zosankha Zanu Mwanzelu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 September tsa. 5

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pitilizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikila

Munthu wocita maseŵela amafunika kupitiliza kucita zinthu zolimbitsa thupi lake kuti akhalebe waluso. Nafenso, tiyenela kupitiliza kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikila. (Aheb. 5:14) Mwina tili na cizoloŵezi cotengela zisankho za ena. Koma tiyenela kukulitsa luntha lathu la kuganiza na kudzipangila tokha zisankho. Cifukwa ciani? Cifukwa aliyense wa ife adzadziyankhila yekha pa zisankho zimene amapanga.—Aroma 14:12.

Tisaganize kuti tizipanga zisankho zabwino, cabe cifukwa cakuti takhala m’coonadi zaka zambili. Kuti tipange zisankho zabwino, tiyenela kudalila Yehova na mtima wonse, Mawu ake, na gulu lake.—Yos. 1:7, 8; Miy. 3:5, 6; Mat. 24:45.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI “KHALANI NDI CIKUMBUMTIMA CABWINO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Khalani Ndi Cikumbumtima Cabwino.” Mlongo Emma na mwamuna wake akuyang’ana ciitanilo ca ku cikwati.

    Kodi mlongo Emma anafunika kupanga cisankho cotani?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Khalani Ndi Cikumbumtima Cabwino.” Mlongo Amy akufotokoza maganizo ake mwamphamvu.

    N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kukambapo maganizo athu pa nkhani zodalila cikumbumtima?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Khalani Ndi Cikumbumtima Cabwino.” Mlongo Emma akufunsila malangizo kwa mlongo Charlotte na m’bale Allan.

    Ni malangizo anzelu ati amene banja lina linapatsa mlongo Emma?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Khalani Ndi Cikumbumtima Cabwino.” Mlongo Emma akufufuza pa “LAIBULALE YA PA INTANETI™ ya Watchtower” pa kompyuta yake.

    N’kuti kumene mlongo Emma anapeza mfundo zothandiza pa vuto lake?

Kodi niyenela kudalila ciani popanga zisankho?

  • Maganizo anga

  • Maganizo a anthu ena

  • Mfundo za m’Baibo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani