UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Musakhale na Nkhawa Mukakumana na Mavuto Azacuma
Umoyo masiku otsiliza ano ni wodzala na mavuto. Ndipo n’zodziŵikilatu kuti pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, mavuto aziculukila-culukila. Tingasoŵe zinthu zina zofunika pa umoyo. (Hab. 3:16-18) N’ciyani cingatithandize kuti tisamakhale na nkhawa tikakumana na mavuto azacuma? Sitiyenela kuleka kudalila Mulungu wathu, Yehova. Iye analonjeza kuti adzasamalila atumiki ake, ndipo olo zinthu zivute bwanji, adzatithandiza kupeza zosowa zathu.—Sal. 37:18, 19; Aheb. 13:5, 6.
Zimene mungacite:
Pemphani Yehova kuti akutsogoleleni, akupatseni nzelu, na kukuthandizani.—Sal. 62:8
Khalani okonzeka kugwila nchito imene simunaigwilepo.—g 1/10 8-9, mabokosi
Musaleke cizoloŵezi canu cocita zinthu zauzimu, monga kuŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kupezeka ku misonkhano ya mpingo, na kulalikila
ONELELANI VIDIYO YAKUTI MANGANI NYUMBA IMENE IDZAKHALITSA—‘KHUTILANI NDI ZIMENE MULI NAZO PA NTHAWIYO,’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Kodi mabanja ena akukumana na mavuto otani?
N’ciyani cofunika kwambili pa umoyo?
Kodi amene akukumana na mavuto azacuma tingawathandize bwanji?