“Limbani m’Cikhulupililo”
“Limbani m’cikhulupililo, . . . khalani amphamvu.” —1 AKORINTO 16:13.
1. (a) N’ciani cinacitikila Petulo pa Nyanja ya Galileya? (Onani cithunzi pamwamba.) (b) N’cifukwa ciani Petulo anayamba kumila?
TSIKU lina usiku, mtumwi Petulo ndi ophunzila ena analimbana ndi mphepo yamkuntho pa Nyanja ya Galileya pofuna kuolokela ku tsidya lina. Mwadzidzidzi, anaona Yesu akuyenda pa nyanja. Petulo anapempha Yesu kuti amulole kuyenda pamadzi kupita kwa iye. Pamene Yesu anamulola, Petulo anatuluka m’bwato ndi kuyamba kupita kwa iye. Patapita nthawi yocepa, Petulo anayamba kumila. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anayamba kuyang’ana mphepo yamkuntho ndipo anacita mantha. Atayamba kumila, Petulo anafuula ndi kupempha Yesu kuti am’thandize. Mwamsanga, Yesu anatambasula dzanja lake ndi kum’gwila ndipo anati: “Wacikhulupililo cocepa iwe, n’cifukwa ciani wakaikila?”—Mateyu 14:24-32.
2. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?
2 Tsopano, tiyeni tikambilane zinthu zitatu zokhudza cikhulupililo zimene tingaphunzile pa cocitika ca Petulo. Zinthu zimenezi ndi: (1) mmene poyamba Petulo anakhulupilila kuti Yehova adzamuthandiza, (2) cimene cinapangitsa Petulo kuyamba kutaya cikhulupililo, ndi (3) cimene cinam’thandiza kulimbitsanso cikhulupililo cake. Kukambilana mfundo zimenezi kungatithandize kuona mmene tingakhalile ‘olimba m’cikhulupililo.’—1 Akorinto 16:13.
CIKHULUPILILO CAKUTI MULUNGU ADZATITHANDIZA
3. N’ciani cinacititsa Petulo kuyenda pamadzi? Nanga ife tacita zotani zofananako?
3 Petulo anali ndi cikhulupililo colimba. N’cifukwa ciani tikutelo? Pamene Yesu anamulola kupita kwa iye, Petulo anatuluka m’bwato ndi kuyamba kuyenda pamadzi. Iye anakhulupilila kuti mphamvu ya Mulungu idzam’thandiza monga mmene inacitila kwa Yesu. Mofananamo, pamene Yesu anatiitana kuti tim’tsatile, tinadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa. N’cifukwa ciani tinacita zimenezo? Cifukwa cakuti tinakhulupilila Yehova ndi Yesu, ndipo tinakhulupililanso kuti adzatithandiza.—Yohane 14:1; ŵelengani 1 Petulo 2:21.
Cikhulupililo ca Petulo cinam’cititsa kucita cinthu cimene cinaoneka ngati cosatheka
4, 5. N’cifukwa ciani cikhulupililo n’cofunika kwambili?
4 Cikhulupililo n’cofunika kwambili. Cikhulupililo ca Petulo cinam’cititsa kuyenda pamadzi, cinthu cimene cinaoneka ngati cosatheka. Nafenso, cikhulupililo cathu cingatithandize kucita zinthu zimene zingaoneke ngati zosatheka. (Mateyu 21:21, 22) Ena a ife tinasintha khalidwe lathu cakuti anthu amene anali kutidziŵa poyamba amatidabwa. Tinapanga masinthidwe amenewa cifukwa cokonda Yehova, ndiponso cifukwa cakuti iye anatithandiza kucita zimenezo. (Ŵelengani Akolose 3:5-10.) Cikhulupililo cinatilimbikitsa kudzipeleka kwa Yehova, komanso kukhala mabwenzi ake, zinthu zimene sizikanatheka popanda thandizo lake.—Aefeso 2:8.
5 Cikhulupililo cathu cimatipangitsa kukhala olimba. Mwacitsanzo, cifukwa ca cikhulupililo timakwanitsa kulimbana ndi Mdyelekezi, mdani wathu wamphamvu. (Aefeso 6:16) Ndiponso cifukwa cokhulupilila Yehova, sitimada nkhawa kwambili tikakumana ndi mavuto. Yehova watilonjeza kutipatsa zinthu zofunikila ngati timamukhulupilila ndi kuika Ufumu wake pamalo oyamba. (Mateyu 6:30-34) Koposa zonse, Yehova adzatipatsa mphatso yamtengo wapatali yomwe ndi moyo wamuyaya cifukwa ca cikhulupililo cathu.—Yohane 3:16.
KUGANIZILA KWAMBILI MAVUTO KUNGAFOOKETSE CIKHULUPILILO CATHU
6, 7. (a) Kodi mphepo yamkuntho ndi mafunde zimene zinacititsa mantha Petulo tingaziyelekezele ndi ciani? (b) N’cifukwa ciani tifunika kudziŵa kuti n’zotheka kutaya cikhulupililo cathu?
6 Pamene Petulo anali kuyenda pa Nyanja ya Galileya, iye anayamba kucita mantha. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anayamba kuyang’ana mphepo ndi mafunde. Izi tingaziyelekezele ndi mavuto amene Akristu amakumana nao masiku ano. Ngakhale kuti mavuto amenewa angaoneke aakulu kwambili, Yehova angatithandize kulimbana nao. Koma kumbukilani zimene zinacitikila Petulo. Iye sanayambe kumila cifukwa coombedwa ndi mphepo komanso mafunde. Baibulo limati: “Ataona mphepo yamkuntho, anacita mantha.” (Mateyu 14:30) Petulo anasiya kuyang’ana Yesu ndipo anayamba kuyang’ana kukula kwa mphepo yamkuntho. Ndiyeno, cikhulupililo cake cinayamba kufooka. Mofananamo, ngati tiganizila kwambili za mavuto athu, tingayambe kukaikila kuti Yehova adzatithandiza.
Ngati tiganizila kwambili zinthu zoipa, cikhulupililo cathu cingayambe kufooka
7 Tifunika kudziŵa kuti n’zotheka kutaya cikhulupililo cathu. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa Baibulo limati kutaya cikhulupililo “ndi chimo limene limatikola mosavuta.” (Aheberi 12:1) Mofanana ndi Petulo, nafenso ngati tiganizila kwambili zinthu zoipa, cikhulupililo cathu cingayambe kufooka. Conco, tingadziŵe bwanji ngati cikhulupililo cathu cayamba kufooka? Mafunso otsatilawa adzatithandiza kudzifufuza.
8. Kodi malonjezo a Mulungu tingayambe kuwaona bwanji kusiyana ndi mmene tinali kuwaonela kale?
8 Kodi malonjezo a Mulungu ndikali kuwaona kuti adzakwanilitsidwadi monga mmene ndinali kuwaonela kale? Mwacitsanzo, Mulungu analonjeza kuti adzaononga dziko la Satana. Komabe, kodi timatengeka ndi zosangulutsa za m’dzikoli? Ngati n’conco, tingayambe kukaikila kuti mapeto ali pafupi. (Habakuku 2:3) Ganizilaninso citsanzo ici: Yehova anapeleka dipo, ndi kulonjeza kuti adzatikhululukila macimo athu. Koma ngati timangoganizila zolakwa zathu zakale, tingayambe kukaikila kuti Yehova anatikhululukila macimo athu. (Machitidwe 3:19) Zotsatilapo zake n’zakuti, tingaleke kusangalala potumikila Mulungu ndipo tingasiye kulalikila.
9. N’ciani cingacitike ngati tiika maganizo athu onse pa zofuna zathu?
9 Kodi ndikali kutumikila Yehova mwakhama? Kutumikila Yehova mwakhama kumatithandiza kuika maganizo athu pa malonjezo a mtsogolo. Koma bwanji ngati tayamba kuika maganizo athu onse pa zofuna zathu? Mwacitsanzo, tingayambe nchito ya malipilo ambili koma imene imatilepheletsa kucita zambili mu utumiki wa Yehova. Izi zingafooketse cikhulupililo cathu, ndipo ‘tingakhale aulesi’ potumikila Yehova.—Aheberi 6:10-12.
Otsatila a Yesu naonso anaphunzila kuti cikhulupililo n’cofunika pokhululukila ena
10. Timaonetsa bwanji kuti timakhulupilila Yehova tikamakhululukila ena?
10 Kodi zimandivuta kukhululukila ena? Anthu ena akatilakwila, kodi timakwiya kapena kuleka kukambitsana nao? Ngati timatelo, ndiye kuti timaganizila kwambili zimene timafuna. Ngati tikhululukila ena timaonetsa kuti timakhulupilila Yehova. N’cifukwa ciani tikutelo? Munthu wina akatilakwila, amakhala ndi ngongole kwa ife. Tikalakwila Yehova, timakhala ndi ngongole kwa iye. (Luka 11:4) Conco, ngati tikhululukila ena, ndiye kuti timakhulupilila Yehova. Timam’khulupilila kuti adzadalitsa khalidwe lathu, ndipo madalitso ake ndi ofunika kwambili kwa ife kuposa kubwezela zoipa zimene ena anaticitila. Otsatila a Yesu anaphunzila kuti cikhulupililo n’cofunika pokhululukila ena. Pamene Yesu anauza otsatila ake kuti azikhululukila ngakhale amene amawalakwila mobwelezabweleza, io anam’pempha kuti: “Tionjezeleni cikhulupililo.”—Luka 17:1-5.
11. N’ciani cingatilepheletse kulandila uphungu?
11 Kodi ndimakhumudwa ndikapatsidwa uphungu? Muziyesetsa kuona mmene uphunguwo ungakupindulitsileni m’malo moganizila zolakwika mu uphunguwo, kapena zofooka za woupeleka. (Miyambo 19:20) Musataye mwai wophunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela.
12. Ndi vuto lotani limene limakhalapo ngati munthu nthawi zonse amangodandaula za amene akutsogolela?
12 Kodi ndimadandaula za amene akutsogolela mumpingo? Pamene Aisiraeli anaganizila kwambili za lipoti loipa la azondi 10, io anayamba kudandaula za Mose ndi Aroni. Ndiyeno, Yehova anafunsa Mose kuti: “Kodi adzayamba liti kundikhulupilila?” (Numeri 14:2-4, 11) Yehova anali kudziŵa kuti Aisiraeli sanali kum’khulupilila cifukwa io anadandaula za utsogoleli wa Mose ndi Aroni, amuna amene anasankhidwa ndi iye. Mofananamo, ngati nthawi zonse timadandaula za abale amene Yehova akugwilitsila nchito kutsogolela anthu ake masiku ano, zimaonetsa kuti cikhulupililo cathu mwa Mulungu cayamba kufooka.
13. N’cifukwa ciani sitiyenela kukhumudwa tikaona kuti cikhulupililo cathu cayamba kufooka?
13 Pambuyo podzifufuza mwa kugwilitsila nchito mafunso awa, musakhumudwe ngati mwaona kuti cikhulupililo canu cayamba kufooka. Kumbukilani kuti nayenso mtumwi Petulo anacita mantha ndi kuyamba kukaikila. Nthawi zina, Yesu anali kupatsa uphungu atumwi onse cifukwa cokhala ndi ‘cikhulupililo cocepa.’ (Mateyu 16:8) Komabe, pali phunzilo lofunika kwambili pa cocitika ca Petulo. Onani zimene anacita atayamba kukaikila ndi kumila pa nyanja.
KUYANG’ANITSITSA YESU KUDZALIMBITSA CIKHULUPILILO CANU
14, 15. (a) Kodi Petulo anacita ciani atayamba kumila? (b) Nanga ‘tingamuyang’anitsitse’ bwanji Yesu?
14 Kodi Petulo anacita ciani atayamba kumila? Petulo anali katswili pa kusambila. Akanafuna akanasambila ndi kubwelela ku bwato. (Yohane 21:7) Nanga n’cifukwa ciani sanacite zimenezo? Cifukwa sanadzidalile. Iye anayang’ananso kwa Yesu ndi kupempha thandizo lake. Ngati taona kuti cikhulupililo cathu cayamba kufooka, tiyenela kutengela Petulo. Tingacite bwanji zimenezo?
15 Monga mmene Petulo anacitila, nafenso tiyenela ‘kuyang’anitsitsa’ Yesu. (Ŵelengani Aheberi 12:2, 3.) Koma sitingathe kumuona ndi maso athu monga mmene Petulo anacitila. Conco, ‘tingamuyang’anitsitse’ bwanji Yesu? Tingacite zimenezo mwa kuŵelenga zinthu zimene anacita ndi kuphunzitsa, ndiponso kum’tsatila mosamala kwambili. Tikatelo, tidzapeza thandizo limene tifunikila kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Tsopano, tiyeni tikambilane njila zimene zingatithandize kutengela Yesu.
Ngati tiyang’anitsitsa Yesu ndi kum’tsatila mosamala kwambili, tidzakhala ndi cikhulupililo colimba (Onani ndime 15)
16. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kulimbitsa cikhulupililo cathu?
16 Muzidalila kwambili Baibulo. Yesu anali wotsimikiza mtima kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu ndi kuti amatipatsa malangizo othandiza kwambili. (Yohane 17:17) Kuti titengele Yesu, tifunika kuŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kuliphunzila, ndi kusinkhasinkha zimene taphunzila. Tifunikanso kufufuza mayankho a mafunso amene tingakhale nao. Mwacitsanzo, kodi mumakhulupililadi kuti tikukhala m’masiku otsiliza? Limbitsani cikhulupililo canu cakuti mapeto ali pafupi mwa kuŵelenga maulosi a m’Baibulo amene akuonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Kodi mufuna kulimbitsa cikhulupililo canu m’malonjezo a Mulungu a mtsogolo? Ŵelengani maulosi a m’Baibulo amene anakwanilitsidwa kale. Kodi mumakhulupilila kuti Baibulo n’lothandiza masiku ano? Mungaŵelenge nkhani za abale ndi alongo amene Baibulo linawathandiza kusintha khalidwe lao.a (Onani mau a munsi.)—1 Atesalonika 2:13.
17. N’ciani cinathandiza Yesu kupilila? Nanga inuyo mungamutsanzile bwanji?
17 Muziika maganizo anu pa madalitso amene Yehova walonjeza. Yesu anaika maganizo ake pa madalitso a mtsogolo. Kucita zimenezi kunam’thandiza kupilila mayeselo aakulu. (Aheberi 12:2) Iye sanatengeke maganizo ndi zinthu za m’dzikoli. (Mateyu 4:8-10) Kodi tingatengele bwanji Yesu? Tingatelo mwa kusinkhasinkha pa zinthu zabwino zimene Yehova walonjeza. Ndipo muziyelekezela kuti muli m’dziko latsopano. Lembani zinthu zimene mufuna kuti mukacite m’Paladaiso. Kapena lembani m’ndandanda wa maina a anthu amene mufuna kudzalankhula nao akadzaukitsidwa. Muziona zimenezi kuti ndi malonjezo a Mulungu. Ndipo muzionanso kuti Mulungu wakulonjezani zimenezi inuyo pa nokha.
18. Kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji kulimbitsa cikhulupililo canu?
18 Muzipempha cikhulupililo coonjezeleka. Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupempha Yehova kuti awapatse mzimu woyela. (Luka 11:9, 13) Pamene mupempha mzimu woyela, muzipemphanso cikhulupililo coonjezeleka. Cikhulupililo ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa. Muzichula zinthu mwacindunji m’pemphelo lanu. Mwacitsanzo, ngati muona kuti zimakuvutani kukhululukila ena, pemphani Yehova kuti alimbitse cikhulupililo canu kuti muzikhululukila ena.
19. Tingasankhe bwanji mabwenzi abwino?
19 Muzisankha mabwenzi amene ali ndi cikhulupililo colimba. Yesu anali kusankha mabwenzi ake mosamala kwambili. Mabwenzi ake apamtima anali atumwi ndipo io anali okhulupilika ndi omvela kwa iye. (Ŵelengani Yohane 15:14, 15.) Muzitengela Yesu pankhani yosankha mabwenzi. Anthu amene mufuna kuti akhale mabwenzi anu ayenela kukhala ndi cikhulupililo colimba ndiponso omvela Yesu. Mabwenzi enieni ndi oona mtima kwa wina ndi mnzake, ngakhale pamene afunika kupatsa uphungu kapena kuulandila.—Miyambo 27:9.
20. Tingapindule bwanji cifukwa cothandiza ena kulimbitsa cikhulupililo cao?
20 Muzithandiza ena kulimbitsa cikhulupililo cao. Yesu anathandiza ophunzila ake kulimbitsa cikhulupililo cao mwa zocita ndi zokamba zake. (Maliko 11:20-24) Nafenso tiyenela kutengela Yesu. Ngati ticita zimenezo, tidzalimbitsa cikhulupililo cathu ndi ca ena. (Miyambo 11:25) Nanga mungathandize bwanji anthu a m’gawo lanu? Pamene muphunzitsa ena Baibulo, muzigogomezela umboni wakuti Mulungu aliko, amasamala za ife, ndiponso kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu. Kodi mungathandize bwanji abale ndi alongo kulimbitsa cikhulupililo cao? Mukaona kuti m’bale kapena mlongo akudandaula za abale amene akutsogolela, musafulumile kusiya kukambitsana naye. Mwanzelu, muthandizeni kulimbitsanso cikhulupililo cake. (Yuda 22, 23) Ngati ndinu mwana wa sukulu, ndipo aphunzitsi anu akuphunzitsa za cisinthiko, limbani mtima ndi kuteteza cikhulupililo canu pa nkhani ya cilengedwe. Mwina aphunzitsi anu ndi ana a sukulu anzanu angavomeleze malingalilo anu.
21. Kodi Yehova watilonjeza ciani?
21 Yehova ndi Yesu anathandiza Petulo kuthetsa cikaikilo ndi mantha. Pambuyo pake, Petulo anadzakhala citsanzo cabwino kwa ena. Mofananamo, Yehova amatithandiza kukhalabe olimba m’cikhulupililo. (Ŵelengani 1 Petulo 5:9, 10.) Kulimbitsa cikhulupililo kumafuna khama, koma Yehova adzatidalitsa ngati tiyesetsa kucita zimenezo.
a Mwacitsanzo, onani nkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu” mu Nsanja ya Mlonda yogaŵila.