MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU
Phunzilani Zambili pa Zithunzi
Zofalitsa zathu n’zodzala ndi zithunzi zophunzitsa mfundo zofunika. Kodi mungatani kuti muzipindula nazo kwambili?
Musanayambe kuwelenga nkhani inayake, muziyamba mwaona zithunzi zake. Zithunzizo zingakukopeni cidwi ndipo zingakusonkhezeleni kuti muwelenge nkhaniyo. Monga mmene zilili ndi cakudya copatsa mudyo, maso ndiwo “amalawa” coyamba. Conco dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikuona ciyani?’—Amosi 7:7, 8.
Powelenga nkhani, ganizilani cifukwa cake cithunzico anaciikamo. Welengani mawu a pa zithunzi kapena mawu ofotokozela zithunzi ngati alipo. Ganizilani mmene zithunzizo zikugwilizanilana ndi nkhani imene mukuwelenga komanso zimene muphunzilapo.
Mukamaliza kuwelenga, gwilitsani nchito zithunzi pobweleza mfundo zikuluzikulu za nkhaniyo. Tsekani maso anu n’kukumbukila zithunzizo m’maganizo mwanu ndipo onani zimene cithunzi ciliconse cakuphunzitsani.
Bwanji osaonanso zithunzi zili m’magazini ino kuti muone ngati mukukumbukila zimene mukuphunzilapo?