CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mumaugwila Mtima?
Pempho la Davide linali loyenela, koma Nabala anam’nyoza Davide pamodzi na asilikali ake (1 Sam. 25:7-11; ia 78 ¶10-12)
Davide posaugwila mtima anafuna kupha amuna a m’nyumba ya Nabala (1 Sam. 25:13, 21, 22)
Abigayeli anathandiza Davide kupewa kupalamula mlandu wa magazi (1 Sam. 25:25, 26, 32, 33; ia 80 ¶18)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi nimalephela kudziletsa nikakwiya, nikamagula zinthu, kapena nikalefulidwa? Kapena nimaima na kuganizila zotulukapo zake n’sanacitepo kanthu?’—Miy. 15:28; 22:3.