LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 9/15 masa. 27-32
  • Tingaonetse Bwanji Kuti Timakonda Yehova?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tingaonetse Bwanji Kuti Timakonda Yehova?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ONETSANI KUTI MUMAYAMIKILA YEHOVA
  • MUZISINKHASINKHA ZIMENE YEHOVA AMAKUPHUNZITSANI
  • MUZILANDILA CILANGO CA YEHOVA
  • MUZIDALILA YEHOVA KUTI AKUTHANDIZENI NDI KUKUTETEZANI
  • Kodi Yehova Waonetsa Bwanji Kuti Amatikonda?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Khalani Pafupi Ndi Yehova
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • “Uzikonda Yehova Mulungu Wako”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Muzikhulupirira Kuti Yehova Amakukondani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 9/15 masa. 27-32
1. M’bale akulalikila; 2. Tate akuŵelengela mwana wake buku la Nkhani za m’Baibulo; 3. Mlongo akuphunzitsa ena za Yehova

Tingaonetse Bwanji Kuti Timakonda Yehova?

“Ife timasonyeza cikondi, cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.”—1 YOHANE 4:19

NYIMBO: 56, 138

KODI MUMAMVA BWANJI MUKAGANIZILA MMENE YEHOVA . . .

  1. amasamalila zosoŵa zanu?

  2. amakuphunzitsilani coonadi?

  3. amakupatsilani cilango?

1, 2. Kodi Yehova watiphunzitsa bwanji kuti tizim’konda?

TATE amaphunzitsa bwino ana ake ngati iye ndi citsanzo cabwino. Ngati tate amakonda ana ake, naonso amayamba kum’konda. Koma palibe munthu amene anatikondapo kuposa mmene Atate wathu Yehova amatikondela. Conco, timakonda Mulungu “cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.”—1 Yohane 4:19.

2 Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti “ndi amene anayamba kutikonda”? Baibulo limati: “Pamene tinali ocimwa, Kristu anatifela.” (Aroma 5:8) Atate wathu wacikondi, Yehova, anapeleka mwana wake dipo kuti atipulumutse ku ucimo ndi imfa. Mphatso yamtengo wapatali imeneyi yapangitsa kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti tizim’konda. Yehova anapeleka citsanzo cabwino kwambili pankhani ya cikondi mwa kupeleka dipo. Iye anatiphunzitsa kuti tifunika kukhala ndi cikondi copanda dyela ndi oolowa manja.—1 Yohane 4:10.

3, 4. Kodi tingaonetse bwanji kuti timakonda Mulungu?

3 Khalidwe lalikulu la Yehova ndi cikondi. N’cifukwa cake Yesu anakamba kuti lamulo lalikulu ndi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse, ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Yehova amafuna kuti tizim’konda ndi ‘mtima wonse.’ Zimam’pweteka mtima akaona kuti tikukonda kwambili munthu wina kapena cinthu cina ciliconse kuposa iye. Komabe sitiyenela kum’konda mwamwambo cabe. Yehova afunanso kuti tizim’konda ndi ‘maganizo athu onse’ komanso ‘mphamvu zathu zonse.’ Izi zitanthauza kuti cikondi cathu pa Yehova cimaphatikizapo zimene timaganiza ndi kucita.—Ŵelengani Mika 6:8.

4 Conco, tiyenela kukonda Yehova ndi moyo wathu wonse kuphatikizapo zonse zimene tili nazo. Timaonetsa kuti timam’kondadi mwa kuika zofuna zake pamalo oyamba. M’nkhani yapita, tinakambilana njila zinai zimene Yehova waonetsela cikondi cake cacikulu kwa ana ake. Koma tsopano tiyeni tikambilane njila zinai zimene zingatithandize kukonda kwambili Yehova, komanso mmene tingaonetsele kuti timam’konda.

ONETSANI KUTI MUMAYAMIKILA YEHOVA

5. Tikaganizila zonse zimene Yehova waticitila, kodi timafuna kucita ciani?

5 Wina wake akakupatsani mphatso, mosakaikila mumaonetsa kuti ndinu oyamikila. Ndipo mumagwilitsila nchito mphatsoyo cifukwa mumaiona kukhala yofunika. Yakobo analemba kuti: “Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo imacokela kumwamba, pakuti imatsika kucokela kwa Atate wa zounikila zonse zakuthambo, ndipo iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yakobo 1:17) Timayamikila kwambili kuti Yehova amatipatsa zonse zimene tifunikila kuti tikhale ndi moyo komanso osangalala. Tikudziŵa kuti Mulungu amatikonda kwambili ndipo nafenso timafuna kuonetsa kuti timam’konda kwambili. Kodi inu mufuna kucita zimenezi?

6. Kodi Aisiraeli anali kufunika kucita ciani kuti Yehova apitilize kuwadalitsa?

6 Aisiraeli analandila zinthu zabwino zambili kucokela kwa Yehova. Kwa zaka mahandeledi ambili, iye anali kuwatsogolela ndi malamulo ake. Anali kuwapatsanso zonse zofunikila paumoyo wao. (Deuteronomo 4:7, 8) Aisiraeli akanaonetsa kuti amayamikila Yehova mwa kumvela malamulowo. Mwacitsanzo, popeleka nsembe kwa Yehova, io anali kufunika kupeleka “zipatso zoyamba kuca zabwino koposa.” (Ekisodo 23:19) Aisiraeli anali kudziŵa kuti Yehova adzapitiliza kuwadalitsa ngati apitiliza kumumvela ndi kupeleka zinthu zabwino koposa.—Ŵelengani Deuteronomo 8:7-11.

7. Tingaonetse bwanji kuti timakonda Yehova ndi ‘zinthu zathu zamtengo wapatali’?

7 Nafenso tingaonetse Yehova kuti timam’konda mwa kum’patsa ‘zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miyambo 3:9) Timacita zimenezi mwa kum’lemekeza pogwilitsila nchito zinthu zimene tili nazo. Mwacitsanzo, tingapeleke zinthu zocilikizila nchito ya Ufumu pampingo wathu kapena padziko lonse lapansi. Kuti tionetse kuti timakonda Yehova sizidalila kuculuka kapena kucepa kwa zinthu zimene tili nazo. (2 Akorinto 8:12) Koma palinso njila zina zimene tingaonetsele Yehova kuti timam’konda .

Ngati tikhulupilila Yehova kwambili, tidzayambanso kum’konda kwambili

8, 9. Ndi njila ina iti imene tingaonetsele Yehova kuti timam’konda? Kodi Mike ndi banja lake anacita ciani?

8 Yesu anatiphunzitsa kuti sitiyenela kudela nkhawa za cakudya ndi zovala, koma tiyenela kupitiliza kufunafuna Ufumu coyamba. Atate wathu walonjeza kuti adzatipatsa zonse zimene timafunikila. (Mateyu 6:31-33) Timam’khulupilila Yehova ndipo tikudziŵa kuti adzakwanilitsa lonjezoli. Ngati munthu umam’kondadi, umam’khulupililanso. Kukamba zoona, ngati tikhulupilila Yehova kwambili tidzayambanso kum’konda kwambili. (Salimo 143:8) Conco, tiyenela kudzifunsa kuti: Kodi zolinga zanga ndi mmene ndimagwilitsila nchito mphamvu ndi nthawi yanga zimaonetsa kuti ndimakondadi Yehova? Kodi ndimadalila Yehova tsiku lililonse kuti adzasamalila zosoŵa zanga?

9 Mike ndi banja lake amadalila Yehova. Pamene Mike anali wacicepele anali kufunitsitsa kukatumikila ku dziko lina. Ngakhale ataloŵa m’banja komanso kukhala ndi ana aŵili, Mike sanasinthe colinga cake. Mike ndi banja lake ataŵelenga za abale ndi alongo amene akutumikila kumalo osoŵa, anaganiza zoyamba kukhala moyo wosalila zambili. Iwo anagulitsa nyumba yao ndi kusamukila m’nyumba ina yaing’ono. Mike anacepetsanso nambala ya makasitomala ake, ndipo anapeza njila imene angaziyendetsela bizinesiyo ali ku dziko lina kupyolela pa intaneti. Pamapeto pake, Mike ndi banja lake anasamukila ku dziko lina, ndipo kumeneko anali kusangalala ndi utumiki wao. Mike anati: “Tinaona kuti mau a Yesu olembedwa pa Mateyu 6:33 ndi oona.”

MUZISINKHASINKHA ZIMENE YEHOVA AMAKUPHUNZITSANI

10. N’cifukwa ciani tiyenela kusinkhasinkha pa zimene timaphunzila za Yehova monga Mfumu Davide?

10 Mfumu Davide inalemba kuti: “Zakumwamba zikulengeza ulemelelo wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza nchito ya manja ake.” Anaonjezelanso kuti: “Cilamulo ca Yehova ndi cangwilo, cimabwezeletsa moyo. Zikumbutso za Yehova ndi zodalilika, zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.” Kuganizila mozama za malamulo a Yehova komanso kukongola kwa cilengedwe, kunathandiza Davide kuyandikila Mulungu, ndipo anafuna kuonetsa mmene amam’kondela. Iye anati: “Mau a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga, zikukondweletseni, inu Yehova, Thanthwe langa ndi Wondiombola.”—Salimo 19:1, 7, 14.

11. Tingagwilitsile nchito bwanji cidziŵitso cimene Yehova watipatsa kuti tionetse kuti timam’konda? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 Masiku ano, Yehova watiphunzitsa zinthu zambili zokhudza iye, colinga cake, cilengedwe cake, komanso Mau ake. Dzikoli limalimbikitsa anthu kucita maphunzilo apamwamba, koma maphunzilowa amacititsa munthu kuleka kukonda Mulungu. Mosiyana ndi dzikoli, Yehova amafuna kuti tikhale ndi cidziŵitso, ndipo amatithandiza kukhala anzelu. Iye afuna kuti tizigwilitsila nchito zimene timaphunzila ndi kuti tizithandiza ena. (Miyambo 4:5-7) Mwacitsanzo, iye amafuna kuti tiziuzako ena ‘coonadi colondola’ ndi kuwathandiza kuti akapulumuke. (1 Timoteyo 2:4) Timaonetsa kuti timakonda Yehova ndi anthu mwa kulalikila mwakhama za Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzacitila anthu.—Ŵelengani Salimo 66:16, 17.

12. Kodi mlongo wina wacitsikana anakamba ciani za mphatso yocokela kwa Yehova?

12 Naonso acinyamata angasinkhesinkhe pa zimene Yehova wawapatsa ndi kuwaphunzitsa. Shannon akali kukumbukila mmene anamvela atapezeka pa msonkhano wa cigawo ali ndi zaka 11, limodzi ndi mng’ono wake amene anali ndi zaka 10. Pa msonkhano umenewo acicepele onse kuphatikizapo Shannon ndi mng’ono wake anapemphedwa kuti akhale pamalo ena ake apadela. Poyamba iye anacita mantha. Kenako, iye anadabwa kwambili kuona kuti acicepele onse akupatsidwa buku lakuti: Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Kodi mphatso ya mtengo wapatali imeneyi inam’cititsa kumva bwanji Shannon ponena za Yehova? Iye anati: “Imeneyi inali nthawi imene ndinatsimikizila kuti Yehova ndi weniweni ndipo amandikonda kwambili. Ndife okondwa kwambili kuti Yehova amatipatsa mphatso zamtengo wapatali kwaulele ngati buku limeneli.”

MUZILANDILA CILANGO CA YEHOVA

13, 14. Kodi tiyenela kucita ciani tikapatsidwa cilango ndi Yehova? Nanga n’cifukwa ciani?

13 Baibulo limatikumbutsa kuti: “Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulila mwana amene amakondwela naye.” (Miyambo 3:12) Ngati timalola Yehova kutiphunzitsa ndi kulandila cilango cocokela kwa iye, timaphunzila kucita zabwino ndipo timakhala osangalala. Komabe, “palibe cilango cimene cimamveka cosangalatsa pa nthawi yomwe ukucilandila, koma cimakhala cowawa.” (Aheberi 12:11) Ngakhale ndi conco, kodi tiyenela kucita ciani Yehova akatipatsa cilango? Sitiyenela kunyalanyaza malangizo a Yehova kapena kukhumudwa ngati tikuona kuti malangizowo sanatikondweletse. M’malo mwake, timamvela Yehova ndi kusintha ngati pafunika kutelo cifukwa cakuti timam’konda.

Ngati timayesetsa kusintha kuti tikondweletse Yehova, timaonetsa kuti timam’kondadi

14 Ayuda ambili m’nthawi ya Malaki sanali kumvela Yehova. Iwo analibe nazo kanthu kuti nsembe zao sizinali kukondweletsa Mulungu. Conco, Yehova anawapatsa uphungu wamphamvu pankhaniyi. (Ŵelengani Malaki 1:12, 13.) Yehova anawapatsa uphungu nthawi zambili koma io sanamumvele. Motelo iye anawauza kuti: “Ndidzakutumizilani tembelelo ndi kutembelela madalitso anu.” (Malaki 2:1, 2) N’zoonekelatu kuti ngati sitimvela Yehova kapena tinyalanyaza uphungu wake tidzaononga ubwenzi wathu ndi iye.

Mtsikana wa Mboni akuyang’ana zovala za masitaelo akudziko pa dzenela ya sitolo

Muziganizila zimene Yehova amafuna osati zimene anthu ambili amakonda m’dzikoli (Onani ndime 15)

15. Ndi maganizo otani amene tiyenela kupewa?

15 Dziko la Satana limalimbikitsa anthu kukhala onyada ndi odzikonda. Anthu ambili safuna kuongoleledwa kapena kuuzidwa zocita. Ena amalandila uphungu cifukwa cakuti akungofunikila kutelo. Ife sitiyenela kukhala conco. Baibulo limatiuza kuti: “Musamatengele nzelu za nthawi ino.” M’malo mwake, tiyenela kuzindikila zimene Yehova amafuna ndi kucita zimene zimam’kondweletsa. (Aroma 12:2) Yehova amagwilitsila nchito gulu lake kupeleka malangizo a panthawi yake. Mwacitsanzo, timalangizidwa mmene tiyenela kucitila zinthu ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzathu. Timalangizidwanso mmene tingasankhile mabwenzi komanso zosangulutsa. Tikamayesetsa kulandila cilango ca Yehova ndi kusintha kuti tim’kondweletse, timaonetsa kuti timayamikila citsogozo cake ndiponso kuti timam’kondadi.—Yohane 14:31; Aroma 6:17.

MUZIDALILA YEHOVA KUTI AKUTHANDIZENI NDI KUKUTETEZANI

16, 17. (a) N’cifukwa ciani tifunika kudziŵa maganizo a Yehova tisanapange zosankha? (b) Kodi Aisiraeli anacita ciani m’malo modalila Yehova?

16 Ana amadalila makolo ao kuti awathandize ndi kuwateteza. Ngakhale akuluakulu amafunsila uphungu kwa makolo ao. Amadziŵa kuti ngakhale kuti ali ndi ufulu wodzisankhila zocita, makolo ao angawapatse malangizo othandiza. Atate wathu Yehova watipatsa ufulu wodzisankhila zocita. Koma popeza kuti timam’khulupilila ndi kum’konda, nthawi zonse timapempha thandizo kwa iye, ndipo timayesetsa kucita zimene tingathe kuti tidziŵe zimene iye amafuna tisanasankhe zocita. Ngati timadalila Yehova, iye adzatipatsa mzimu wake woyela kuti utithandize kucita zabwino.—Afilipi 2:13.

17 M’nthawi ya Samueli, Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Afilisiti. M’malo mofunsila kwa Yehova kuti awauze zocita, io anati: “Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.” Kodi cosankhaco cinali ndi zotsatilapo zotani? Baibulo limati: “Amene anaphedwa anali oculuka kwambili. Panaphedwa amuna oyenda pansi a Isiraeli okwanila 30,000. Ngakhalenso likasa la Mulungu linalandidwa.” (1 Samueli 4:2-4, 10, 11) Aisiraeli anali kuganiza kuti kungotenga likasa ndi kupita nalo kunkhondo, ndiye kuti Yehova adzawathandiza ndi kuwateteza. Koma sanapemphe thandizo kwa Yehova kapena kuyesa kudziŵa zimene anali kuganiza. M’malo mwake, io anangocita zimene anaona kuti n’zabwino. Ndipo anavutika kwambili ndi zotsatilapo zake.—Ŵelengani Miyambo 14:12.

18. Kodi Baibulo limati ciani pankhani yokhulupilila Yehova?

18 Wamasalimo amene anali kukonda kwambili Yehova ndi kum’dalila analemba kuti: “Yembekezela Mulungu, ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu. Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima. N’cifukwa cake ndakumbukila inu.” (Salimo 42:5, 6) Kodi inunso mumamva conco? Kodi mumaona kuti ndinu woyandikana ndi Yehova ndipo mumam’dalila? N’zotheka kuyamba kum’khulupilila kwambili. Baibulo limatiuza kuti: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzaongola njila zako.”—Miyambo 3:5, 6.

19. Kodi inu mudzamuonetsa bwanji Yehova kuti mumam’konda?

19 Popeza kuti Yehova ndiye anayamba kutikonda, watiphunzitsa mmene tingaonetsele kuti timam’konda. Tiyeni nthawi zonse tiziganizila kuculuka kwa zinthu zimene Yehova waticitila ndi mmene waonetsela kuti amatikonda. Ndipo tizimuonetsa kuti timam’konda ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse.—Maliko 12:30.

KUFOTOKOZA MAU ENA

  • Yehova watiphunzitsa mmene tingaonetsele cikondi: Yehova samangotiuza kuti amatikonda, koma wacita zinthu zambili zoonetsa kuti amatikondadi. Tikamaganizila kwambili mmene amatikondela, cikondi cathu pa iye cimakula kwambili ndipo timafunitsitsa kutengela citsanzo cake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani