LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 February masa. 26-30
  • Nakhala Nikuona Cikhulupililo ca Anthu a Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Nakhala Nikuona Cikhulupililo ca Anthu a Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NORTHERN IRELAND—“DZIKO LA MABOMBA NA ZIPOLOPOLO”
  • SIERRA LEONE—AUMPHAWI KOMA OKHULUPILIKA
  • KU NIGERIA N’NAPHUNZILA CIKHALIDWE CATSOPANO
  • ABALE KU KENYA ANALI KULEZA NANE MTIMA
  • KU AMERICA—OPEZA BWINO KOMA OKHULUPILIKA
  • ‘Anthu Okumvelani’ Adzapulumuka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kucita Zimene Yehova Watilamula Kumabweletsa Madalitso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 February masa. 26-30
M’bale Robert Landis.

MBILI YANGA

Nakhala Nikuona Cikhulupililo ca Anthu a Yehova

WOSIMBA NI MWINIWAKE: ROBERT LANDIS

MWINA mumakumbukila makambilano amene munakhalapo nawo omwe anali opindulitsa kwa inu. Ine nikumbukila bwino makambilano amene n’nali nawo na mnzanga wina ku Kenya zaka 50 zapitazo, pamene tinali kuwotha moto. Pa nthawiyo, tinali paulendo wautali komanso wotopetsa umene unatenga miyezi ingapo. Poceza tinakambilana za filimu inayake yokhudza zacipembedzo. Ndiyeno mnzangayo anati, “Filimu imeneyo siinafotokoze zoona zokhudza Baibo.”

N’naseka cifukwa mnzangayo anaoneka kuti sadziŵa zacipembedzo. N’nafunsa kuti, “Udziŵapo ciyani za Baibo?” Iye anazengeleza kupeleka yankho. Pothela pake, ananiuza kuti amayi ake ni a Mboni za Yehova, ndipo anaphunzilako zinthu zina kwa iwo. Cifukwa cocita cidwi, n’nam’pempha kuti aniuze zambili.

Tinakambilana pafupifupi usiku wonse. Mnzangayo ananiuza kuti Baibo imaonetsa kuti Satana ndiye akulamulila dzikoli. (Yoh. 14:30) Mwina mwakhala mukudziŵa zimenezi kwa moyo wanu wonse. Koma kwa ine mfundoyo inali yatsopano komanso yocititsa cidwi. Nthawi zonse n’nali kumva anthu akunena kuti Mulungu wokoma mtima komanso wacilungamo ndiye alamulila dzikoli. Koma n’nali kulephela kumvetsa zimenezi nikaganizila zimene n’nakumana nazo pa umoyo. Ngakhale kuti n’nali na zaka 26 cabe, n’nali n’takumana na mavuto ambili.

Atate anali msilikali ku United States, ndipo anali woyendetsa ndeke za nkhondo. Conco nili mwana, n’nali kudziŵa kuti asilikali anali okonzeka kuphulitsa mabomba nthawi iliyonse. Nkhondo ya ku Vietnam inadodometsa maphunzilo anga a ku koleji ku California. Conco, n’naloŵa m’gulu la ana a sukulu amene anali kucita zionetselo. Apolisi a zida m’manja anatithamangitsa, ndipo tinathaŵa uku tikulephela kuona bwino-bwino cifukwa ca utsi wokhetsa misozi (tear gas) umene unatiloŵa m’maso. Inali nthawi ya cipwilikiti komanso msokonezo wokha-wokha. Anthu andale anali kuphana, kucita zionetselo, komanso zipolowe. Aliyense anali na maganizo osiyana othetsela vutolo. Panali msokonezo wokha-wokha!

M’bale Robert waimilila pafupi na mthuthuthu wake, ndipo akuonetsa mapu ya ulendo wake.

Kucokela ku London kupita ku Central Africa

Mu 1970, n’nayamba kugwila nchito kumpoto kwa Alaska, ndipo n’nali kulandila ndalama zambili. Ndiyeno n’napita ku London. Kumeneko n’nagula mthuthuthu na kuloŵela kum’mwela, koma sin’nali kudziŵa kumene n’nali kupita. Patapita miyezi, n’nafika ku Africa. Pa ulendowo, n’nali kukumana na anthu amene anali ofunitsitsa kumasuka ku mavuto awo.

Conco, n’naona kuti zimene Baibo imanena zakuti colengedwa cauzimu ndico cikulamulila dzikoli n’zoona, cifukwa ca mavuto amene n’nali kuona na kumva. Koma n’nadzifunsa kuti, “Ngati Mulungu si ndiye akulamulila dzikoli, kodi akucita ciyani?”

M’miyezi yotsatila n’napeza yankho lake. Ndipo m’kupita kwa nthawi, n’nadziŵana na amuna komanso akazi ambili. Iwo anali okhulupilika kwa Mulungu yekha woona olo kuti anali kukumana na mavuto osiyanasiyana, ndipo n’nafika powakonda.

NORTHERN IRELAND—“DZIKO LA MABOMBA NA ZIPOLOPOLO”

Pamene n’nabwelela ku London, n’nakambilana na amayi a mnzanga uja, ndipo iwo ananipatsa Baibo. Pambuyo pake, n’napita ku mzinda wa Amsterdam, ku Netherlands. Kumeneko, wa Mboni wina ananiona nikuŵelenga Baibo n’takhala pansi, ndipo ananithandiza kudziŵa zambili. Kenako, pamene n’nali mumzinda wa Dublin, ku Ireland, n’napita kukaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. N’nagogoda pakhomo, ndipo n’taloŵa n’nakumana na m’bale Arthur Matthews. Iye anali wanzelu komanso ciyambakale. N’nam’pempha kuti aziniphunzitsa Baibo, ndipo anavomela.

N’nali wodzipeleka kwambili pophunzila Baibo, komanso n’nali kuŵelenga mwakhama mabuku na magazini ofalitsidwa na Mboni. N’nali kuŵelenganso Baibo yeniyeniyo. Zinali zosangalatsa! Pa misonkhano yampingo, n’naona kuti ngakhale ana anali kudziŵa mayankho pa mafunso omwe anthu ophunzila akhala akufuna-funa mayankho ake kwa zaka zambili. Mafunsowo ni monga akuti: ‘N’cifukwa zinthu zoipa zimacitika? Kodi Mulungu ndani? N’ciyani cimacitika munthu akamwalila?’ A Mboni za Yehova ndiwo anakhala mabwenzi anga cifukwa ndiwo okha amene n’nali kudziŵa m’dzikolo. Iwo ananithandiza kum’konda Yehova na kucita cifunilo cake.

Nili na Nigel komanso Denis

Mu 1972 n’nabatizika. Patapita caka cimodzi, n’nakhala mpainiya ndipo n’napita kukacilikiza mpingo waung’ono ku Newry, Northern Ireland. Kumeneko n’nali kucita lendi nyumba imene inali payokha-yokha mphepete mwa phili. Pafupi na nyumbayo panali malo odyela ng’ombe, ndipo n’nali kuyeseza nkhani zanga pamaso pa ng’ombezo. Zinali kuoneka kuti zikumvetsela mwachelu kwinaku zikutafuna msipu. Poti sizilankhula, sizinali kuniwongolela pomwe sin’nacite bwino. Koma kucita zimenezi kunali kunithandiza kuti niphunzile kuyang’ana omvela nikamakamba nkhani. Mu 1974, n’naikidwa kukhala mpainiya wapadela, ndipo n’nayamba kutumikila na m’bale Nigel Pitt. Iye anadzakhala mnzanga kwa moyo wonse.

Panthawiyo, kunali ciwawa cosaneneka ku Northern Ireland. Conco, anthu ena anacha dzikoli kuti “dziko la mabomba na zipolopolo.” Paliponse tinali kuona anthu akumenyana, kuwombelana mfuti, kuphulitsa magalimoto, na zina zotelo. Nkhani zandale komanso zacipembedzo ndizo zinabweletsa mavuto amenewa. Komabe Apulotesitanti na Akatolika anali kudziŵa kuti Mboni za Yehova sizimatengako mbali m’zandale. Conco, tinali kulalikila momasuka komanso motetezeka. Nthawi zambili, anthu amene tinali kuwalalikila akadziŵa nthawi komanso malo kumene kudzacitika ciwawa, anali kuticenjeza kuti tisaike moyo wathu pa ciwopsezo.

Ngakhale n’telo, tinali kukumana na zovuta. Tsiku lina, ine na mpainiya mnzanga Carrigan tinapita kukalalikila kudela lina lapafupi kumene kunalibe Mboni za Yehova, komanso kumene tinangopitako kamodzi kokha m’mbuyomu. Kumeneko mzimayi wina anatiimba mlandu wakuti ndife asilikali acisinsi a ku Britain, mwina cifukwa cakuti sitinali kudziŵa bwino kukamba ci Irish. Izi zinaticititsa mantha. Kucita zinthu mwaubwenzi na asilikali kukanapangitsa kuti uphedwe kapena kuwombeledwa mfuti m’nkhongono. Titaima panja tokha-tokha tikuyembekezela basi apo n’kuti kwazizila, tinangoona motoka yabwela pa lesitilandi imene panali mzimayi uja amene anatiimba mlandu. Mzimayiyo anatuluka panja n’kukambilana na amuna aŵili amene anali m’motokayo uku akuloza ife. Amunawo anabwela kwa ife na kutifunsa mafunso angapo okhudza nthawi yofika basi. Basiyo itafika, iwo anayamba kukambilana na dalaivala. Sitinali kumva zimene anali kulankhula. M’basimo munalibe munthu aliyense. Conco, tinangoti basi apanga ciwembu cakuti akathane nafe kunja kwa tauni. Koma zimenezo sizinacitike. Pamene n’natuluka m’basimo, n’nafunsa dalaivalayo kuti: “Kodi amuna aŵili aja anali kukufunsani ciyani za ife?” Iye anayankha kuti: “Ine nimakudziŵani, ndipo nawafotokozela. Musade nkhawa. Ndinu otetezeka.”

M’bale Robert na mkazi wake pa tsiku la ukwati wawo.

Pa tsiku la cikwati cathu, March 1977

Mu 1976 pa msonkhano wacigawo, n’nakumana na mlongo Pauline Lomax, mpainiya wapadela amene anacokela ku England. Anali mlongo wauzimu, wodzicepetsa, komanso wokongola. Iye na mlongosi wake Ray, anaphunzila coonadi kuyambila ali acicepele. Pambuyo pa caka cimodzi, ine na Pauline tinakwatilana, ndipo tinapitiliza kucita upainiya wapadela ku Ballymena, Northern Ireland.

Tinali m’nchito yadela kwa nthawi yaitali, kutumikila abale athu ku Belfast, Londonderry, komanso kumalo ena oopsa. Tinalimbikitsidwa kwambili poona cikhulupililo ca abale na alongo amene anasiya zikhulupililo zacipembedzo, tsankho, na cidani, zimene zinali zozika mizu kuti atumikile Yehova. Iye anawadalitsa na kuwateteza.

Ku Ireland n’nakhalako zaka 10. Ndiyeno mu 1981 anatiitana kuti tikaloŵe sukulu ya Giliyadi ya kalasi nambala 72. Titatsiliza maphunzilowo, anatitumiza ku Sierra Leone, ku West Africa.

SIERRA LEONE—AUMPHAWI KOMA OKHULUPILIKA

Pa nyumba ya amishonale imene tinali kukhala tinalipo anthu 11. Tonse tinali kugwilitsa nchito cipinda cimodzi cophikila, zimbuzi zitatu, zipinda ziŵili zosambila, foni imodzi, makina amodzi ocapila zovala, komanso amodzi oumitsila zovala. Magetsi anali kuzimazima nthawi iliyonse. Mu mtenje munali makoswe osaneneka, komanso njoka zinali kuloŵa m’cipinda capansi.

M’bale Robert na anthu ena ali na mithuthuthu, ndipo akuwoloka mtsinje.

Tikuwoloka mtsinje kupita ku msonkhano m’dziko la Guinea

Ngakhale panali zovuta zonsezi, utumiki wathu tinali kusangalala nawo kwambili. Anthu anali kuilemekeza Baibo, komanso anali kumvetsela mwacidwi tikamawalalikila. Ambili anaphunzila Baibo, ndipo anakhala Mboni. Anthu kumeneko anali kunichula kuti “Bambo Robert.” Mkazi wanga Pauline anali kumuchula kuti “Mayi Robert.” Koma n’tayamba kutangwanika kwambili na nchito pa ofesi ya nthambi, nthawi yopita mu ulaliki inali kunicepela. Conco, anthu anayamba kuchula mkazi wanga Pauline kuti “Mayi Pauline.” Ine anayamba kunichula kuti “Bambo Pauline.” Izi zinali kum’kondweletsa mkazi wanga.

M’bale Robert na mkazi wake ali pa motoka yawo.

Tili pa ulendo wokalalikila ku Sierra Leone

Abale na alongo ambili anali osauka. Koma nthawi zonse Yehova anali kusamalila zosoŵa zawo, nthawi zina m’njila yapadela. (Mat. 6:33) Nikumbukila tsiku lina, mlongo wina anali na ndalama yokhayo yogulila cakudya ca tsiku limodzi ca iye na ana ake. Koma anapeleka ndalamayo kwa m’bale wina wodwala malungo kuti akagulile mankhwala. Ndiyeno tsiku lomwelo, mosayembekezela mayi wina anapita kwa mlongoyo, na kupeleka ndalama kuti amuluke tsitsi. Panalinso zocitika zina zambili ngati zimenezi.

KU NIGERIA N’NAPHUNZILA CIKHALIDWE CATSOPANO

Ku Sierra Leone tinakhalako zaka 9. Kenako, anatitsamutsila ku Beteli ku Nigeria. Ofesi ya nthambi imeneyi inali yaikulu, ndipo n’nali kugwila nchito imodzimodzi ya mu ofesi imene n’nali kucita ku Sierra Leone. Koma mkazi wanga anam’patsa nchito ina yatsopano komanso yovuta. Iye anali kuthela maola 130 mu ulaliki mwezi uliwonse, na kutsogoza maphunzilo a Baibo opita patsogolo. Koma tsopano anam’patsa nchito yosoka zovala zong’ambika, ndipo anali kucita zimenezo tsiku lililonse. Zinam’tengela nthawi kuti azoloŵele. Koma anazindikila kuti abale na alongo anali kuyamikila ngako utumiki wake, ndipo anaika maganizo ake pa kulimbikitsa atumiki ena a pa Beteli.

Cikhalidwe ku Nigeria cinali catsopano kwa ife. Panali zambili zofunika kuphunzila. Tsiku lina, m’bale wina anabwela ku ofesi kwanga kuti anionetse mlongo amene anangoitanidwa kumene pa Beteli. N’tatambasula dzanja kuti nim’patse moni, mlongoyo anagwada pansi. N’nadabwa kwambili! Nthawi yomweyo n’naganizila lemba la Machitidwe 10:25, 26 komanso Chivumbulutso 19:10. Mumtima n’nati, ‘Kodi nimuuze kuti asacite zimenezo?’ Panthawi imodzimodzi, n’naganiza kuti popeza waitanidwa ku Beteli, ayenela kuti akudziŵa bwino zimene Baibo imaphunzitsa.

Koma sin’nali womasuka pa makambilano amenewo. Conco pambuyo pake, n’nacita kafukufuku. Zimene n’napeza n’zakuti mlongoyo anacita zimenezo malinga na cikhalidwe cimene anthu anali kutsatila m’madela ena a dzikolo. Nawonso amuna anali kugwada n’kuŵelama monga njila yoonetsela ulemu, osati kulambila ayi. Ndipo m’Malemba muli zitsanzo za anthu amene anacitapo zimenezo. (1 Sam. 24:8) N’nakondwela kwambili kuti sin’nakambe zinthu zimene zikanacititsa manyazi mlongo wangayo, olo kuti sin’namvetse cifukwa cimene anacitila zimenezo.

Ku Nigeria, tinadziŵana na abale komanso alongo ambili amene anaonetsa cikhulupililo colimba kwa zaka zambili. Mwacitsanzo, panali m’bale wina dzina lake Isaiah Adagbona.a M’baleyu anaphunzila coonadi ali wacinyamata. Koma m’kupita kwa nthawi anadzakhala na khate. Iye anapelekedwa ku malo osungilako akhate, kumene ndiye yekha anali Mboni. Ngakhale kuti anali kutsutsidwa, anathandiza anthu akhate oposa 30 kuphunzila coonadi. Ndipo anafika ngakhale pokhazikitsa mpingo kumalo amenewo.

ABALE KU KENYA ANALI KULEZA NANE MTIMA

Ku Kenya titapeza cipembele ali yekha

Mu 1996 anatitumiza ku ofesi ya nthambi ku Kenya. Uku kunali kuyamba kubwelelanso ku Kenya, kucokela nthawi imene n’nadzafika m’dzikoli monga nachulila kuciyambi kwa nkhani ino. Tinali kukhala pa Beteli. Pamalo amenewa panali kufikanso akolwe (apusi). Iwo anali kutsomphola zipatso zimene alongo anali kunyamula. Tsiku lina, mlongo wina pa Beteli anasiya windo ya cipinda cake yotsegula. Atabwela ku cipinda, anapeza akolwe oculuka akusangalala na cakudya m’cipindamo. Iye anakuwa na kuthamangila panja. Nawonso akolwe amenewo analumpha kutulukila pawindo.

Ine na mkazi wanga Pauline tinayamba kusonkhana na mpingo wa Ciswahili. Posakhalitsa, n’nayamba kutsogoza Phunzilo la Buku la Mpingo (imene masiku ano ni Phunzilo la Baibo la Mpingo). Komabe, sin’nali kudziŵa bwino kukamba cinenelo cimeneco. N’nali kukonzekela phunzilo limenelo kukali nthawi, kuti nikathe kukawaŵelenga bwino mafunso. Cifukwa cosadziŵa bwino Ciswahili, cinali covuta kudziŵa ngati zimene ena ayankha m’gulu n’zolondola. N’nali kumva kuipa. Koma niyamikila kwambili kuti analeza nane mtima, ndipo modzicepetsa analola kuti nizitsogoza phunzilolo.

KU AMERICA—OPEZA BWINO KOMA OKHULUPILIKA

Ku Kenya tinacokako caka cisanakwane, cifukwa mu 1997 anatiitana kuti tizitumikila pa Beteli ku Brooklyn, New York. Lomba tili m’dziko limene anthu ali na zinthu zambili zakuthupi, zimene zimakhala na mavuto ake. (Miy. 30:8, 9) Koma ngakhale m’maiko olemela, abale na alongo athu amakhalabe na cikhulupililo colimba. Iwo amagwilitsa nchito nthawi na cuma cawo, osati kuti azipindulitse, koma kuti athandizile pa nchito za gulu la Yehova.

Kwa zaka zambili, takhala tikuona cikhulupililo colimba ca Akhristu anzathu m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Ku Ireland, tinaona kuti abale athu anali na cikhulupililo colimba olo kuti m’dzikolo munali ciwawa. Ku Africa, abale athu anali na cikhulupililo olimba mosasamala kanthu za umphawi. Ndipo kuno ku America, abale athu ali na cikhulupililo colimba ngakhale kuti ali na zinthu zambili zakuthupi. Mosakayikila, Yehova amakondwela akaona anthu amene amaonetsa kuti amam’konda kaya akhale m’mikhalidwe yotani.

Ine na Pauline pa Beteli ku Warwick

Zaka zikupita mofulumila “kuposa mmene cimathamangila cowombela nsalu.” (Yobu 7:6) Palipano, tili ku likulu la padziko lonse ku Warwick, New York, ndipo tikupitiliza kutumikila na anthu amene amakondanadi. Ndife acimwemwe komanso okhutila kucita zimene tingathe pothandizila Mfumu yathu, Khristu Yesu, amene posacedwa adzafupa anthu ake okhulupilika osaŵelengeka.—Mat. 25:34.

a Mbili ya m’bale Isaiah Adagbona inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1998, masa. 22-27. M’baleyu anamwalila mu 2010.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani