LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 10/15 tsa. 27
  • ‘Abale Okhala Ngati Amenewa Muziwalemekeza Kwambili’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Abale Okhala Ngati Amenewa Muziwalemekeza Kwambili’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova N’ciyani?
    Mafunso Ofunsidwa Kaŵili-kaŵili pa Mboni za Yehova
  • Mmene Bungwe Lolamulila Limagwilila Nchito Masiku Ano
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • N’ndani Akutsogolela Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Udindo wa “Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu”
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 10/15 tsa. 27
Cithunzi cakuda coonetsa miting’i ya komiti ya Bungwe Lolamulila

‘Abale Okhala Ngati Amenewa Muziwalemekeza Kwambili’

KUYAMBILA m’caka ca 1992, Bungwe Lolamulila lakhala likusankha akulu okhwima kuuzimu, kuti azithandizila makomiti a bungweli kukwanilitsa nchito yao.a (Onani mau amunsi.) Abale amenewa, amene ndi a “nkhosa zina,” amapeleka thandizo lofunikila ku Bungwe Lolamulila. (Yohane 10:16) Iwo amakhala ndi miting’i mlungu uliwonse m’makomiti amene akutumikila. Nchito yao ndi kufotokozela Bungwe Lolamulila mfundo zina zofunika ndi kupelekapo malingalilo ao. Pambuyo pake, bungwelo limapeleka cigamulo pa mfundozo. Ndiyeno, abalewa amaonetsetsa kuti zimene zagamulidwa zacitika. Abale amenewa ndi odzipeleka kucita utumiki ulionse umene apatsidwa. Iwo amayendela limodzi ndi abale a m’Bungwe Lolamulila ku misonkhano yapadela ndi ya maiko. Amapatsidwanso utumiki wocezela maofesi a nthambi monga oimila likulu la Mboni za Yehova.

M’bale wina amene watumikila monga wothandizila kuyambila mu 1992 anati: “Kucita mwakhama utumiki uliwonse umene ndapatsidwa, kumathandiza kuti Bungwe Lolamulila liziika kwambili maganizo ao pa zinthu za kuuzimu.” M’bale wina amene watumikila monga wothandizila kwa zaka 20 nayenso anati: “Umenewu ndi mwai waukulu koposa umene sindinauyembekezele.”

Bungwe Lolamulila lapatsa othandizila ao amenewa nchito yaikulu, ndipo limayamikila abale okhulupilika amenewa cifukwa ca nchito imene amagwila mwakhama. Tiyeni tonse tipitilize kulemekeza kwambili abale okhala ngati amenewa.—Afilipi 2:29.

a Kuti mudziŵe zambili za nchito ya makomiti 6 a Bungwe Lolamula, onani buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulila, pa tsamba 131.

Abale Othandizila Makomiti a Bungwe Lolamulila

Komiti ya Ogwilizanitsa

  • John Ekrann

  • Robert Wallen

Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli

  • Gerald Grizzle

  • Patrick LaFranca

  • Daniel Molchan

  • Ralph Walls

Komiti Yoona za Nchito Yofalitsa Mabuku

  • Don Adams

  • Robert Butler

  • Harold Corkern

  • Donald Gordon

  • Robert Luccioni

  • Alex Reinmueller

  • David Sinclair

Komiti ya Utumiki

  • Gary Breaux

  • Joel Dellinger

  • Seth Hyatt

  • Christopher Mavor

  • Baltasar Perla, Jr.

  • William Turner, Jr.

  • Robert Wallen

  • Leon Weaver, Jr.

Komiti Yoona za Nchito Yophunzitsa

  • Ronald Curzan

  • Kenneth Flodin

  • William Malenfant

  • Mark Noumair

  • David Schafer

Komiti Yoona za Nchito Yolemba Mabuku

  • Robert Ciranko

  • James Mantz

  • Izak Marais

  • Gene Smalley

  • John Wischuk

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani