LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsa. 9
  • Amagwila Nchito Molimbika Potitumikila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Amagwila Nchito Molimbika Potitumikila
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Muzionetsa kuti Mumayamikila “Mphatso za Amuna”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • “Paulo Anayamika Mulungu Ndipo Analimba Mtima”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kodi Oyang’anila Dela Amatithandiza m’Njila Ziti?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 July tsa. 9
Zithunzi: Woyang’anila wadela akucezela mpingo. 1. Iye akucititsa msonkhano wokonzekela ulaliki. 2. Akumana na bungwe la akulu. 3. Akuyenda mu ulaliki pamodzi na m’bale wacinyamata.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Amagwila Nchito Molimbika Potitumikila

Oyang’anila madela na akazi awo amaonetsa cikondi codzimana kwa abale na alongo amene amawatumikila. Mofanana na ife tonse, nawonso ali na zosoŵa zawo. Ndipo nthawi zina amalema, amalefuka, ndiponso amakhala na nkhawa. (Yak. 5:17) Ngakhale n’conco, mlungu uliwonse iwo amayesetsa kulimbikitsa abale na alongo a mumpingo umene akuucezela. Kukamba zoona, oyang’anila madela “ayenela kupatsidwa ulemu waukulu.”—1 Tim. 5:17.

Pamene mtumwi Paulo anali kukonzekela zopita ku Roma kukagaŵila mpingo wa kumeneko “mphatso inayake yauzimu”, anali kuyembekezela ‘kukalimbikitsana’ na abale na alongo. (Aroma 1:11, 12) Kodi muganiza kuti mungamulimbikitse bwanji woyang’anila dela wanu na mkazi wake, ngati ni wokwatila?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI UMOYO WA OYANG’ANILA DELA AMENE AMATUMIKILA KU MIDZI, KENAKO KAMBILANANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi oyang’anila madela na akazi awo amaonetsa bwanji cikondi codzimana potumikila mipingo?

  • Kodi inu pacanu mwapindula bwanji na khama lawo?

  • Kodi mungawalimbikitse bwanji?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani