LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 October tsa. 31
  • Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mukukumbukila?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 October tsa. 31
Cithunzi ca kacisi wa Solomo.

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi khonde la kacisi wa Solomo linali lalitali motani?

Khonde linali malo amene anthu anali kudutsa poloŵa ku Malo Oyela a pakacisi. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika limene linapulintidwa cisanafike caka ca 2023, limanena kuti “khonde lakutsogolo linali mikono 20 m’litali, ndipo linkafanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo, kucoka pansi kufika pamwamba khondelo linali lalitali 120.” (2 Mbiri 3:4) Ma Baibo ena anamasulilanso kuti khonde limeneli linali lalitali “mikono 120,” zimene zionetsa kuti inali nsanja ya mamita 53.

Komabe, Baibulo la Dziko Latsopano la Cingelezi limene linapulintidwa mu 2023, linanena izi pofotokoza za khonde la kacisi wa Solomo: “Kucoka pansi kufika pamwamba khondelo linali lalitali mikono 20,” kapena kuti nsanja ya mamita 9.a Tiyeni tioneko zina mwa zifukwa zimene zinapangitsa kuti pakhale masinthidwe amenewo.

Kutalika kwa khondelo sikunachulidwe pa 1 Mafumu 6:3. Polemba vesi limeneli, Yeremiya anachula m’litali mwa khonde limenelo, komanso kuzama kwake, koma sanachule kutalika kwake. Kenako, iye m’mavesi otsatila anafotokoza momveka bwino zinthu zina zomwe zinali pabwalo la kacisi, kuphatikizapo thanki yosungilamo madzi, zotapilamo madzi zokwanila 10, komanso zipilala ziŵili zakopa zomwe zinaikidwa kunja pafupi na khondelo. (1 Maf. 7:​15-37) Ngati khondelo linali lalitali kuposa kacisi yense, n’cifukwa ciyani Yeremiya sanachule kutalika kwake? Ngakhale pambuyo pa zaka zambili, olemba aciyuda sananene kuti khonde linali lalitali kuposa kacisi yense wa Solomo.

Akatswili amakaikila ngati zipupa za kacisi zikanatha kukhala na khonde lalitali mikono 120. Zimango zazitali zamiyala komanso zanchelwa za m’nthawi yakale, monga mageti a kacisi wa ku Iguputo, zinali kukhala na tsinde lalikulu pansi pake ndipo zinali kupita n’zicepa kumwamba. Koma kacisi wa Solomo anamangidwa mosiyanako. Akatswili amanena kuti kucindikala (mtiga) kwa zipupa za kacisi sikunali kupitilila mamita 2.7 (mikono 6). Katswili wolemba mbili yakale wa zomangamanga Theodor Busink ananena kuti: “Malinga na kucindikala kwa zipupa za khomo loloŵela m’kacisi, khondelo silikanakhala lalitali mikono 120.”

N’kutheka kuti mawu a pa 2 Mbiri 3:4 anawakopela molakwika. Zolemba zina zakale pa vesili zimanena kuti “mikono 120.” Komabe zolemba zina zakale, monga Baibo ya Alexandrinus ya m’zaka za m’ma 400 C.E, komanso ya Ambrosianus ya m’zaka za m’ma 500 C.E, zimanena kuti “mikono 20.” N’ciyani cikanapangitsa okopela Malemba kuphonyetsa na kulemba “120”? Mu Ciheberi, mawu otanthauza “handiledi” amaoneka ofanana na mawu otanthauza “mikono”. Conco n’kutheka kuti okopelawo analemba mawu akuti “handiledi” m’malo molemba mawu akuti “mikono.”

Pamene tikuyesetsa kumvetsa bwino zinthu zimenezi, komanso kujambula molondola kacisi wa Solomo, cofunika kwambili kwa ife ni zimene kacisiyo anaimila, zomwe ni kacisi wamkulu wauzimu. Ndife oyamikila kwambili kuti Yehova waitana atumiki ake onse kuti adzamulambile pa kacisi ameneyu!—Aheb. 9:​11-14; Chiv. 3:12; 7:​9-17.

a Mawu a m’munsi a pa lembali amati “zolemba zina zakale zimati ‘120,’ pomwe zolemba zinanso zakale komanso ma Baibo ena amati ‘mikono 20.’”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani