LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 July masa. 26-30
  • “Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUUMBIDWA NDI AMISHONALE OKANGALIKA
  • KUKATUMIKILA KU LIKULU LA PADZIKO LONSE
  • UTUMIKI WANGA M’DIPATIMENTI YA ZAMALAMULO
  • KUTETEZA NDI KUKHAZIKITSA MWALAMULO NCHITO YOLENGEZA UTHENGA WABWINO
  • ZIKOMO YEHOVA!
  • Kumenyela Ufulu wa Kulambila
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kucilikiza Boma la Mulungu Mokhulupilika
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kuteteza Ufulu wa Kulambila Pakati pa Anthu Otsatila Cikhalidwe ca Makolo
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 July masa. 26-30
Philip Brumley.

MBILI YANGA

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

YOSIMBIDWA NDI PHILIP BRUMLEY

PA JANUARY 28, 2010, n’nali mu mzinda wokongola wa Strasbourg, ku France, ndipo linali tsiku lozizila kwambili. Sin’napite kumeneko monga mlendo wokaona malo ayi. Koma ndinali pakagulu kamene kanatumizidwa kukateteza ufulu wa Mboni za Yehova ku khoti ya European Court of Human Rights (ECHR). Nkhani yake inali yofuna kuona ngati boma la France linacita cilungamo polamula kuti abale athu apeleke msonkho wokwela kwambili wa ndalama zokwanila madola 89,000,000 a ku America. Koma codetsa nkhawa kwambili n’cakuti izi zinakhudza dzina la Yehova, komanso zinaika pa ciopsezo mbili ya anthu ake ndi ufulu wawo wa kulambila. Zimene zinacitika pa tsikulo zinatsimikiziladi kuti “Yehova ndiye mwini nkhondo.” (1 Sam. 17:47) Lekani ndikusimbileni.

Nkhaniyi inayamba mu 1999, pomwe boma la France mopanda cilungamo linafuna kukhometsa msonkho pa ndalama zimene zinapelekedwa mwaufulu ku ofesi ya nthambi ya dzikolo kuyambila mu 1993 mpaka mu 1996. Tinatengela nkhaniyi ku makhoti, koma sizinaphule kanthu. Titaluza mlanduwu ku khoti ya apilo, boma linalanda ndalama zomwe zinali mu akaunti ya banki ya ofesi ya nthambi ya ku France zopitilila madola 6,300,000 a ku America. Boma likanabweza ndalamazo kokha tikanapeleka nkhaniyo ku khoti ya European Court of Human Rights (ECHR). Koma khotiyo isanamvetsele mlandu wathu, inakamba kuti tikumane ndi loya wa boma la France limodzi ndi woimilako khotiyo kuti aone ngati zinali zotheka kuthetsa mlanduwo usanapite kukaweluzidwa m’khoti.

Tinali kuganiza kuti woimilako khotiyo adzatinyengelela kuti tipeleke ndalama yaing’ono pa ndalama zimene boma linali kufuna kuti nkhaniyo ithe. Koma tinali kudziwa bwino lomwe kuti kulipilako ngakhale 1 ngwee, kunali kosemphana ndi mfundo za m’Baibo. Abale ndi alongo anacita zopeleka zawo kuti acilikize nchito ya Ufumu. Conco ndalamazo sizinali za boma ayi. (Mat. 22:21) Koma pofuna kulemekeza ndondomeko ya khotiyo tinapitabe.

Gulu lathu la zamalamulo patsogolo pa khoti ya ECHR mu 2010

Conco tinakumana m’cipinda ca pambali cokongola ca khotiyo kuti tikambilane. Makambilano athu sanayambe bwino. Woimilako khotiyo ananena kuti anali kuyembekezela kuti Mboni za Yehova zipelekako zina pa ndalama za msonkho zimene boma la France linali kufuna. Kenako mzimu wa Yehova unatipangitsa kufunsa mzimayiyo kuti: “Kodi mukudziwa kuti boma la France lalanda kale ndalama zopitilila madola 6,300,000 a ku America, omwe anali mu akaunti yathu?”

Iye anangocita kakasi. Woimilako boma anavomela kuti anatengadi ndalamazo. Izi zinasinthilatu mmene mzimayiyo anali kuonela nkhaniyi. Iye anawadzudzula mwamphamvu ndi kuithetsa miting’iyo. Ndinazindikila kuti Yehova ndiye analowelelapo kuti tipambane mlanduwo m’njila imene sitinayembekezele. Tinacoka pa miting’iyo tili osangalala komanso tili odabwa ndi zimene zinacitika.

Pa June 30, 2011, oweluza onse a khoti ya ECHR mogwilizana anapeleka cigamulo cotikomela. Anagamula kuti tisapeleke msonkho pa ndalamazo, ndipo anagamulanso kuti boma litibwezele ndalama zathu ndi kuikapo ndapusa. Cigamulo cosaiwalika cimeneci cateteza kulambila koyela ku France mpaka pano. Funso limene tinafunsa mosakonzekela lija, linali ngati mwala umene unaboola mphumi ya Goliyati ndipo linasinthilatu nkhani yonse. N’ciyani cinacititsa kuti tipambane? Yankho lili m’mawu amene Davide anauza Goliyati akuti: “Yehova ndiye mwini nkhondo.”​—1 Sam. 17:​45-47.

Koma iyi si nthawi yokhayo pomwe tinapambana mlandu. Ngakhale kuti maboma amphamvu komanso zipembedzo zakhala zikutitsutsa, tapambanapo milandu yokwana 1,225 m’makhoti akuluakulu m’maiko 70, komanso m’makhoti aakulu a padziko lonse. Kupambana milandu imeneyi kwateteza ufulu wathu. Maufulu amenewa aphatikizapo ufulu wodziwika kuti ndife cipembedzo cokhazikitsidwa mwalamulo, ufulu wolalikila, ufulu wokana kutengako mbali m’miyambo ya dziko, komanso ufulu wokana kuikidwa magazi.

Koma n’cifukwa ciyani n’nali kuthandiza pa mlandu wa ku Europe ngakhale kuti ndinali kutumikila ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova ku New York, ku America?

KUUMBIDWA NDI AMISHONALE OKANGALIKA

Makolo anga, a George ndi a Lucille, analowa kalasi ya nambala 12 ya Giliyadi. Iwo anali kutumikila ku Ethiopia, komwe ndinabadwila mu 1956. Anandipatsa dzina lakuti Philip, lomwe linali la mlaliki wa m’zaka za zana loyamba. (Mac. 21:8) Caka cotsatila, boma linaletsa nchito yathu. Ngakhale ndinali mwana, ndikumbukila bwinobwino kuti banja lathu linali kulalikila komanso kusonkhana mwakabisila. Popeza ndinali mwana, ndinali kuona kuti zinali zosangalatsa! N’zacisoni kuti mu 1960, boma linatikakamiza kuti ticoke m’dzikolo.

M’bale Nathan H. Knorr (kumanzele kwambili) akucezela banja lathu ku Addis Ababa, Ethiopia, mu 1959

Banja lathu litasamukila mu mzinda wa Wichita, m’cigawo ca Kansas, ku America, makolo anga anapitiliza kucita utumiki waumishonale mokangalika. Iwo anali kucikonda kwambili coonadi, ndipo anali kutumikila mokangalika. Anaphunzitsanso ife ana awo atatu, ine, mlongosi wanga Judy, ndi mng’ono wanga Leslie kukonda Yehova ndi kum’tumikila ndi mtima wonse. Ana tonsefe tinabadwila ku Ethiopia. Ndinabatizika ndili ndi zaka 13. Patapita zaka zitatu, banja lathu linapita kukatumikila ku malo osowa mu mzinda wa Arequipa, ku Peru.

Mu 1974, ndili ndi zaka 18, ofesi ya nthambi ya ku Peru inatumiza ine ndi abale ena 4 kukatumikila monga apainiya apadela. Tinali kupita kukalalikila ku magawo amene sanalalikidwepo, kudela la mapili a Andes Mountains. Izi zinaphatikizapo kulalikila anthu olankhula ci Quechua ndi ci Aymara. Tinali kuyendela m’galimoto yomwe inakhalanso nyumba yathu. Tinaipatsa dzina lakuti Cingalawa ca Nowa cifukwa ca mmene inali kuonekela. Ndimasangalala ndikakumbukila nthawi pamene tinali kugwilitsa nchito Baibo poonetsa anthu a kumeneko kuti Yehova posacedwa adzacotsapo umphawi, matenda, ndi imfa. (Chiv. 21:​3, 4) Ndipo ambili anayamba kulambila Yehova.

Galimoto yomwenso inali nyumba yathu ikudutsa pa madzi.

Galimoto yochedwa “Cingalawa ca Nowa” mu 1974

KUKATUMIKILA KU LIKULU LA PADZIKO LONSE

Mu 1977, M’bale Albert Schroeder, ciwalo ca Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova anaticezela ku Peru. Pa ulendowo, iye anandilimbikitsa kuti ndifunsile utumiki wa pa Beteli ku likulu la padziko lonse. Ndipo n’natelodi. Posakhalitsa, pa June 17, 1977, ndinayamba utumiki wanga pa Beteli ya ku Brooklyn. Kwa zaka 4 zotsatila, ndinatumikila m’dipatimenti yoyeletsa ndi kukonza zinthu.

Pa tsiku la ukwati wathu mu 1979

Mu June 1978, ndinakumana ndi Elizabeth Avallone, pa msonkhano wa maiko womwe unacitikila mu mzinda wa New Orleans, ku Louisiana. Nayenso analeledwa ndi makolo amene anali kucikonda coonadi. Iye anali atatumikila monga mpainiya wa nthawi zonse kwa zaka 4, ndipo anali kuukonda kwambili utumikiwo. Kucokela nthawiyo tinali kukambilana, ndipo posakhalitsa tinagwa m’cikondi. Tinakwatilana pa October 20, 1979, ndipo tonse tinayamba kutumikila pa Beteli.

Abale ndi alongo a mu mpingo wathu woyamba wa Brooklyn Spanish, anali acikondi kwambili. Pa zaka zonsezi, mipingo itatu imene tinasonkhanapo nayo, inatilandila bwino ndipo inaticilikiza pa utumiki wathu wa pa Beteli. Timayamikila kwambili thandizo lawo, thandizo la mabwenzi athu, komanso la acibale athu amene anatithandiza kusamalila makolo athu mu ukalamba wawo.

Philip ndi abale anzake a pa Beteli pa msonkhano wa mpingo

Abale a pa Beteli amene anali kusonkhana ndi mpingo wa Brooklyn Spanish mu 1986

UTUMIKI WANGA M’DIPATIMENTI YA ZAMALAMULO

N’nadabwa kuti mu January 1982, anandiuza kuti ndikatumikile m’Dipatimenti ya Zamalamulo ya pa Beteli. Patapita zaka zitatu, n’napemphedwa kuti ndipite ku sukulu ya zamalamulo kuti ndikakhale loya wovomelezeka. N’nadabwa kuphunzila kuti anthu ambili ku America komanso pa dziko lonse ali ndi ufulu wocita zinthu zambili cifukwa ca nkhani zimene Mboni za Yehova zinapambana m’makhoti. Zina mwa nkhani zikuluzikuluzi, tinaziphunzila mozamilapo m’kalasi.

Mu 1986, ndili ndi zaka 30, ndinaikidwa kukhala woyang’anila Dipatimenti ya Zamalamulo. Ndinasangalala kulandila utumikiwu. Koma popeza ndinali wamng’ono, ndinacita mantha cifukwa sin’nali kudziwa zambili.

Ndinakhala loya mu 1988, koma sin’nazindikile kuti sukuluyo inasokoneza ubale wanga ndi Yehova. Maphunzilo apamwamba angacititse munthu kuyamba kudzikweza ndi kumaganiza kuti popeza adziwa bwino nchito inayake, ndiye kuti ndi wapamwamba kuposa ena amene alibe maphunzilowo. Koma zosangalatsa n’zakuti Elizabeth anandithandiza. Anandithandiza kuti ndipitilize kutsatila pulogilamu yanga yocita zinthu zauzimu imene ndinali kucita n’sanapite ku sukulu. Zinanditengela nthawi koma pang’ono m’pang’ono ndinacila kuuzimu. Zimene zinandicitikilazi zinandiphunzitsa kuti kukhala ndi maphunzilo apamwamba sindiye cinthu cofunika kwambili pa umoyo. Zomwe zimapangitsa umoyo kukhala waphindu ndi kukhala pa ubale wathithithi ndi Yehova komanso kukhala ndi cikondi cacikulu pa iye ndi anthu ake.

KUTETEZA NDI KUKHAZIKITSA MWALAMULO NCHITO YOLENGEZA UTHENGA WABWINO

N’tamaliza kucita maphunzilo a zamalamulo, n’nayamba kuthandiza dipatimenti yathu kusamalila nkhani zokhudzana ndi malamulo pa Beteli, komanso kuthandiza gulu la Yehova kuti likhale ndi ufulu wolalikila uthenga wabwino. Kuthandiza gulu lathu limene linali kusintha ndi kukula mofulumila, kunali kosangalatsa komanso kovuta pa nthawi imodzimodzi. Mwacitsanzo, mu 1990, dipatimenti yathu inapemphedwa kutsogolela nchito yosintha zimene tinali kucita kwa nthawi yaitali zopempha anthu kuti azipeleka kenakake akafuna zofalitsa. Kucokela nthawi imeneyo, ife a Mboni za Yehova takhala tikugawila zofalitsa popanda kulipilitsa. Izi zinapeputsa nchito yathu pa Beteli komanso mu utumiki. Komanso zinathandiza kuti tipewe mavuto okhudzana ndi kulipila misonkho. Ena anaganiza kuti masinthidwewa adzacititsa kuti gulu lathu likhale lilibe ndalama komanso kuti nchito yolalikila idzalephela cifukwa cosowa zofalitsa. Koma si mmene zinakhalila. Kucoka mu 1990, ciwelengelo ca anthu amene akutumikila Yehova cawonjezeka kuposa kuwilikiza kawili. Ndipo masiku ano, anthu angapeze cakudya cauzimu copulumutsa moyo kwaulele. Ndadzionela ndekha kuti mphamvu zimene Yehova amapeleka komanso citsogozo cimene iye akupeleka kudzela mwa kapolo wokhulupilika, n’zimene zimapangitsa kuti masinthidwe monga awa, komanso masinthidwe ena amene gulu lapanga azikhaladi othandiza.​—Eks. 15:2; Mat. 24:45.

Kungokhala ndi maloya abwino si kumene kumapangitsa kuti tipambane mlandu kukhoti. Nthawi zambili, zimene zimasintha maganizo a olamulila, ndi khalidwe labwino la anthu a Yehova. N’naona citsanzo ca zimenezi mu 1998, pomwe abale atatu a m’Bungwe Lolamulila limodzi ndi azikazi awo anapezeka ku msonkhano wacigawo wapadela ku Cuba. Khalidwe lawo lokoma mtima komanso laulemu n’limene linacititsa akuluakulu a boma kukhulupilila kuti sitimatengela mbali m’zandale. Khalidwe lawo labwino ndi limene linacitila umboni kwambili kuposa zilizonse zimene tinakamba pokumana ndi olamulila pa mamiting’i.

Komabe, zikavuta kukambilana ndi akuluakulu a boma mwamtendele pa nkhani zokhudzana ndi malamulo, timapeleka nkhaniyo ku khoti kuti ‘tikateteze uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo nchito yolengeza uthenga wabwino.’ (Afil. 1:7) Mwacitsanzo, kwa zaka, ku Europe ndi ku South Korea, akuluakulu a boma anali kutiphela ufulu mwa kutikakamiza kuti tigwile nchito zokhudzana ndi usilikali. Cifukwa ca zimenezi, abale pafupifupi 18,000 ku Europe komanso oposa 19,000 ku South Korea, anaikidwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo pokana kugwilako nchito zokhudzana ndi usilikali.

Pa July 7, 2011, khoti ya ECHR inapeleka cigamulo cosaiwalika comwe cinachedwa Bayatyan v. Armenia. Cigamuloci cinapeleka ufulu wakuti munthu akhoza kugwilako nchito zina zosakhudzana ndi usilikali, ndipo cinakhudza maiko onse a ku Europe. Pa June 28, 2018, khoti yoona za malamulo ya Constitutional Court ya ku South Korea, inapeleka cigamulo cofanana ndi cimeneci. Kagulu kocepa cabe ka abale kakanalolela kugwilako nchito zokhudzana ndi usilikali, zigamulozi sizikanapelekedwa.

Dipatimenti yoona zamalamulo ku likulu lathu komanso madipatimenti a zamalamulo omwe ali m’maofesi a nthambi padziko lonse, akugwila nchito mwakhama kuti ateteze ufulu wathu wolambila Yehova ndi kulalikila uthenga wabwino. Timayamikila mwayi woimilako abale ndi alongo amene akutsutsidwa ndi akuluakulu a boma. Kaya tipambane milanduyo m’khoti kapena ayi, kukambilana nawo anthuwo kumatithandiza kuti ticitile umboni kwa abwanamkubwa, mafumu, komanso kumaiko. (Mat. 10:18) Oweluza, oimilako boma, oulutsa nkhani, komanso anthu ena, ayenela kuganizila malemba amene timaika m’zikalata zofotokoza mbali yathu pa mlandu komanso m’zimene timakamba tikakhala m’khoti. Anthu amaganizo abwino amaphunzila kuti a Mboni za Yehova n’ndani, komanso kumene amacotsa zimene amakhulupilila. Ena mwa anthu amenewa akhala okhulupilila anzathu.

ZIKOMO YEHOVA!

Kwa zaka zoposa 40 zapitazi, ndakhala ndi mwayi wosewenzela limodzi ndi madipatimenti oona zamalamulo m’maofesi a nthambi padziko lonse. Ndipo ndakhalanso ndi mwayi woimilako abale ndi alongo m’makhoti akuluakulu ambili komanso wolankhulana ndi akuluakulu a boma. Ndimawakonda komanso kuwanyadila anchito anzanga a m’Dipatimenti Yoona za Malamulo ku likulu lathu la padziko lonse, komanso a m’madipatimenti a zamalamulo padziko lonse. Ndakhala ndi umoyo wodzala ndi madalitso komanso wokhutilitsa.

Philip ndi Elizabeth Brumley.

Elizabeth wakhala akundicilikiza mwacikondi komanso mokhulupilika kwa zaka 45 zapitazi, ndipo watelo m’nthawi zabwino komanso zovuta. Ndimamunyadila cifukwa wakhala akucita zimenezi ngakhale kuti wakhala akulimbana ndi matenda amene amafooketsa thanzi lake.

Tazionela tekha kuti mphamvu ndi cipambano sizicokela m’maluso amene tingakhale nawo. Izi n’zogwilizana ndi zimene Davide anakamba kuti, “Yehova ndiye mphamvu kwa anthu ake.” (Sal. 28:8) Zoonadi, “Yehova ndiye mwini nkhondo.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani