LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsa. 3
  • Kucita Upainiya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kucita Upainiya
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 July tsa. 3
Mtsikana, makolo ake, na ambuye ake aakazi akukambilana za ndandanda zawo.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU | DZIIKILENI ZOLINGA ZA CAKA CA UTUMIKI CATSOPANO

Kucita Upainiya

Kudziikila zolinga zauzimu kumatithandiza kuseŵenzetsa mphamvu zathu mwanzelu. (1 Akor. 9:26) Zolinga zimatithandiza kuseŵenzetsa mwanzelu nthawi imene yatsala mapeto a dziko loipali asanafike. (Aef. 5:15, 16) Pa kulambila kwa pabanja, bwanji osakambilanako zolinga za banja lanu zimene mungadziikile m’caka ca utumiki catsopano? Pofuna kukuthandizani kucita zimenezi, m’kabuku kano ka misonkhano muli nkhani zofotokoza zolinga zosiyanasiyana zimene mungaziganizile mwapemphelo.—Yak. 1:5.

Mwacitsanzo, kodi mungakambilane monga banja kuti mumasuleko mmodzi wa inu kuti ayambe upainiya wa nthawi zonse? Ngati simuli otsimikiza zakuti mungakwanitse maola ofunikila, kambilanani na apainiya ena amene mikhalidwe yawo ni yofanana na yanu. (Miy. 15:22) Mwinanso mungaitanile mpainiya pa kulambila kwanu kwa pabanja, na kumufunsako mafunso okhudza kucita upainiya. Kenako lembani ndandanda zosiyanasiyana zimene mungakwanitse kuzitsatila. Ngati munacitako upainiya kumbuyoku, onani ngati n’zotheka tsopano kuyambilanso utumikiwu.

Kodi ena m’banja mwanu angaciteko upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo? Ngati mphamvu zanu ni zocepekela, mungakwanitse kucita upainiya wothandiza mwa kuthela nthawi yocepa tsiku lililonse mu ulaliki. Ngati mumakhala na nthawi yocepa yopita mu ulaliki mkati mwa mlungu cifukwa ca nchito kapena sukulu, mungasankhe mwezi umene uli na holide kapena umene uli na masiku asanu a Ciwelu komanso Sondo. Pa kalenda yanu, ikani cizindikilo pa tsiku limene mufuna kudzayamba upainiya wothandiza, ndipo lembani ndandanda yake.—Miy. 21:5.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KHALANI OLIMBA MTIMA . . . INU APAINIYA, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

  • Kodi citsanzo ca mlongo Aamand citiphunzitsa ciyani za mmene Yehova amasamalila mwacikondi anthu amene amadzimana zinthu zina kuti acite upainiya?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani