Kodi Mumaona Dzanja la Mulungu pa Umoyo Wanu?
“Dzanja la Yehova lidzadziŵika kwa atumiki ake.”—YESAYA 66:14.
1, 2. Kodi anthu ena amaganiza ciani ponena za Mulungu?
ANTHU ambili amakhulupilila kuti Mulungu alibe nazo kanthu zimene io amacita. Amaganiza kuti Mulungu sakhudzidwa ndi zimene zimawacitikila pa umoyo wao. Mwacitsanzo, pambuyo pakuti mphepo yamkuntho yaononga mizinda ina m’dziko la Philippines mu November 2013, meya wa mzinda wina waukulu anati: “Zioneka kuti Mulungu anali kwinakwake.”
2 Anthu ena amaganiza kuti Mulungu saona zimene io amacita. (Yesaya 26:10, 11; 3 Yohane 11) M’nthawi ya mtumwi Paulo, ena analinso ndi maganizo amenewo. Iye anati: ‘Iwo sanafune kumudziŵa Mulungu molondola.’ Anthu amenewo anali osalungama ndi oipa. Ndipo anali kusilila mwa nsanje komanso kucita macimo.—Aroma 1:28, 29.
3. (a) Ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa? (b) Kodi “dzanja” la Mulungu limatanthauza ciani?
3 Nanga bwanji ifeyo? Ife tidziŵa kuti Yehova amaona zonse zimene timacita. Koma kodi timakhulupilila kuti Yehova amatikonda? Kodi timaona kuti amatithandiza pa umoyo wathu? M’Baibulo, mau akuti “dzanja” la Mulungu amatanthauza mphamvu zake. Iye amagwilitsila nchito mphamvu zake kuti athandize atumiki ake ndi kugonjetsa adani ake. (Ŵelengani Deuteronomo 26:8.) Yesu anakamba kuti anthu ena “adzaona Mulungu.” (Mateyu 5:8) Kodi tili pakati pa anthu amenewo? Nanga ‘tingamuone bwanji Mulungu’? Tiyeni tione zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anaona dzanja la Mulungu ndi za amene sanalione. Tidzaphunzilanso mmene cikhulupililo cingatithandizile kuona dzanja la Mulungu pa umoyo wathu.
ANALEPHELA KUONA DZANJA LA MULUNGU
4. N’cifukwa ciani adani a Isiraeli analephela kuona dzanja la Mulungu?
4 Kale, anthu ambili anali ndi mwai woona ndi kumva za mmene Mulungu anali kuthandizila Aisiraeli. Yehova anacita zozizwitsa kuti atulutse anthu ake mu Iguputo ndi kugonjetsa mafumu ambili m’Dziko Lolonjezedwa. (Yoswa 9:3, 9, 10) Ngakhale kuti mafumu ena anamva ndi kuona mmene Yehova anapulumutsila anthu ake, io “anasonkhanitsa pamodzi magulu ao ankhondo kuti amenyane ndi Yoswa ndi Isiraeli.” (Yoswa 9:1, 2) Pamene anali kumenyana ndi Aisiraeli, mafumuwo anali ndi mwai woona dzanja la Mulungu. Cifukwa ca mphamvu zazikulu za Yehova, ‘dzuŵa linaima, ndiponso mwezi unaima mpaka mtunduwo utalanga adani ake.’ (Yoswa 10:13) Koma Yehova analola adani a Isiraeli “kuumitsa mitima” yao kuti acite nkhondo ndi Isiraeli. (Yoswa 11:20) Adaniwo anagonjetsedwa cifukwa analephela kuvomeleza kuti Yehova anali kumenyela nkhondo anthu ake.
Tifunika kuona dzanja la Mulungu pa umoyo wathu
5. Kodi Mfumu yoipa Ahabu analephela kukhulupilila ciani?
5 Patapita zaka zambili, Mfumu yoipa Ahabu, anali ndi mwai woona dzanja la Mulungu pa zocitika zosiyanasiyana. Eliya anamuuza kuti: “Sikugwa mame kapena mvula zaka zikubwelazi, pokhapokha ine nditalamula.” (1 Mafumu 17:1) Izi zinatheka cifukwa ca dzanja la Mulungu, koma Ahabu analephela kukhulupilila zimenezi. Pambuyo pake, Eliya anapemphela kwa Yehova, ndipo Mulungu anamuyankha mwa kutumiza moto kucokela kumwamba. Ahabu anaona zimenezo. Ndiyeno, Eliya anauza Ahabu kuti Yehova adzathetsa cilala ndipo adzagwetsa cimvula. (1 Mafumu 18:22-45) Ahabu anaona zozizwitsa zimenezi, koma sanakhulupilile kuti zinatheka cifukwa ca mphamvu za Yehova. Tiphunzilapo ciani pa zitsanzo zonsezi? Tifunika kuona dzanja la Mulungu pa umoyo wathu.
ANAONA DZANJA LA YEHOVA
6, 7. Kodi Agibeoni ndi Rahabi anazindikila ciani?
6 Agibeoni anali osiyana kwambili ndi anthu amene anali kukhala nao pafupi. Iwo anaona dzanja la Mulungu. M’malo mocita nkhondo, Agibeoni anacita pangano la mtendele ndi Aisiraeli. N’cifukwa ciani? Iwo anakamba kuti cifukwa anamva za Yehova ndi zonse zimene anacitila anthu ake. (Yoswa 9:3, 9, 10) Anacita bwino kuzindikila kuti Yehova anali kumenyela nkhondo Aisiraeli.
7 Rahabi nayenso anaona dzanja la Yehova. Iye sanali Mwiisiraeli, koma anamva zimene Yehova anacita kuti atulutse anthu ake mu Iguputo. Pamene azondi aŵili aciisiraeli anapita kunyumba kwake, iye anawauza kuti: “Ndikudziŵa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.” Rahabi anali kukhulupilila kuti Yehova adzam’pulumutsa iye ndi banja lake. Iye anali ndi cikhulupililo mwa Yehova ngakhale kuti anadziŵa kuti kucita zimenezo kunali kuika moyo wake pangozi.—Yoswa 2:9-13; 4:23, 24.
8. Kodi Aisiraeli ena anazindikila bwanji mphamvu za Mulungu?
8 Mosiyana ndi Ahabu Mfumu yoipa, Aisiraeli ena amene anaona moto ukucokela kumwamba, anazindikila kuti Mulungu ndiye wacita zimenezo poyankha pemphelo la Eliya. Iwo anafuula kuti: “Yehova ndiye Mulungu woona!” (1 Mafumu 18:39) Ataona zimenezi, anthuwo anavomeleza kuti anaona mphamvu za Mulungu.
9. N’ciani cingatithandize kuona Yehova ndi dzanja lake?
9 Takambilana zitsanzo zabwino ndi zoipa zimene zingatithandize kudziŵa zimene ‘kuona Mulungu,’ kapena kuona dzanja la Mulungu kumatanthauza. Pamene tiphunzila za Yehova ndi makhalidwe ake, timayamba kuona dzanja lake ndi ‘maso a mtima wathu.’ (Aefeso 1:18) Izi zimatilimbikitsa kuyamba kutengela zitsanzo za anthu okhulupilika akale ndi a masiku ano, amene anaonapo mmene Yehova anathandizila anthu ake. Komabe, kodi tili ndi umboni woonetsa kuti Mulungu akuthandiza anthu ake masiku ano?
UMBONI WAKUTI MULUNGU AMATITHANDIZA MASIKU ANO
10. Ndi umboni uti umene uonetsa kuti Yehova akuthandiza anthu ake masiku ano? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
10 Tili ndi maumboni ambili oonetsa kuti Yehova akupitiliza kuthandiza anthu ake masiku ano. Timamva za zocitika za anthu amene anapempha thandizo kwa Mulungu ndipo iye anayankha mapemphelo ao. (Salimo 53:2) Mwacitsanzo, tsiku lina pamene Allan anali kulalikila pacilumba ca ku Philippines, anakumana ndi mai wina. Mai ameneyo anayamba kulila. Allan anakamba kuti, “M’maŵa tsiku limenelo, mai ameneyo anapempha Yehova kuti a Mboni afike panyumba pake.” Pamene anali mtsikana, iye anali kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma ataloŵa m’banja, anasamuka kupita pacilumba cina. Conco, sanapitilize kuphunzila Baibulo. Mulungu anayankha pemphelo lake mwamsanga, ndipo zimenezi zinam’khudza mtima kwambili. Patangopita miyezi yocepa, anadzipeleka kwa Yehova.
Kodi mumayesetsa kuona dzanja la Yehova pa umoyo wanu? (Onani ndime 11-13)
11, 12. (a) Kodi Yehova amathandiza bwanji atumiki ake? (b) Fotokozani mmene Yehova anathandizila mlongo wina.
11 Atumiki a Yehova ambili anaona dzanja lake likuwathandiza kusiya zizoloŵezi zoipa monga kukoka fodya, kumwa mankhwala osokoneza bongo, ndi kuonelelela zamalisece. Ena anakamba kuti anayesapo kusiya, koma analephela. Komabe, atapempha Yehova kuti awathandize, iye anawapatsa “mphamvu yoposa yacibadwa,” ndipo anakwanitsa kuthetsa zizoloŵezi zimenezo.—2 Akorinto 4:7; Salimo 37:23, 24.
Yehova amathandiza atumiki ake kupilila mavuto aakulu
12 Yehova amathandizanso atumiki ake kupilila mavuto aakulu. Izi n’zimene zinacitikila mlongo wina dzina lake Amy. Iye anatumizidwa kuti akathandize kumanga Nyumba ya Ufumu ndi nyumba ya amishonale pacilumba ca pa Nyanja ya Pacific. Cikhalidwe ca kumeneko cinali cosiyana ndi ca kwao. Nthawi zambili sikunali kupezeka magetsi ndiponso madzi abwino. Ndipo m’dela limenelo madzi anali kusefukila. Analinso kuyewa acibale ake, ndipo anali kukhala m’cipinda cacing’ono m’hotela. Tsiku lina, mlongoyu anakamba mokhadzula kwa mlongo amene anali kuseŵenza naye. Pambuyo pake, anadziimba mlandu cifukwa ca zimene anacita. Atapita kucipinda cake, anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize. Panthawiyo kunalibe magetsi. Ndiyeno, magetsi atabwela, iye anayamba kuŵelenga nkhani yokamba za Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi mu Nsanja ya Olonda. Nkhaniyo inafotokoza mavuto ofanana ndi amene iye anali kukumana nao. Mlongoyu anakamba kuti: “Zinali ngati kuti Yehova akukamba ndi ine usikuwo. Nkhaniyo inandilimbikitsa kupitiliza utumiki wanga.”—Salimo 44:25, 26; Yesaya 41:10, 13.
13. Ndi umboni wotani umene tili nao woonetsa kuti Yehova wathandiza anthu ake kuteteza ufulu wao wolalikila?
13 Yehova wathandizanso anthu ake kuteteza ndi kulembetsa mwalamulo nchito yolalikila uthenga wabwino. (Afilipi 1:7) Mwacitsanzo, maboma ena akafuna kuletsa nchito yathu yolalikila, timadziteteza mwa kupita ku khoti. Kuyambila mu 2000, tapambana milandu 268 m’makhoti akuluakulu padziko lonse. Ndipo milandu 24 tinapambanila mu Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. N’zoonekelatu kuti palibe munthu amene angalepheletse dzanja la Mulungu.—Yesaya 54:17; ŵelengani Yesaya 59:1.
14. Ndi umboni wina uti umene uonetsa kuti Mulungu ali ndi anthu ake?
14 Nchito yolalikila uthenga wabwino padziko lonse ndi umboni winanso woonetsa kuti Mulungu amatithandiza. (Mateyu 24:14; Machitidwe 1:8) Ndipo mgwilizano umene uli pakati pa atumiki a Yehova ocokela m’mitundu yonse umatheka cifukwa ca thandizo la Yehova. Mgwilizano umenewu ndi wapadela kwambili. Ngakhale anthu amene satumikila Yehova amakamba kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (1 Akorinto 14:25) Pali maumboni ambili oonetsa kuti Mulungu ali ndi anthu ake. (Ŵelengani Yesaya 66:14.) Kodi inu panokha mumaona dzanja la Yehova pa umoyo wanu?
KODI MUMAONA DZANJA LA YEHOVA PA UMOYO WANU?
15. N’cifukwa ciani nthawi zina sitingaone dzanja la Yehova pa umoyo wathu?
15 Nthawi zina, sitingaone dzanja la Mulungu pa umoyo wathu. N’cifukwa ciani tikutelo? Tikakumana ndi mavuto ambili, tingaiŵale kuti Yehova anatithandizapo nthawi zambili m’mbuyomu. Izi n’zimene zinacitikila Eliya. Iye anali wolimba mtima. Koma pamene Mfumukazi Yezebeli anafuna kumupha, anacita mantha. Kwa kanthawi, iye anaiŵala mmene Yehova anam’thandizila m’mbuyomo. Baibulo limakamba kuti Eliya analakalaka kufa. (1 Mafumu 19:1-4) Ndi kuti kumene iye akanapeza thandizo ndi cilimbikitso? Iye anafunika kuyang’ana kwa Yehova.—1 Mafumu 19:14-18.
16. N’ciani cingatithandize kuona Mulungu tikakumana ndi mavuto?
16 Yobu anaika maganizo ake onse pa nkhawa zake, cakuti analephela kuona zinthu monga mmene Yehova anali kuzionela. (Yobu 42:3-6) Nthawi zina, nafenso tingalephele kuona dzanja la Mulungu cifukwa ca mavuto amene tikukumana nao. N’ciani cingatithandize kuona zinthu zimene Mulungu amaticitila? Tifunika kusinkhasinkha zimene Baibulo limakamba ponena za mavuto athu. Tikatelo, tidzaona kuti Yehova ndi weniweni kwa ife, ndipo nafenso tidzakamba kuti: “Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.”
Kodi Yehova amakugwilitsilani nchito kuti muthandize ena kuti ayambe kumuona? (Onani ndime 17 ndi 18)
17, 18. (a) Mungalione bwanji dzanja la Yehova pa umoyo wanu? (b) Fotokozani cocitika cimene cionetsa mmene Mulungu amatithandizila masiku ano.
17 Kodi mungalione bwanji dzanja la Yehova pa umoyo wanu? Tiyeni tikambilane zitsanzo zisanu. Coyamba, ganizilani mmene Yehova anakuthandizilani kuti muphunzile coonadi. Caciŵili, kumbukilani nthawi imene munapita ku msonkhano wacikristu. Pambuyo pomvetsela nkhani, mwina munanenapo kuti: “Nkhani imeneyi monga kuti analembela ine!” Cacitatu, n’kutheka kuti munaona mmene Yehova anayankhila pemphelo lanu. Cacinai, mwina munali kufuna kuonjezela utumiki wanu, ndipo munaona mmene Yehova anakuthandizilani kukwanilitsa colingaco. Cacisanu, n’kutheka kuti munasiya nchito imene inali kukudyelani nthawi yotumikila Yehova, ndipo munaona mmene Mulungu anakwanilitsila lonjezo lake lakuti: ‘Sindidzakutaya ngakhale pang’ono.’ (Aheberi 13:5) Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kudzatithandiza kuona dzanja lake pa umoyo wathu.
18 Mlongo wina wa ku Kenya, dzina lake Sarah, anati: “Ndinapemphelela wophunzila Baibulo amene ndinaona kuti sayamikila zimene anali kuphunzila. Ndinapempha Yehova ngati ndingapitilize kuphunzila naye kapena ai. Nditangokamba kuti ‘Ame,’ foni yanga inalila. Wophunzilayo ndiye anatuma foni ndi kundipempha kuti tipitile limodzi ku misonkhano. Zimenezi zinandikondweletsa kwambili!” Ngati timaona zimene Mulungu amaticitila, tikhoza kuona dzanja lake. Mlongo wina dzina lake Rhonna, amene amakhala ku Asia, anakamba kuti zimatenga nthawi kuti tione mmene Yehova amatithandizila pa umoyo wathu. Anakambanso kuti: “Ukacita zimenezi, umacita cidwi kudziŵa kuti Mulungu amatikonda kwambili.”
19. N’ciani cina cimene tifunika kucita kuti tione Mulungu?
19 Yesu anakamba kuti anthu amene “adzaona Mulungu” afunika kukhala “oyela mtima.” (Mateyu 5:8) Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Zitanthauza kuti maganizo athu ayenela kukhala oyela, ndipo tiyenela kuleka kucita ciliconse coipa. (Ŵelengani 2 Akorinto 4:2.) M’nkhani ino, taphunzila kuti tifunika kupitilizabe kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu kuti tithe kumuona. M’nkhani yotsatila, tidzaphunzila mmene cikhulupililo cingatithandizile kuliona bwinobwino dzanja la Yehova pa umoyo wathu.