MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU
Zimene Mungacite Kuti Muziwelenga Baibo Tsiku Lililonse
Pokhala ndi zocita zambili, kodi nthawi zina zimakubvutani kutsatila pulogilamu yanu yowelenga Mau a Mulungu tsiku lililonse? (Yos. 1:8) Ngati n’conco, yesani malingalilo otsatilawa:
Chelani alamu. Chelani alamu pa cipangizo kuti izikukumbutsani kuti muwelenge Baibo.
Ikani Baibo pa malo oonekela bwino. Ngati mumawelenga Baibo yopulinta, muziiika pa malo oonekela kuti muziiona mosabvuta tsiku lililonse.—Deut. 11:18.
Muzimvetsela Baibo ya mau. Muzimvetsela Baibo ya mau pomwe mukugwila nchito za tsiku ndi tsiku. Pa nkhaniyi, mpainiya wina dzina lake Tara, amenenso ndi mai ndipo amagwila nchito usiku, anakamba kuti: “Ndikamamvetsela Baibo ya mau pomwe ndikugwila nchito za pakhomo, zimakhala kuti ndikuwelenga Baibo.”
Limbikilani. Ngati zocitika zosayembekezeleka zasokoneza pulogilamu yanu, mungawelengeko mavesi ocepa musanagone. Ngakhale mutamawelenga kambali kocepa tsiku lililonse, mudzapindulabe kwambili.—1 Pet. 2:2.