MBILI YANGA
Mlangizi Wathu Wamkulu Watiphunzitsa kwa Moyo Wathu Wonse
ASILIKALI pa malodibuloko, zochinga njila zoyaka moto, anamondwe, nkhondo zapaciweniweni, komanso kusamukasamuka. Izi ndi zina mwa zoopsa zimene ine ndi mkazi wanga tinakumana nazo tikucita upainiya komanso umishonale. Ngakhale n’telo, sitinong’oneza bondo cifukwa ca umoyo umene tinasankha! Pa zonse zimene takumana nazo, Yehova waticilikiza ndi kutidalitsa. Pokhala Mlangizi wathu Wamkulu, watiphunzitsa zinthu zambili zofunika.—Yobu 36:22; Yes. 30:20.
CITSANZO CA MAKOLO ANGA
Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1950, makolo anga anasamuka ku Italy ndi kupita ku tauni ya Kindersley, mu mzinda wa Saskatchewan, ku dziko la Canada. Posapita nthawi, anaphunzila coonadi ndipo cinakhala cofunika kwambili pa umoyo wathu. Ndikumbukila kuti ndili mwana n’nali kuthela nthawi yoculuka mu utumiki ndi a m’banja lathu. Conco, nthawi zina ndimakamba moseka kuti ndinacitako upainiya wothandiza ndili ndi zaka 8.
Ndili ndi banja lathu mu 1966
Makolo anga anali osauka. Komabe, anatipatsa citsanzo cabwino pa nkhani yodzimana potumikila Yehova. Mwacitsanzo, mu 1963 iwo anagulitsa katundu wawo wambili kuti apeze ndalama zopitila ku msonkhano wa maiko umene unacitikila ku mzinda wa Pasadena, ku California, m’dziko la America. Mu 1972, tinayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 1,000 kupita ku mzinda wa Trail, mu pulovinsi ya British Columbia, m’dziko la Canada, kuti tikalalikile anthu olankhula ci ltalian. Atate anali kugwila nchito yoyeletsa komanso yokonza zinthu m’sitolo. Anali kukana kukwezedwa pa nchito n’colinga cakuti aike maganizo awo pa zinthu zauzimu.
Ndiyamikila kwambili kuti makolo anga anatisiyila citsanzo cabwino ife ana awo anayi. Citsanzo cawo ndiye cinali ciyambi ca kuphunzitsidwa kwanga ndi Yehova. Cimodzi cimene n’naphunzila kwa iwo pa umoyo wanga wonse n’cakuti: Ndikafuna Ufumu coyamba, Yehova adzandisamalila.—Mat. 6:33.
KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
Mu 1980, n’nakwatila Debbie, mlongo wokongola amene maganizo ake onse anali pa kutumikila Yehova. Tinali kufuna kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Conco, Debbie anayamba upainiya patapita miyezi itatu titakwatilana. Patapita caka cimodzi titalowa m’banja, tinasamukila mu mpingo waung’ono umene unali wosowa, ndipo nanenso n’nayamba upainiya.
Pa tsiku la cikwati cathu mu 1980
M’kupita kwa nthawi, sitinalinso osangalala ndi utumiki wathu. Conco, tinafuna kucokako kumaloko. Koma coyamba tinakambilana ndi woyang’anila dela. Iye mwacikondi koma mosapita mbali anatiuza kuti: “Inunso mukuwonjezela vuto limene lilipo. Mukuika maganizo anu pa zinthu zolefula. Koma mukayesetsa kuika maganizo anu pa zinthu zabwino, mudzazipeza.” Uphungu umenewo unalidi wa pa nthawi yake. (Sal. 141:5) Nthawi yomweyo tinayamba kuugwilitsa nchito ndipo tinazindikila kuti panali zinthu zabwino zimene sitinali kuona. Ena mu mpingo anali kufuna kucita zoculuka potumikila Yehova kuphatikizapo acinyamata komanso ena amene anali ndi mnzawo wa mu ukwati wosakhulupilila. Izi zinatiphunzitsa mfundo yofunika kwambili. Tinaphunzila kuika maganizo athu pa zinthu zabwino ndi kuyembekezela Yehova kuti akonze zinthu zimene zikuoneka zovuta. (Mika 7:7) Tinapezanso cimwemwe, ndipo zinthu zinasinthila kwabwino.
Alangizi a sukulu yathu yoyamba ya upainiya anatumikilapo m’maiko osiyanasiyana. Pamene anali kutionetsa zithunzi ndi kutifotokozela mavuto amene anakumana nawo komanso madalitso amene anapeza, zinakulitsa cikhumbo cathu cofuna kutumikila monga amishonale. Conco, tinadziikila colinga cokakhala amishonale.
Tili pa Nyumba ya Ufumu ku British Columbia mu 1983
Kuti tikwanilitse colinga cimeneci, mu 1984, tinasamukila ku mzinda wa Quebec, m’dela limene anthu ambili amalankhula ci French. Delali lili pa mtunda wa makilomita oposa 4,000 kucokela m’cigawo ca British Columbia. Tinafunikila kuphunzila cikhalidwe ndi cilankhulo catsopano. Kuwonjezela pa zimenezi, nthawi zambili tinalibe ndalama zokwanila. Pa nthawi ina, tinapulumukila mbatatisi zimene tinakunkha m’munda wa munthu wina. Debbie anafika pokhala katswili wophika mbatatisi m’njila youtsa madyo. Ngakhale kuti panali zovuta zimenezi, tinayesetsa kupilila mwacimwemwe. Ndipo tinaonanso kuti Yehova anali kutisamalila.—Sal. 64:10.
Tsiku lina, tinalandila foni imene sitinali kuyembekezela. Uthenga wake unali wotiitana kuti tikatumikile ku Beteli ya ku Canada. Popeza tinali titafunsila kulowa sukulu ya Giliyadi, sitinakondwele kwenikweni ndi ciitano cimeneci. Koma tinapitabe. Titafika, tinafunsa M’bale Kenneth Little wa m’Komiti ya Nthambi kuti: “Nanga bwanji za Sukulu ya Giliyadi imene tinafunsila?” Iye anayankha kuti, “Mtima m’malo, ciliconse cili ndi nthawi.”
Patangopita mlungu umodzi, tinaonadi kuti ciliconse cili ndi nthawi yake, cifukwa ine ndi Debbie tinaitanidwa kukalowa Sukulu ya Giliyadi. Conco tinafunika kusankha kaya kulowa Sukulu ya Giliyadi kapena kukhala pa Beteli. M’bale Little anatiuza kuti: “Mulimonse mmene mungasankhile, tsiku lina mudzaganizabe kuti mukanacita bwino mukanasankha utumiki winawo. Koma palibe utumiki woposa unzake. Yehova amadalitsa uliwonse.” Tinasankha kupita ku Giliyadi, ndipo kwa zaka taona kuti M’bale Little anakambadi zoona. Ndipo nthawi zambili, uphungu wake tinali kulimbikitsa nawo ena amene anafunikila kusankha kuti ndi utumiki uti umene adzacita.
UTUMIKI WA UMISHONALE
(Kumanzele) Ulysses Glass
(Kulamanja) Jack Redford
Zinali zosangalatsa kulowa nawo kalasi ya nambala 83 ya sukulu ya Giliyadi. M’kalasimo tinalimo ophunzila 24. Zimenezi zinacitika mu April 1987, mu mzinda wa Brooklyn ku New York. M’bale Ulysses Glass ndi M’bale Jack Redford, ndiwo anali kutiphunzitsa kawilikawili. Miyezi 5 yocita maphunzilowa inadutsa mofulumila. Ndipo tinakhala ndi mwambo wa omaliza maphunzilo pa September 6, 1987. Tinatumizidwa kuti tikatumikile ku Haiti limodzi ndi M’bale John ndi mkazi wake Marie Goode.
Tili ku Haiti mu 1988
Amishonale otsala m’dzikolo anathamangitsidwa mu 1962. Conco, kucokela pa nthawiyo, ndife tinali oyamba kulowa m’dzikolo monga amishonale. Pambuyo pa milungu itatu titacoka ku Giliyadi, tinapita kukatumikila mu mpingo waung’ono wa ofalitsa 35 ku Haiti womwe unali kutali kwambili ku mapili. Tinali acinyamata komanso osadziwa zambili. Ndipo tinali kukhala tokhatokha m’nyumba ya amishonale. Anthu a kumeneko anali osauka kwambili, ndipo ambili anali osadziwa kuwelenga. Pa nthawiyo, anthu a m’dzikolo anali kucita zipolowe, kufuna kulanda boma, komanso kucita zionetselo zoonetsa kusakondwa. Ndipo kunali kucitikanso anamondwe.
Tinaphunzila zambili kwa abale ndi alongo a ku Haiti amene anapilila zinthu zimenezo mwacimwemwe. Ambili anali ndi umoyo wovutikila koma anali kukonda Yehova ndi utumiki. Mwacitsanzo, panali mlongo wina wacikulile amene sanali kudziwa kuwelenga koma analoweza malemba 150 pamtima. Zocitika za tsiku lililonse zinali kutilimbikitsa kulalikila uthenga wa Ufumu womwe ndiwo mankhwala okha pa mavuto a mtundu wa anthu. Zimatilimbikitsa kwambili kuona ena mwa anthu omwe tinali kuwaphunzitsa Baibo akutumikila monga apainiya a nthawi zonse, apainiya apadela, komanso akulu.
Tili ku Haiti, n’nakumana ndi mnyamata wina dzina lake Trevor, wa cipembedzo ca Mormon. Ndipo tinakambilana nkhani za m’Baibo maulendo angapo. Patapita zaka, n’nalandila kalata kucokela kwa iye. Ndipo n’nadabwa ndi zimene ananiuza. Iye anati, “Ndidzabatizika pa msonkhano wa dela umene ukubwela. Pambuyo pake, ndidzabwelela ku Haiti kukatumikila monga mpainiya wapadela m’dela limodzimodzi limene n’nali kutumikila monga mmishonale wa ci Mormon. Iye anatumikiladi monga mpainiya wapadela kwa zaka zambili limodzi ndi mkazi wake.
TINAPITA KU EUROPE KENAKO KU AFRICA
Ndikugwila nchito ku Slovenia mu 1994
Tinatumizidwa kukatumikila ku Europe, kumadela kumene ziletso pa nchito ya Ufumu zinayamba kucotsedwa. Mu 1992, tinafika mu mzinda wa Ljubljana ku Slovenia kufupi ndi kumene makolo anga anakulila asanapite ku Italy. Nkhondo inali kucitikabe m’madela amene kale anali kupanga dziko la Yugoslavia. Ofesi ya nthambi ya mu mzinda wa Vienna ku Austria, komanso maofesi a mu mzinda wa Zagreb ku Croatia, ndi mu mzinda wa Belgrade ku Serbia, ndiwo anali kuyang’anila nchito yathu ku cigawoco. Apa tsopano dziko lililonse limene kale linali kupanga dziko la Yugoslavia, linafunika kukhala ndi ofesi yake ya nthambi.
Izi zinatanthauza kuti tinafunika kuphunzilanso cinenelo ndi cikhalidwe cina. Nthawi zambili anthu a kumeneko anali kunena kuti cilankhulo cawo cinali covuta. Ndipo n’zoona cinalidi covuta. Tinali kunyadila kuona abale ndi alongo okhulupilika amene anali okonzeka kutsatila masinthidwe a gulu. Ndipo tinaona mmene Yehova anawadalitsila. Tinaonanso mmene Yehova nthawi zonse anali kuwongolela zinthu mwacikondi, ndipo anali kucita zimenezo pa nthawi yake. Tinaphunzila zinthu zambili ku Slovenia. Ndipo zoculuka zimene tinaphunzila tisanapite kumeneko zinatithandiza kupilila mavuto amene tinakumana nawo kumeneko.
Koma zinthu zinali kudzasinthanso. Mu 2000, tinatumizidwa kuti tikatumikile ku West Africa, m’dziko la Côte d’Ivoire. Cifukwa ca nkhondo ya paciweniweni, mu November 2002, anatisamutsila ku Sierra Leone. Apa n’kuti nkhondo ya paciweniweni yomwe inatenga zaka 11 yangotha kumene m’dzikolo. Zinali zovuta kucoka ku Côte d’Ivoire mwadzidzidzi conco. Koma zimene tinaphunzila kumbuyoko zinatithandiza kukhalabe acimwemwe.
Tinaika maganizo athu pa mmene nchito yolalikila inali kupitila patsogolo komanso pa abale na alongo athu acikondi amene anali atapilila nkhondo kwa zaka zambili. Iwo anali osauka ku thupi koma anali kugawana ndi ena zimene anali nazo. Mwacitsanzo, mlongo wina anapatsa Debbie zovala. Debbie atazengeleza kulandila zovalazo, mlongoyo anamukakamiza ndipo anati: “Abale ndi alongo m’madela ena anatithandiza pa nthawi ya nkhondo. Conco ndi nthawi yathu nafenso yoti tithandize ena.” Tinacipanga kukhala colinga cathu kutengela citsanzo cawo.
Patapita nthawi tinabwelela ku Côte d’Ivoire, ndipo cifukwa ca mavuto a zandale, zacipolowe zinayambilanso. Conco mu November 2004, anatisamutsa ndi helikopitala. Pocoka, aliyense anangonyamula cola ca katundu wolemela makilogilamu 10 basi. Usiku wa tsiku limenelo tinagona pansi penipeni m’bwalo la asilikali a ku France m’dzikolo, ndipo tsiku lotsatila tinakwela ndeke kupita ku Switzerland. Tinafika ku ofesi ya nthambi capakati pa usiku. Komiti ya Nthambi, komanso alangizi a Sukulu ya Utumiki limodzi ndi akazi awo anatilandila ndi manja awili. Anatikumbatila, kutipatsa cakudya camoto komanso chokoleti wa ku Switzerland. Izi zinatikhudza mtima kwambili.
Ndikulankhula ndi anthu othawa kwawo ku Côte d’Ivoire mu 2005
Anatitumiza kukatumikila ku Ghana kwa kanthawi, kenako anatitumizanso kukatumikila ku Côte d’Ivoire cipolowe citacepako. Kukoma mtima kwa abale kunatithandiza kupilila zovuta zimene tinakumana nazo posamukasamuka, komanso pocita mautumiki apakanthawi amenewa. Ine ndi Debbie tinagwilizana kuti ngakhale kuti khalidwe la cikondi ndi lofala m’gulu la Yehova, sitidzasiya kulinyadila. Ndipo masautso amene tinakumana nawo anatiphunzitsa zinthu zofunika kwambili.
KUPITA KU MIDDLE EAST
Tili ku Middle East mu 2007
Mu 2006, tinalandila kalata yocokela ku likulu lathu lotiuza za utumiki wathu watsopano ku Middle East. Izi zinatanthauza kuti tinafunikanso kupita ku malo atsopano, kukumana ndi mavuto ena, kuphunzila zilankhulo komanso zikhalidwe zatsopano. Kudela limeneli kunali mavuto ambili cifukwa ca zandale komanso zacipembedzo. Ngakhale kuti m’mipingo munali anthu olankhula zinenelo zosiyanasiyana, tinaona kuti anthuwo anali ogwilizana cifukwa cotsatila malangizo a gulu la Yehova. Tinali kuwanyadila ngako abale ndi alongo a kumeneko cifukwa ambili a iwo anali kuzipilila molimba mtima zitsutso zocokela kwa a m’banja lawo, anzawo a ku nchito, anzawo a ku sukulu, ndi maneba awo.
Mu 2012, tinapezeka pa msonkhano wa cigawo wapadela womwe unacitikila mu mzinda wa Tel Aviv, ku Israel. Aka kanali koyamba m’cigawo cimeneci anthu a Yehova kusonkhana ambili conci kucokela pa Pentekosite mu 33 C.E. Cinali cocitika cosaiwalika!
M’zaka zimenezo tinatumizidwa kukayendela dziko kumene nchito yathu inali yoletsedwa. Popita kumeneko tinanyamula zofalitsa zathu. Titafika, tinapita nawo mu utumiki abale ndi kucita nawo misonkhano yadela ing’onoing’ono. Asilikali azida komanso malodibuloko anali paliponse, koma tinali kumva kuti ndife otetezeka cifukwa tinali kuyenda mosamala ndi abale ocepa a kumaloko.
KUBWELELA KU AFRICA
Ndikukonzekela nkhani mu 2014 ku Congo
Mu 2013, tinalandila utumiki wosiyana kwambili ndi mautumiki ena omwe tinacitako. Tinauzidwa kukatumikila pa ofesi ya nthambi ya ku Congo mu mzinda wa Kinshasa. Dzikoli n’lodzala ndi zinthu zokongola zacilengedwe. Koma lakhala pa umphawi wadzaoneni ndipo mwakhala mukucitika nkhondo zambili. Titalandila utumikiwu tinati, “Ku Africa tidziwako bwino, ndife okonzeka.” Koma panali pakali zambili zofunika kuphunzila, monga kuyenda maulendo m’madela opanda misewu ndi maulalo. Koma panali zinthu zambili zocititsa cidwi, monga kuona abale ndi alongo athu akupilila mwacimwemwe ngakhale kuti anali ndi mavuto a zacuma, kukonda kwawo ulaliki, komanso khama limene anali kuonetsa kuti akapezeke pa misonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikuluikulu. Tinadzionela tokha mmene Yehova anathandizila nchito ya Ufumu ndi kuidalitsa kuti ipite patsogolo. Sitidzaiwala zinthu zambili zimene tinaphunzila pocita utumiki wa nthawi zonse ku Congo. Utumiki wathu kumeneko unatithandizanso kuwonjezela mabwenzi athu.
Tikugwila nchito yolalikila ku South Africa mu 2023
Cakumapeto kwa 2017, tinalandilanso utumiki wina watsopano. Tinatumizidwa ku South Africa. Ofesi ya nthambi ya ku South Africa ndiyo inali yaikulu kwambili pa maofesi onse a nthambi amene tinatumikilapo. Ndipo nchito zimene tinapatsidwa kumeneko tinali tisanazigwilepo. Apanso tinafunika kuphunzila zinthu zambili zatsopano, koma zimene tinaphunzila kumbuyoku zinatithandiza. Timawakonda kwambili abale ndi alongo amene akhala akupilila mokhulupilika kwa zaka zambili. Ndipo n’zocititsa cidwi kuona banja la Beteli likugwilila nchito limodzi mogwilizana ngakhale kuti anthu ake amasiyana mitundu ndi zikhalidwe. Umboni wakuti Yehova akudalitsa anthu ake ndi kuwapatsa mtendele ukuonekela bwino pomwe abale ndi alongo akuvala umunthu watsopano ndi kugwilitsa nchito mfundo za m’Baibo.
Kwa zaka, ine ndi Debbie talandilapo mautumiki osangalatsa ndipo taphunzila zikhalidwe ndi zinenelo zosiyanasiyana. Koma izi sizinali zofewa nthawi zonse. Koma taona cikondi ca Yehova kudzela mwa abale ndi alongo komanso m’gulu lake. (Sal. 144:2) Tikuona kuti zimene taphunzila mu utumiki wathu wa nthawi zonse zatithandiza kukhala atumiki a Yehova ocita bwino kwambili.
Ndiyamikila kwambili zimene makolo anga anandiphunzitsa, thandizo la mkazi wanga wokondeka, Debbie, komanso zitsanzo zabwino kwambili za banja lathu lauzimu la padziko lonse. Pamene ine ndi mkazi wanga tikuganizila za tsogolo lathu, ndife otsimikiza mtima kupitiliza kuphunzila zinthu zatsopano zimene Mlangizi wathu wamkulu angatiphunzitse.