LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 May tsa. 32
  • Kupilila Zopanda Cilungamo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kupilila Zopanda Cilungamo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Nkhani Zofanana
  • “Woweluza wa Dziko Lonse” Amacita Cilungamo Nthawi Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Yehova Akukuthandizani Kupambana Mayeso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • ‘Tamvelani Maloto Awa’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 May tsa. 32

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU

Kupilila Zopanda Cilungamo

Ŵelengani Genesis 37:​23-28; 39:​17-23 kuti muphunzile ku citsanzo ca Yosefe ca kupilila zopanda cilungamo.

Mvetsani nkhani yonse. N’ciyani cinacititsa ena kucitila Yosefe zopanda cilungamo? (Gen. 37:​3-11; 39:​1, 6-10) Kodi Yosefe anapilila zinthu zopanda cilungamo kwa utali wotani? (Gen. 37:2; 41:46) Kodi Yehova anamucitila ciyani Yosefe pa nthawiyo? Nanga sanamucitile ciyani?—Gen. 39:​2, 21; w23.01 17 ¶13.

Kumbani mozamilapo. Baibo sinachulepo kuti Yosefe anayesa kudziteteza ku zinenezo zabodza za mkazi wa Potifara. Kodi Malemba otsatilawa angatithandize bwanji kudziŵa cifukwa cimene Yosefe anakhalila cete, kapena cifukwa cake sitiyenela kuyembekezela kuuzidwa mfundo zonse? (Miy. 20:2; Yoh. 21:25; Mac. 21:37) Ni makhalidwe ati amene ayenela kuti anathandiza Yosefe kupilila zopanda cilungamo?—Mika 7:7; Luka 14:11; Yak. 1:​2, 3.

Onani zimene muphunzilapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Ni zopanda cilungamo zotani zimene ningakumane nazo pokhala wophunzila wa Yesu?’(Luka 21:​12, 16, 17; Aheb. 10:​33, 34)

  • ‘Kodi ningakonzekele bwanji kupilila zopanda cilungamo?’ (Sal. 62:​7, 8; 105:​17-19; w19.07 2-7)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani