LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w20 February masa. 26-30
  • N’napeza Madalitso Ambili Cifukwa Cophunzila kwa Ofalitsa Acitsanzo Cabwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’napeza Madalitso Ambili Cifukwa Cophunzila kwa Ofalitsa Acitsanzo Cabwino
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MMENE N’NAYAMBILA KUKONDA ULALIKI
  • TINABWELELA KU QUEBEC KUKATUMIKILA MONGA APAINIYA APADELA
  • KUITANIDWA KUKATUMIKILA MONGA WOYANG’ANILA WOYENDELA
  • CAKA COSAIŴALIKA
  • KUSAMUKILA KU GAWO LINA
  • Kuonetsa Ena Cidwi Kumabweletsa Madalitso Okhalitsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kupatsidwa Ufulu Wolalikila ku Quebec
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • N’natsimikiza Mtima Kuti Sinidzabwelela M’mbuyo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Nakhala na Umoyo Wosangalatsa Potumikila Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
w20 February masa. 26-30

MBILI YANGA

N’napeza Madalitso Ambili Cifukwa Cophunzila kwa Ofalitsa Acitsanzo Cabwino

WOSIMBA NI: LÉONCE CRÉPEAULT

M’bale Léonce Crépeault ali wacinyamata.

PAMENE n’nali wacicepele, n’nali kuyopa kulalikila. Koma n’takula, n’nayamba kupatsidwa mautumiki amene poyamba n’nali kuona kuti siningawakwanitse. Lekani nikuuzenkoni za anthu acitsanzo cabwino amene ananithandiza kuthetsa mantha. Cifukwa ca thandizo lawo, napeza madalitso ambili pa zaka 58 zimene nakhala mu utumiki wanthawi zonse.

N’nabadwila mu mzinda wa Quebec, m’cigawo ca Quebec ku Canada. Anthu ambili m’cigawoci amakamba Cifulenchi. Makolo anga a Louis ndi a Zélia anali kunisamalila mwacikondi. Atate anali munthu wamanyazi, koma anali kukonda kuŵelenga. Ine n’nali kukonda kwambili kulemba, ndipo n’nali kulaka-laka kudzakhala mtolankhani.

Nili na zaka pafupi-fupi 12, a Rodolphe Soucy, mmodzi wa anthu amene anali kuseŵenza pamodzi na atate, anabwela ku nyumba kwathu na mnzawo. Iwo na mnzawoyo anali Mboni za Yehova. Sin’nali kuwadziŵa bwino a Mboni ndiponso n’nalibe cidwi na cipembedzo cawo. Koma n’nacita cidwi na mmene anali kuyankhila mafunso mokoma mtima komanso mwaluso poseŵenzetsa Baibo. Makolo anga naonso anacita cidwi. Conco, tinayamba kuphunzila Baibo.

Pa nthawiyo, n’nali kuphunzila pa sukulu ya Akatolika. Nthawi na nthawi, n’nali kuuzako anzanga a m’kilasi zimene n’nali kuphunzila m’Baibo. M’kupita kwa nthawi, matica amenenso anali ansembe anadziŵa zimenezi. M’malo moti aseŵenzetse Malemba potsutsa zimene n’nali kukamba, mmodzi wa iwo ananinena pamaso pa anzanga onse m’kilasi kuti ndine wopanduka. Zimene zinacitikazo zinali zokhumudwitsa, koma zinanithandiza kuona kuti mfundo zacipembedzo zimene anali kuphunzitsa pa sukulupo zinali zosagwilizana na Baibo. Apa, n’nazindikila kuti nifunika kucoka pa sukulu imeneyi. N’tapempha cilolezo kwa makolo, n’nayamba kuphunzila pa sukulu ina.

MMENE N’NAYAMBILA KUKONDA ULALIKI

N’napitiliza kuphunzila Baibo, koma sin’napite patsogolo mwamsanga cifukwa n’nali kuyopa kulalikila ku nyumba na nyumba. Chechi ya Akatolika inali yamphamvu kwambili, ndipo inali kutsutsa ngako nchito yathu yolalikila. Mtsogoleli wandale ku Quebec, dzina lake Maurice Duplessis, anali kugwilizana kwambili na chechi ya Akatolika. Iye anali kutuntha magulu aciwawa kuti azivutitsa Mboni, ngakhale kuzimenya kumene. Panthawiyo, kuti munthu alalikile anafunika kukhala wolimba mtima kwambili.

M’bale John Rae ndiye ananithandiza kucotsa mantha. Iye analoŵa Sukulu ya Giliyadi ya namba 9. Anali munthu wodziŵa zambili, wofatsa, wodzicepetsa, ndiponso wofikilika. Sanali kunipatsa uphungu wacindunji kaŵili-kaŵili, koma n’naphunzila zambili mwa kutengela citsanzo cake cabwino. M’bale Rae anali kuvutika kukamba Cifulenchi. Conco, n’nali kuyenda naye mu ulaliki kuti nizimuthandiza kukamba citundu cimeneci. Kucitila zinthu pamodzi na m’bale Rae kunanithandiza kuti nilimbe mtima mpaka kupanga cosankha cokhala Mboni. Pa May 26, 1951 n’nabatizika, ndipo panali patapita zaka 10 kucokela pamene n’nakumana na Mboni.

M’bale Léonce Crépeault na m’bale John Rae ali na anzawo.

Citsanzo cabwino ca m’bale John Rae (A) cinanithandiza ine (B) kuti nisamaope kulalikila ku nyumba na nyumba

Mpingo wathu mu mzinda wa Quebec unali waung’ono, koma ofalitsa ambili anali apainiya. Cangu cawo pa nchito yolalikila cinanilimbikitsa kuyamba upainiya. Panthawiyo, tinali kuseŵenzetsa cabe Baibo polalikila ku nyumba na nyumba. Popeza sitinali kuseŵenzetsa zofalitsa mu ulaliki, tinafunika kuphunzila mmene tingagwilitsile nchito Baibo mogwila mtima. Conco, n’nayesetsa kudziŵa bwino mavesi a m’Baibo amene akananithandiza kukhalila kumbuyo coonadi. Olo zinali telo, anthu ambili anali kukana kuŵelenga Baibo ina iliyonse yosavomelezedwa na Chechi ya Akatolika.

Mu 1952, n’nakwatila Simone Patry, mlongo wokhulupilika wa mu mpingo mwathu. Tinakukila ku mzinda wa Montreal, ndipo pasanathe caka tinakhala na mwana wamkazi dzina lake Lise. Olo kuti nili pafupi kukwatila n’nasiya upainiya, ine na mkazi wanga Simone tinayesetsa kukhala na umoyo wosalila zambili, n’colinga cakuti tonse monga banja tizitengako mbali mokwanila pa zinthu zauzimu mu mpingo.

Patapita zaka 10, n’nayamba kuganizila kwambili za kuyambanso upainiya. Mu 1962, n’nangena Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya akulu ya mwezi umodzi. Sukuluyi inacitikila pa Beteli ku Canada, ndipo n’nali kukhala m’cipinda cimodzi na m’bale Camille Ouellette. N’nacita cidwi kwambili na cangu ca m’bale Camille pa nchito yolalikila, maka-maka cifukwa cakuti anali na colinga coyamba upainiya ngakhale kuti anali na mkazi komanso ana. Pa nthawiyo, panali abale na alongo ocepa kwambili amene anali kucita upainiya uku akulela ana. Pamene tinali kukhala limodzi, m’baleyu ananilimbikitsa kuganizilanso mmene zinthu zinalili pa umoyo wanga. Patapita miyezi yocepa cabe, n’naona kuti ningayambenso kutumikila monga mpainiya. Ena anali kuona kuti sin’naganize bwino popanga cosankha cimeneci. Ngakhale n’telo, n’nayambabe upainiya pokhulupilila kuti Yehova adzanithandiza kucita zambili mu ulaliki.

TINABWELELA KU QUEBEC KUKATUMIKILA MONGA APAINIYA APADELA

Mu 1964, ine na mkazi wanga Simone tinauzidwa kuti tikatumikile monga apainiya apadela m’tauni ya kwathu ku Quebec, ndipo tinatumikila kumeneko kwa zaka zingapo. Apa lomba citsutso pa nchito yathu yolalikila cinali citacepako. Koma anthu ena anali kutsutsabe.

Tsiku lina pa Ciŵelu masana, wapolisi ananigwila mu tauni yaing’ono ya Sainte-Marie, imene ili pafupi na mzinda wa Quebec. Iye anan’tengela ku polisi na kunitsekela m’citolokosi cifukwa colalikila ku nyumba na nyumba popanda cilolezo. Pambuyo pake, ananitengela ku khoti kwa woweluza wina wake wa maonekedwe ocititsa mantha, dzina lake Baillargeon. Iye ananifunsa kuti, ‘N’ndani adzakhala loya wako?’ N’tayankha kuti ni Glen How,a loya wodziŵika kwambili wa Mboni, mwamantha woweluzayo anati: “Mm, iyayi, osati uja!” Iye anada nkhawa cifukwa m’bale Glen How anali loya wodziŵika kwambili pa nchito yoteteza Mboni za Yehova pa milandu m’makhoti. Pasanapite nthawi, a khoti ananiuza kuti milandu yanga yonse yathetsedwa.

Popeza anthu anali kutsutsa nchito yathu yolalikila ku Quebec, cinali covuta kupeza malo abwino ocitilako misonkhano. Conco, mpingo wathu umene unali waung’ono, unali kusonkhana mu galaji yakale, mmene munali mozizila. M’nyengo yozizila kwambili, abale anali kuseŵenzetsa mbaula yamagetsi kuti m’galajiyo muthumeko. Tikakumana pamodzi, nthawi zambili tinali kukhala mozungulila mbaulayo kwa maawazi angapo misonkhano isanayambe, n’kumakambilana zocitika zolimbikitsa.

N’zolimbikitsa ngako kuona mmene nchito yolalikila yapitila patsogolo m’zaka zapitazi. M’zaka za m’ma 1960, mu mzinda wa Quebec na m’zigawo za Côte-Nord komanso Gaspé Peninsula, munali mipingo yocepa ing’ono-ing’ono. Koma masiku ano, m’madela atatu amenewa muli Mboni zambili-mbili, ndipo abale na alongo amasonkhana mu Nyumba za Ufumu zokongola.

KUITANIDWA KUKATUMIKILA MONGA WOYANG’ANILA WOYENDELA

M’bale Léonce Crépeault pamodzi na oyang’anila oyendela ena pa miting’i ya mu 1977, ku Toronto, m’dziko la Canada.

Mu 1977, n’nacita nawo miting’i ya oyang’anila madela ku Toronto m’dziko la Canada

Mu 1970, ine na mkazi wanga Simone tinapemphedwa kuti tiyambe kutumikila m’dela. Kenako mu 1973, tinapemphedwa kuti tikayambe kutumikila m’cigawo. M’zaka zimenezo, n’naphunzila zambili kwa abale aluso monga m’bale Laurier Saumurb na m’bale David Splane.c Onse anali kutumikila monga oyang’anila oyendela. Pambuyo pa msonkhano wadela ulionse, ine na M’bale Splane tinali kupatsana malangizo othandiza pa zimene tingacite kuti tiwonjezele maluso athu a kuphunzitsa. Nikumbukila nthawi ina m’bale Splane ananiuza kuti: “M’bale Crépeault, nakondwela maningi na nkhani yanu yothela. Mwaikamba bwino, koma mfundo zinaculuka kwambili moti nikanakhala ine, sembe naigaŵa-gaŵa n’kupanga nkhani zitatu!” Nthawi zambili, m’nkhani zanga n’nali kuikamo mfundo zambili-mbili. N’nafunika kuphunzila kukamba mfundo mwacidule.

Mapu yoonetsa mizinda ya ku Canada kumene M’bale Léonce Crépeault anatumikilako: Sainte-Marie, Quebec City, Montreal, na Toronto.

N’natumikila m’mizinda yosiyana-siyana m’cigawo ca kum’maŵa kwa dziko la Canada

Nchito ya oyang’anila zigawo inali yolimbikitsa oyang’anila madela. Koma popeza ofalitsa ambili ku Quebec anali kunidziŵa kwambili, nikamacezela madela awo, nthawi zambili anali kufuna kuti niziseŵenza nawo mu ulaliki. N’nali kukondwela kulalikila nawo pamodzi, koma vuto linali lakuti sin’nali kupatula nthawi yokwanila yolimbikitsa woyang’anila dela. Nikumbukila kuti pa nthawi ina, woyang’anila dela wina wacikondi ananiuza kuti: “Mucita bwino kupatula nthawi yolimbikitsa abale, koma musaiŵale kuti ino ni wiki yanga yoti munilimbikitse. Inenso nifunikila cilimbikitso!” Uphungu wacikondi umenewu unanithandiza kugaŵa bwino nthawi.

Mu 1976, panacitika zinthu zomvetsa cisoni zimene sin’nayembekezele. Mkazi wanga wokondedwa Simone, anadwala kwambili mpaka anamwalila. Anali mnzanga wabwino kwambili cifukwa anali wosadzikonda komanso anali kukonda kwambili Yehova. Kutaila nthawi yaitali mu ulaliki kunanithandiza kupilila imfa yake, ndipo nimayamikila Yehova kuti ananithandiza mwacikondi pa nthawi yovutayo. Patapita nthawi, n’nakwatila mpainiya wacangu wokamba Cizungu, dzina lake Carolyn Elliott. Iye anabwela ku Quebec kudzatumikila kosoŵa. Carolyn ni wofikilika ndipo amakondadi anthu, maka-maka omangika ndi amanyazi. Ananithandiza kwambili pamene anayamba kutumikila nane m’dela.

CAKA COSAIŴALIKA

Mu January 1978, n’nauzidwa kuti nikakhale mlangizi wa kilasi yoyamba ya Sukulu ya Utumiki Waupainiya mu Quebec. N’nali na nkhawa kwambili cifukwa n’nali nisanaloŵepo sukuluyi, ndipo ngakhale buku la apainiya n’nali nisanalionepo. Mwayi wake, m’kilasiyo munali apainiya ambili acidziŵitso. Olo kuti n’nali mlangizi, n’naphunzila zambili kwa iwo.

Patapita nthawi m’caka comweco, tinacita msonkhano wa maiko wa mutu wakuti: “Cikhulupililo Copambana.” Msonkhanowo unacitikila mu sitediyamu ya Olympic ku Montreal. Unali msonkhano waukulu umene unali usanacitikepo mu Quebec, ndipo ofalitsa oposa 80,000 anapezekapo. Pa msonkhanowo, n’nali kuseŵenzela ku Dipatimenti ya Nyuzi. N’nakamba na atolankhani ambili ndipo n’nakondwela kuona kuti analemba nkhani zabwino zambili zokhudza ife. Cina, anakonza pulogilamu yotifunsa mafunso pa TV na pa wailesi imene inatenga maawazi oposa 20, ndiponso anafalitsa nkhani m’manyuzipepala zofika m’mahandiledi. Tinacitila umboni wamphamvu kwambili.

KUSAMUKILA KU GAWO LINA

Mu 1996, zinthu zinasintha kwambili kwa ine. Kucokela pamene n’nabatikiza, n’nali kutumikila cabe m’gawo la anthu okamba Cifulenchi ku Quebec. Koma apa ananitumiza m’gawo la Cizungu ku Toronto. N’nali kuona kuti sinikanakwanitsa, ndiponso n’nali kuyopa kuti nidzakamba bwanji nkhani m’Cizungu cifukwa sin’nali kucidziŵa bwino. N’nafunika kupemphela kaŵili-kaŵili na kudalila kwambili Yehova.

N’nali na mantha kwambili pamene n’nali kuyamba kutumikila ku Toronto. Koma kukamba zoona, zaka ziŵili zimene n’natumikila m’gawo limeneli zinali zokondweletsa ngako. Mkazi wanga Carolyn, ananithandiza moleza mtima kuti niyambe kukamba Cizungu momasuka. Naonso abale ananicilikiza na kunilimbikitsa kwambili. Posapita nthawi, tinapeza mabwenzi atsopano ambili.

N’nali kukhala na zocita zambili zokonzekela msonkhano wadela wocitika ku mapeto kwa wiki. Kuwonjezela apo, nthawi zambili n’nali kupatulako ola limodzi pa Cisanu m’madzulo locita ulaliki wa ku nyumba na nyumba. Mwina ena anali kudabwa kuti n’cifukwa ciani n’nali kuyenda mu ulaliki pa Cisanu olo kuti ku mapeto kwa wiki tinali kukhala otangwanika kwambili na msonkhano. Koma ine n’nali kuona kuti makambilano abwino amene n’nali kukhala nawo mu ulaliki anali kunitsitsimula kwambili. Ngakhalenso lomba, kuyenda mu ulaliki kumanitsitsimula nthawi zonse.

Mu 1998, ine na mkazi wanga Carolyn anatiuza kuti tikatumikilenso ku Montreal monga apainiya apadela. Kwa zaka zambili, nchito yanga inali yolinganiza makampeni apadela a ulaliki wapoyela, komanso kukamba na atolankhani pothandiza kuti azifalitsa zoona ponena za Mboni za Yehova. Ine na mkazi wanga timakondwela kulalikila anthu a ku maiko ena amene anasamukila kuno ku Canada posacedwa. Nthawi zambili, anthu amenewa amakhala na cidwi cofuna kuphunzila zambili za Baibo.

M’bale Léonce Crépeault na mkazi wake, Carolyn.

Ine na mkazi wanga Carolyn

Nikaganizila zaka 68 zimene natumikila Yehova kucokela pamene n’nabatizika, nimaona kuti Yehova wanidalitsa kwambili. Nimakondwela kwambili cifukwa n’naphunzila kukonda ulaliki komanso nathandiza anthu ambili kudziŵa coonadi. Mwana wanga Lise na mwamuna wake anayamba upainiya wa nthawi zonse pamene ana awo anakula n’kudziimila paokha. Nimakondwela kuona kuti Lise akupitilizabe kulalikila mwacangu. Nimayamikila kwambili atumiki anzanga amene ananithandiza kupita patsogolo mwauzimu na kutumikila Yehova m’njila zosiyana-siya. Iwo ananithandiza mwa citsanzo cawo cabwino na malangizo awo anzelu. Ndipo naphunzila kuti tingathe kupitiliza kucita utumiki umene tapatsidwa m’gulu la Yehova kokha ngati tidalila mzimu wake woyela, umene ni wamphamvu. (Sal. 51:11) Nimamuyamikila Yehova cifukwa conipatsa mwayi wa mtengo wapatali wolemekeza dzina lake.—Sal. 54:6.

a Onani nkhani yofotokoza mbili ya M’bale W. Glen How, “The Battle Is Not Yours, but God’s,” mu Galamuka! ya Cizungu ya April 22, 2000 peji 18-24.

b Onani nkhani yokamba za mbili ya M’bale Laurier Saumur “I Found Something Worth Fighting For,” mu Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya November 15, 1976 peji 690-695.

c M’bale David Splane akutumikila m’Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani