LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 2 masa. 10-12
  • Zimene Mungacite Kuti Mukakhalemo m’Dziko Latsopano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Mungacite Kuti Mukakhalemo m’Dziko Latsopano
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TIYENELA “KUDZIŴA” MULUNGU KUTI TIKAPULUMUKE MAPETO A DZIKO
  • MUZIŴELENGA MAWU A MULULNGU BAIBO TSIKU LILILONSE
  • MUZIPEMPHELA KWA MULUNGU KUTI AKUTHANDIZENI
  • Kodi Mulungu Waticitila Zotani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kutifela?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Mungakhale na Moyo Kwamuyaya Padziko Lapansi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • N’zotheka Kudzakhala na Moyo Kwamuyaya
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 2 masa. 10-12

Zimene Mungacite Kuti Mukakhalemo m’Dziko Latsopano

Nkhani zapita zaonetsa kuti posacedwapa, Mulungu adzawononga anthu oipa na kuthetsa mavuto onse padzikoli. Sitiyenela kukayikila kuti zimenezi zidzacitika. Cifukwa ciani? Cifukwa Baibo, Mawu a Mulungu, inakambilatu kuti:

“Dziko likupita.”—1 YOHANE 2:17.

Tidziŵa kuti padzakhala opulumuka cifukwa vesi imene ili pamwambayi imakambanso kuti:

“Wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.”

Conco kuti munthu akapulumuke ayenela kucita cifunilo ca Mulungu. Kuti tidziŵe cifunilo ca Mulungu, coyamba tiyenela kum’dziŵa bwino Mulunguyo.

TIYENELA “KUDZIŴA” MULUNGU KUTI TIKAPULUMUKE MAPETO A DZIKO

Zithunzi: 1. Nesi wakhala pansi m’cipatala ali wolema komanso wopanikizika kwambili maganizo. 2. Pa nthawi yopumula, wapita ku malo odyela. Kumeneko waona wanchito mnzake akuŵelenga magazini mwacimwemwe. 3. Mnzakeyo akumuŵelengela vesi ya m’Baibo na kum’patsa kakhadi kongenela pa webusaiti ya jw.org.

Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yohane 17:3) Kuti tikapulumuke mapeto a dzikoli na kudzakhala na moyo kwamuyaya, tiyenela “kudziŵa” Mulungu. Izi sizitanthauza cabe kukhulupilila kuti Mulungu aliko, kapena kudziŵako zinthu zina zocepa zokhudza iye. Koma tiyenela kukhala naye paubwenzi. Kuti ubwenzi wathu na munthu wina ulimbe, timafunika kupatula nthawi yoceza naye. N’zimenenso tiyenela kucita kuti ubwenzi wathu na Mulungu ulimbe. Onani mfundo zina zofunika za coonadi zimene timaphunzila m’Baibo, zimene zingatithandize kukhala pa ubwenzi na Mulungu na kuulimbitsa.

Mfundo za Coonadi Zimene Timaphunzila m’Baibo

Pamene ali ku nyumba kwake, nesiyo akuona pa webusaiti ya jw.org.

Timaphunzila kuti Mulungu anali kufuna kuti tizikhala m’Paradaiso.

Iye analenga anthu oyambilila, Adamu na Hava, na kuwaika m’munda wokongola wochedwa Edeni. Iwo anali angwilo ndipo Mulungu anawapatsa zonse zofunikila kuti azikhala osangalala. Sembe kuti Adamu na Hava anapitiliza kukhala mabwenzi a Mulungu, akanakhala na moyo kwamuyaya, sakanafa. Koma anasankha kusamvela lamulo losavuta limene Mulungu anawapatsa.

Timaphunzila cifukwa cake timavutika masiku ano.

Cifukwa ca kusamvela Mulungu, munthu woyambilila Adamu anataya mwayi wokhala na moyo kwamuyaya. Ndipo kusamvela kwake kunapangitsanso kuti mtundu wonse wa anthu umanidwe mwayi umenewo. Baibo imafotokoza kuti: “Monga mmene uchimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa uchimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” (Aroma 5:12) Mofanana na mmene munthu amatengela cilema kwa makolo ake, ana onse a Adamu anatengela kupanda ungwilo kwake. Ndiye cifukwa cake timakalamba na kufa.

Timaphunzila zimene Mulungu anacita kuti atithandize.

Baibo imati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzapeleke moyo wake kaamba ka ife. Ponena za cikondi cimene Mulungu anaonetsa, mwamuna wina wa ku India dzina lake Prabhakar, anati: “Zimenezi zimaonetsa kuti Yehovaa amanikonda kwambili. Cikondi cake canipatsa ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha.”

Timaphunzila mmene tingaonetsele kuyamikila pa zimene Mulungu anaticitila.

Baibo imakamba kuti tingaonetse kuyamikila pa zimene Mulungu anaticitila mwa “kusunga malamulo ake.” (1 Yohane 2:3) Yehova Mulungu mwacikondi amatiphunzitsa zimene tingacite kuti tizisangalala na umoyo pa nthawi ino. (Yesaya 48:17, 18) Mulungu safuna kuti tizivutika. Iye analonjeza kuti ngati titsatila malangizo ake, tidzakhala na umoyo wokondweletsa panthawi ino, komanso tidzakhala na mwayi wokasangalala na moyo kwamuyaya.

MUZIŴELENGA MAWU A MULULNGU BAIBO TSIKU LILILONSE

Nesi uja wakhala panja, pa nthawi yopumula masana, ndipo akuyang’ana kumwamba pambuyo poŵelenga Baibo.

Mungapulumuke mapeto a dzikoli mwa kupempha thandizo la Mulungu na kucita cifunilo cake.

Timadya cakudya nthawi zonse kuti tikhalebe na moyo. Koma Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”—Mateyu 4:4.

Masiku ano, mawu a Yehova timawapeza m’Baibo. Mukamaŵelenga buku lopatulika limeneli, mudzadziŵa zimene Mulungu anacita kalelo, zimene akucita tsopano, na zimene adzacita kutsogolo.

MUZIPEMPHELA KWA MULUNGU KUTI AKUTHANDIZENI

Kodi mungacite ciani ngati mumafuna kumvela Mulungu koma zimakuvutani kuleka kucita zinthu zimene iye amati n’zoipa? Ngati zili conco, kum’dziŵa bwino Mulungu kungakuthandizeni kwambili.

Ganizilani za mayi wina amene tam’patsa dzina lakuti Sakura. Iye anali na khalidwe laciwelewele. Atayamba kuphunzila Baibo, anadziŵa za lamulo la Mulungu lakuti “thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Sakura anapemphela kwa Mulungu kuti amupatse mphamvu, ndipo anakwanitsa kuleka khalidwe loipalo. Koma nthawi zina amalimbanabe na mayeselo. Iye anati: “Maganizo oipa akabwela mumtima mwanga, nimauza Yehova zonse m’pemphelo, cifukwa nidziŵa kuti panekha siningakwanitse kulimbana nazo. Pemphelo lanithandiza kwambili kuti nikhale pafupi na Yehova.” Mofanana na Sakura, anthu mamiliyoni akuphunzila za Mulungu. Iye amawapatsa mphamvu zofunikila kuti asinthe umoyo wawo, na kukhala na umoyo umene umam’kondweletsa.—Afilipi 4:13.

Mukam’dziŵa bwino Mulungu, nayenso ‘adzakudziŵani’ monga bwenzi lake. (Agalatiya 4:9; Salimo 25:14) Mukacita zimenezi, mudzapulumuka na kukaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Koma kodi dziko latsopano limenelo lidzakhala lotani? Nkhani yotsatila idzafotokoza.

a Baibo imakamba kuti dzina la Mulungu ni Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani