LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 December tsa. 32
  • Cocitika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cocitika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Muzimvela Anthu Onse Cifundo
  • Tengelani Khalidwe la Yehova la Cifundo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Kodi Mwacikonzekela Cisautso Cacikulu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Muzicitila Cifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Amvetseleni, Adziŵeni Bwino, Aonetseni Cifundo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 December tsa. 32

Cocitika

Muzimvela Anthu Onse Cifundo

Tsiku lina mlongo wina wa ku New Zealand anaonelela vidiyo yakuti “Khalani Omvelana Cifundo,” imene imafotokoza cifundo ca Yehova na mmene amacionetsela. (Yes. 63:​7-9) Iye anasankha kuseŵenzetsa zimene anaphunzila mwa kupeleka thandizo kwa ena. Tsiku limenelo pomwe anali kugula zinthu anakumana na mayi wina yemwe analibe pokhala. Iye anauza mayiyo kuti akufuna kumugulila cakudya. Mayiyo anavomela. Pamene mlongoyo anapeleka cakudya kwa mayiyo, iye anacita ulaliki wacidule poseŵenzetsa kathilakiti kakuti Kodi Mavuto Adzathadi?

Mayiyo anayamba kulila. Anafotokoza kuti anakulila m’banja la Mboni, koma anasankha kusiya coonadi zaka zambili m’mbuyomo. Koma caposacedwa anali kupemphela kwa Yehova kuti am’thandize kubwelelanso kwa iye. Mlongoyo anapatsa mayiyo Baibo, ndipo anapanga makonzedwe akuti ayambe kuphunzila naye.a

Tingaonetse ena cifundo mmene Yehova amacitila. Tingatelo kwa acibale athu, komanso abale na alongo athu mumpingo. Tingaonetsenso cifundo mwa kuyesetsa kupeza mipata yolalikila kwa ena.

a  Kuti mudziŵe mmene mungathandizile ozilala, onani nkhani yakuti “Bwelelani Kwa Ine” mu Nsanja ya Mlonda ya June 2020.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani