NKHANI YOPHUNZILA 7
Timam’konda Kwambili Atate Wathu Yehova
“Ife timasonyeza cikondi, cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.—1 YOH. 4:19.
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
ZIMENE TIKAMBILANEa
1-2. N’cifukwa ciani Yehova anatitsegulila mwayi woloŵa m’banja lake? Nanga anacita bwanji zimenezo?
YEHOVA anatiitana kuti tiloŵe m’banja la olambila ake. Ndithudi, ni mwayi wamtengo wapatali kwambili kukhala m’banja limeneli! M’banjali muli Akhristu odzipatulila kwa Mulungu, amene amakhulupilila nsembe ya dipo la Mwana wake. Tilidi m’banja lacimwemwe. Tili na umoyo waphindu pali pano, komanso tili na ciyembekezo cokalandila moyo wosatha, kaya kumwamba kapena m’Paradaiso pano padziko lapansi.
2 Cifukwa cotikonda, Yehova anataya zambili kuti atitsegulile mwayi woloŵa m’banja lake. (Yoh. 3:16) Baibo imakamba kuti “tinagulidwa pa mtengo wokwela.” (1 Akor. 6:20) Kudzela mu dipo la Yesu, Yehova anapangitsa kuti zikhale zotheka kwa ife kukhala naye pa ubale. Conco, olo kuti Yehova ni wamkulu kwambili m’cilengedwe conse, tili na mwayi womuchula kuti Atate wathu. Ndipo monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yehova ni Tate wabwino koposa.
3. Ni mafunso ati amene tingafunse? (Onaninso bokosi lakuti “Kodi Yehova Amanionadi Kuti Ndine Wofunika?”)
3 Mofanana na wamasalimo, tingafunse kuti: “Yehova ndidzamubwezela ciani pa zabwino zonse zimene wandicitila?” (Sal. 116:12) Yankho ni lakuti sitingakwanitse kum’bwezela Atate wathu wakumwamba pa zonse zimene amaticitila. Koma zimene amaticitila zimatisonkhezela kumukonda. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Timasonyeza cikondi, cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Kodi tingaonetse bwanji kuti timamukonda Atate wathu wakumwamba?
KHALANIBE PA UBWENZI WOLIMBA NA YEHOVA
Timaonetsa kuti timam’konda kwambili Yehova, Atate wathu wacikondi wakumwamba, mwa kupemphela kwa iye, kumumvela, na kuthandiza ena kuti nawonso ayambe kumukonda (Onani ndime 4-14)
4. Malinga na Yakobo 4:8 n’cifukwa ciani tifunika kuyesetsa kukulitsa cikondi cathu pa Yehova?
4 Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi kuti tizikamba naye momasuka. (Ŵelengani Yakobo 4:8.) Amatilangiza kuti ‘tizilimbikila kupemphela,’ ndipo ni wokonzeka nthawi zonse kumvetsela mapemphelo athu. (Aroma 12:12) Iye sakhala wotangwanika kwambili kapena kukhala wolema cakuti n’kulephela kumvetsela mapemphelo athu. Ndipo ife timamvetsela kwa iye mwa kuŵelenga Mawu ake Baibo na zofalitsa zotithandiza kuimvetsetsa, komanso kumvetsela mwachelu tikakhala pamisonkhano. Cikondi pakati pa ana na makolo awo cimakula ngati amakambilana kaŵili-kaŵili. N’cimodzi-modzinso na cikondi cathu na Yehova. Cimakula ngati timakamba naye kaŵili-kaŵili.
Onani ndime 5
5. Kodi mapemphelo athu ayenela kukhala otani kuti Yehova azitimvetsela?
5 Kodi mapemphelo anu amakhala otani? Yehova amafuna kuti tizimukhuthulila za mu mtima mwathu pamene tipemphela. (Sal. 62:8) Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mapemphelo anga amangokhala oloŵeza monga nyimbo, kapena amakhala ocokeladi pansi pa mtima?’ N’zodziŵikilatu kuti mumamukonda kwambili Yehova, ndiponso mumafuna kukhalabe naye pa ubale wolimba. Kuti zimenezi zitheke, mufunika kumakamba naye kaŵili-kaŵili. Muzimufotokozela za mu mtima mwanu. Muzimuuzanso zimene zimakukondweletsani na zimene zimakudetsani nkhawa. Khalani omasuka kupempha thandizo kwa iye.
6. Kodi tifunika kucita ciani kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba na Atate wathu wakumwamba?
6 Kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba na Atate wathu wakumwamba, tifunika kumamuyamikila nthawi zonse. Tigwilizana na zimene wamasalimo anakamba, zakuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, mwaticitila zinthu zambili zodabwitsa, ndipo mumatiganizila. Palibe angafanane ndi inu. Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo, zimaculuka kwambili moti sindingathe kuzifotokoza.” (Sal. 40:5) Sitiyamikila Yehova mumtima cabe, koma timaonetsanso kuyamikila kwathu m’mawu na m’zocita zathu. Izi zimatipangitsa kukhala osiyana kwambili ndi anthu ambili m’dzikoli. Ambili m’dzikoli sayamikila zinthu zabwino zimene Yehova amawacitila. Ndipo kusayamikila ni mbali imodzi ya cizindikilo ca “masiku otsiliza.” (2 Tim. 3:1, 2) Tifunika kupewelatu khalidwe losayamikila limeneli.
7. Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala bwanji na Akhristu anzathu? Nanga n’cifukwa ciani?
7 Makolo safuna kuti ana awo azikangana, koma amafuna kuti azigwilizana. Mofananamo, Yehova amafuna kuti olambila ake onse azikondana na kugwilizana. Cikondi cimene tili naco pakati pathu n’cimene cimatidziŵikitsa kuti ndife Akhristu oona. (Yoh. 13:35) Tigwilizana na zimene wamasalimo analemba, zakuti: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!” (Sal. 133:1) Tikamakonda abale na alongo athu, timaonetsa kuti timam’kondadi Yehova. (1 Yoh. 4:20) Ni zokondweletsa ngako kukhala m’banja la abale na alongo amene ni “okomelana mtima,” komanso “acifundo cacikulu”!—Aef. 4:32.
ONETSANI CIKONDI MWA KUKHALA OMVELA
Onani ndime 8
8. Malinga na 1 Yohane 5:3, kodi cifukwa cacikulu cimene timamvelela Yehova n’citi?
8 Yehova amafuna kuti ana azimvela makolo awo. Amafunanso kuti ife tizimumvela monga ana ake. (Aef. 6:1) Tifunika kumumvela cifukwa ndiye anatilenga, amatipatsa zofunikila mu umoyo, ndiponso ni kholo lanzelu kwambili kuposa kholo lina lililonse. Koma cifukwa cacikulu cimene timamvelela Yehova n’cakuti timamukonda. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Olo kuti pali zifukwa zambili zimene ziyenela kutipangitsa kumvela Yehova, iye satikakamiza kumumvela. Anatipatsa ufulu wodzisankhila zocita, ndipo amakondwela tikasankha kumumvela cifukwa comukonda.
9-10. N’cifukwa ciani kudziŵa malamulo a Mulungu na kuwatsatila n’kofunika?
9 Makolo amafuna kuti ana awo azikhala motetezeka. Ndiye cifukwa cake amawapatsa malamulo a mmene afunika kukhalila. Malamulo amenewo amawateteza anawo. Ana akamamvela malamulowo, amaonetsa kuti amalemekeza makolo awo na kuwadalila. Nanga kuli bwanji ife? Kodi sitiyenela kuwadziŵa bwino malamulo amene Atate wathu wakumwamba anatipatsa na kuyesetsa kuwatsatila? Tikamamvela malamulo a Yehova, timaonetsa kuti timam’konda na kumulemekeza, ndiponso kucita zimenezi kumatipindulitsa. (Yes. 48:17, 18) Koma anthu amene amakana kumvela malamulo a Mulungu, amadzibweletsela okha mavuto.—Agal. 6:7, 8.
10 Ngati titsatila malamulo a Yehova mu umoyo wathu, timakhala otetezeka mwakuthupi na mwauzimu. Timakhalanso na umoyo wacimwemwe. Yehova amadziŵa zimene zingatithandize kukhala na umoyo wabwino kwambili. Mlongo Aurora, amene akhala ku America anati, “Nidziŵa kuti kumvela Yehova kumatithandiza kukhala na umoyo wabwino koposa nthawi zonse.” Mfundo imeneyi ni ya zoona. Umu ni mmene zimakhalila nthawi zonse. Kodi imwe mwapindula bwanji pa umoyo wanu cifukwa comvela malangizo acikondi a Yehova?
11. Kodi pemphelo limatithandiza bwanji?
11 Pemphelo limatithandiza kukhala omvela ngakhale pamene kucita zimenezi kuli kovuta. Nthawi zina, zingativute kumvela Yehova cifukwa copanda ungwilo, koma tiyenela kuyesetsa nthawi zonse kumumvela. Wamasalimo anacondelela Mulungu kuti: “Ndithandizeni kukhala wozindikila kuti nditsatile cilamulo canu, ndiponso kuti ndicisunge ndi mtima wonse.” (Sal. 119:34) Mlongo Denise, amene ni mpainiya anati, “Zikanivuta kumvela lamulo linalake la Yehova, nimapemphela kuti anipatse mphamvu zonithandiza kucita coyenela.” Sitikayikila kuti Yehova nthawi zonse amayankha mapemphelo otelo.—Luka 11:9-13.
THANDIZANI ENA KUTI AZIKONDA ATATE WATHU
12. Malinga na Aefeso 5:1, kodi tiyenela kucita ciani?
12 Ŵelengani Aefeso 5:1. Pokhala “ana [a Yehova] okondedwa,” timacita zonse zotheka kuti titengele citsanzo cake. Timatengela makhalidwe ake mwa kukhala acikondi, okoma mtima, ndiponso okhululuka pocita zinthu na ena. Anthu osadziŵa Mulungu akaona makhalidwe athu abwino, angakopeke cakuti angafune kuphunzila zambili za Yehova. (1 Pet. 2:12) Makolo acikhristu ayenela kuyesetsa kucita zinthu mwacikondi ndi ana awo monga mmene Yehova amacitila nafe. Akamatelo, nawonso ana awo angafune kukhala mabwenzi a Atate wathu wacikondi, Yehova.
Onani ndime 13
13. Kodi tiyenela kukumbukila ciani?
13 Mwana amaŵanyadila atate ŵake. Amakondwela kuuzako ena za iwo. Nafenso timanyadila kuti tili na Atate wathu wakumwamba Yehova, ndipo timafuna kuti ena amudziŵe. Tonsefe tingakambe monyadila monga mmene Mfumu Davide anakambila kuti: “Ndidzadzitamandila mwa Yehova.” (Sal. 34:2) Koma bwanji ngati timacita manyazi kukamba ndi anthu za Yehova? Kodi n’ciani cingatithandize kukhala wolimba mtima? Cingatithandize ni kukumbukila kuti Yehova amakondwela ngako ngati tiuzako ena za iye. Tifunikanso kukumbukila mmene ena amapindulila tikawauza za Yehova. Tikatelo, Yehova adzatithandiza kukhala olimba mtima monga mmene anathandizila Akhristu a m’nthawi ya atumwi.—1 Ates. 2:2.
14. Ni zifukwa zabwino ziti zimene zimatituntha kugwila nchito yolalikila?
14 Yehova alibe tsankho, ndipo amakondwela akaona kuti timaonetsa cikondi kwa ena mopanda tsankho. (Mac. 10:34, 35) Njila imodzi yabwino kwambili imene timaonetsela cikondi kwa ena ni kuwauzako uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Kodi kugwila nchitoyi kuli na mapindu otani? Anthu akamvetsela uthenga wabwino, umoyo wawo umasintha kwambili komanso amakhala na ciyembekezo codzakhala na moyo wamuyaya.—1 Tim. 4:16.
TIYENELA KUKONDA ATATE WATHU KUTI TIKHALE ACIMWEMWE
15-16. Kodi tili na zifukwa ziti zokhalila acimwemwe?
15 Yehova ni Tate wacikondi. Iye amafuna kuti banja lake lizikhala lacimwemwe. (Yes. 65:14) Ngakhale kuti timakumana na mavuto, tili na zifukwa zambili zokhalila acimwemwe. Mwacitsanzo, timadziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambili. Tili na cidziŵitso colongosoka ca Mawu a Mulungu, Baibo. (Yer. 15:16) Cinanso, tili m’banja lapadela la anthu okondana, amenenso amakonda Yehova na malamulo ake.—Sal. 106:4, 5.
16 Timakhalabe acimwemwe cifukwa tili na ciyembekezo codalilika cakuti kutsogolo tidzakhala na umoyo wabwino kwambili. Timadziŵa kuti posacedwa Yehova adzawononga oipa onse, ndipo mu Ufumu wake adzakonza dziko lonse lapansi kukhala Paradaiso. Tilinso na ciyembekezo cokondweletsa kwambili cakuti anthu amene anamwalila adzaukitsidwa, moti adzakhalanso pamodzi na okondedwa awo. (Yoh. 5:28, 29) Idzakhala nthawi yokondweletsa cotani nanga! Koposa zonse, tili na cikhulupililo cakuti posacedwa, aliyense kumwamba na padziko lapansi, adzalemekeza Yehova Atate wathu wacikondi, adzamulambila na kum’tamanda. Ndipo izi n’zimene iye amafunikila.
NYIMBO 12 Mulungu Wamkulu, Yehova
a Tidziŵa kuti Atate wathu Yehova amatikonda kwambili, ndipo watibweletsa m’banja la olambila ake. N’cifukwa cake nafenso timam’konda. Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’kondadi Yehova Atate wathu? M’nkhani ino, tikambilana zina zimene tingacite kuti tionetse kuti timam’konda.