Pa Nkhondo Pamacitika Zinthu Zoipa Kwambili
Nkhondo ndi cimodzi mwa zinthu zimene zimabweletsa mavuto aakulu kwa anthu. Asilikali komanso anthu amene anakhalako kumalo kumene kunali nkhondo amawadziwa bwino mavuto amenewa.
ZIMENE ASILIKALI ANAKAMBA
“Nthawi zonse umaona anthu akuphedwa kapena kuvulazidwa koopsa. Nthawi zonse umaona kuti ndiwe wosatetezeka.”—Gary, wa ku Britain.
“Ndinaombeledwa kumsana ndi kumaso, ndipo n’nali kuona anthu ambili akuphedwa, kuphatikizapo ana komanso okalamba. Nkhondo imakupangitsa kukhala wouma mtima.”—Wilmar, wa ku Colombia.
“Munthu wina akaombeledwa ukuona, sumaiwala zocitikazo. Nthawi zonse m’maganizo umakhala ukumuona komanso kumumva akulila. Sumamuiwala munthuyo ngakhale pang’ono.”—Zafirah, wa ku United States.
ZIMENE ANTHU ENA ANAKAMBA
“N’nali kuona kuti n’zosatheka kukhalanso wacimwemwe. Umakhala ndi nkhawa yakuti udzaphedwa. Koma umakhalanso ndi nkhawa yaikulu yakuti a m’banja lako komanso anzako adzaphedwa.”—Oleksandra, wa ku Ukraine.
“Tinali kukhala ndi mantha tikaimilila pa mzele wolandila cakudya kucokela ca m’ma 02:00 kukafika ca m’ma 23:00, cifukwa tinali kudziwa kuti nthawi ina iliyonse tikhoza kuombeledwa.”—Daler, wa ku Tajikistan.
“Makolo anga anaphedwa pa nkhondo. N’nakhala wamasiye, ndipo n’nalibe aliyense wonditonthoza kapena wondisamalila.”—Marie, wa ku Rwanda.
Ngakhale kuti anthuwa anakumana ndi mavuto cifukwa ca nkhondo, iwo tsopano ali ndi mtendele wa mumtima. Ndipo ndi otsimikiza kuti nkhondo zonse zidzatha posacedwa. Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda idzagwilitsa nchito Baibo pofotokoza mmene zimenezi zidzacitikila