LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 June masa. 27-30
  • Khalidwe Labwino Kwambili Kuposa Dayamondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalidwe Labwino Kwambili Kuposa Dayamondi
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAKHALIDWE ABWINO NI AMTENGO WAPATALI KUPOSA CUMA
  • CIFUKWA CAKE KUKHALA OONA MTIMA KUMAVUTA
  • YEHOVA AMATITHANDIZA
  • Khalani Oona Mtima M’zinthu Zonse
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Citani Zinthu Zonse Moona Mtima
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Khalani Woona Mtima pa Zinthu Zonse
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 June masa. 27-30
Mwamuna ndi mkazi wake akubweza pasipoti imene anatola kwa eni ake

Khalidwe Labwino Kwambili Kuposa Dayamondi

Anthu amaona kuti dayamondi ni mwala wa mtengo wapatali. Miyala ina ya dayamondi amaigulitsa madola mamiliyoni ambilimbili. Koma kodi pali zinthu zina zimene Mulungu amaona kuti ni za mtengo wapatali kuposa dayamondi ndi miyala ina ya mtengo wapatali?

Wofalitsa wina wosabatizika dzina lake Haykanush, amene amakhala ku Armenia anatola kacikwama ka ndalama pafupi ndi nyumba yake. Mkati mwake munali khadi la ku banki, pasipoti, ndi ndalama zambilimbili. Mlongoyo anauza mwamuna wake, amene analinso wofalitsa wosabatizika, kuti watola ndalama.

Pa nthawiyo, Haykanush ndi mwamuna wake analibiletu ndalama ndiponso anali ndi nkhongole. Ngakhale zinali conco, iwo anaganiza zobweza ndalamazo kwa mwiniwake. Mwamuna amene anataya ndalamazo ndi banja lake anadadwa kwambili. Haykanush ndi mwamuna wake anafotokozela banjalo kuti zimene amaphunzila m’Baibulo, n’zimene zinawathandiza kukhala oona mtima. Ndipo anapezelapo mwayi wouza banjalo zambili zokhudza Mboni za Yehova ndiponso anawagaŵila zofalitsa.

Banjalo linafuna kupatsa Haykanush ndalama pofuna kumuyamikila, koma iye anakana. Tsiku lotsatila, mkazi wa mwamuna amene anataya ndalamayo anapita ku nyumba ya Haykanush kuti akawathokoze pa zimene anacita. Iye anawacondelela kuti atenge ling’i ya dayamondi.

Mofanana ndi banja limeneli, anthu ambili angadabwe ndi kuona mtima kwa Haykanush ndi mwamuna wake. Koma kodi Yehova anadabwa? Nanga analiona bwanji khalidwe lawo la kuona mtima? Kodi kuona mtima kwawo kunawapindulitsa m’njila lililonse?

MAKHALIDWE ABWINO NI AMTENGO WAPATALI KUPOSA CUMA

Mayankho a mafunso amenewa si ovuta. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti anthu a Mulungu amadziŵa kuti kutengela makhalidwe a Yehova n’kwabwino kwambili kuposa dayamondi, golide, kapena zinthu zina za kuthupi. Kukamba zoona, zimene Yehova amaona kuti n’zamtengo wapatali n’zosiyana kwambili ndi zimene anthu amaona kuti n’zofunika. (Yesaya 55:8, 9) Atumiki ake amaona kuti kutengela makhalidwe a Yehova n’kofunika kwambili.

Tingamvetsetse mfundo imeneyi tikaganizila zimene Baibulo imakamba pankhani yokhala wozindikila ndi wanzelu. Lemba la Miyambo 3:13-15 limati: “Wodala ndi munthu amene wapeza nzelu, ndiponso munthu amene wapeza kuzindikila, cifukwa kupeza nzelu monga phindu n’kwabwino kuposa kupeza siliva monga phindu, ndipo kukhala nazo monga zokolola n’kwabwino kuposa kukhala ndi golide. N’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali, ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo.” Apa n’zoonekelatu kuti Yehova amaona kuti makhalidwe amenewa ni ofunika kwambili kuposa cuma ca kuthupi.

Nanga bwanji za kukhala oona mtima?

Yehova ni woona mtima. Iye “sanganame.” (Tito 1:2) Ndipo anauzila mtumwi Paulo kulembela Akhiristu oyambilila aciheberi kuti: “Pitilizani kutipemphelela, pakuti tikukhulupilila kuti tili ndi cikumbumtima coona, popeza tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

Yesu anapeleka citsanzo cabwino pankhani yokhala woona mtima. Mwacitsanzo, pamene Mkulu wa Ansembe Kayafa anakamba kuti, “Ndikukulumbilitsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khiristu Mwana wa Mulungu!” Yesu anakamba moona mtima ndipo anamuuza kuti ndine Mesiya. Iye anakamba zoona ngakhale kuti anadziŵa kuti Khoti Lalikulu la Ayuda lingamuimbe mlandu wonyoza Mulungu, ndi kuti zimenezi zingacititse kuti aphedwe.—Mateyu 26:63-67.

Nanga bwanji ifeyo? Kodi tidzakhalabe oona mtima ngati tiona kuti tingapeze cuma mwa kukamba bodza?

CIFUKWA CAKE KUKHALA OONA MTIMA KUMAVUTA

Masiku ano otsiliza, kukhala oona mtima kungakhale kovuta cifukwa anthu ambili ni “odzikonda,” ndiponso “okonda ndalama.” (2 Timoteyo 3:2) Ngati pakhala vuto la ndalama kapena ngati nchito n’zovuta kupeza, ambili amaona kuti palibe vuto kuba, kunama kapena kucita zinthu mosaona mtima. Maganizo amenewa ni ofala cakuti ambili amaona kuti kukhala osaona mtima ndiyo njila yabwino yopezela cuma. Ngakhale Akristu ena asankha zinthu zoipa ndipo cifukwa ca kucita zinthu “mwacinyengo,” awononga mbili yawo mumpingo.—1 Timoteyo 3:8; Tito 1:7.

Komabe, Akhiristu ambili amatengela Yesu. Iwo amadziŵa kuti kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo n’kofunika kwambili kuposa cuma kapena phindu lililonse limene angapeze. Ndiye cifukwa cake Akhiristu acicepele sacita cinyengo kuti apeze magiledi abwino ku sukulu. (Miyambo 20:23) Monga mmene taonela pa citsanzo ca Haykanush, si nthawi zonse pamene tingalandile mphatso cifukwa cokhala oona mtima. Komabe, Yehova amasangalala tikakhala oona mtima. Ndipo kukhala oona mtima kumatithandiza kukhala ndi cikumbumtima coyela, cimene n’cinthu ca mtengo watapali.

Citsanzo ca Gagik cionetsa kuti mfundo imeneyi ni yoona. Iye anati: “Nikalibe kukhala Mboni, n’nali kuseŵenza pa kampani ina yaikulu. Mwiniwake wa kampaniyo anali kucitila lipoti ndalama zocepa monga phindu la kampaniyo kuti azilipila msonkho wocepa. Popeza n’nali bwana wamkulu pa kampaniyo, n’nali kufunika kunyengelela anthu otenga msonkho mwa kuwapatsa n’cekeleko kuti asaulule cinyengo ca kampaniyo. Izi zinacititsa kuti ndizidziŵika monga munthu wosaona mtima. N’taphunzila coonadi, ndinaleka nchitoyo ngakhale kuti n’nali kulandila ndalama zambili. M’malomwake, ndinayamba bizinesi yanga. Kungocokela pa tsiku loyamba, n’nalembetsa kampani yanga ndipo n’malipila misonkho yonse.”—2 Akorinto 8:21.

Gagik anati: “Ndalama zimene n’nali kupeza zinali zocepa kwambili, ndipo cinali covuta kusamalila banja langa. Ngakhale n’telo, ndine wosangalala tsopano. Nili ndi cikumbumtima cabwino pamaso pa Yehova. Napeleka citsanzo cabwino kwa ana anga aŵili aamuna, ndipo tsopano n’naikidwa paudindo mumpingo. Cifukwa cokhala woona mtima, nili ndi mbili yabwino kwa anthu amene amatenga misonkho ndi ena amene nimacita nawo bizinesi.”

YEHOVA AMATITHANDIZA

Yehova amakonda anthu amene amacititsa kuti iye atamandike mwa kutengela makhalidwe ake apamwamba, kuphatikizapo khalidwe la kukhala oona mtima. (Tito 2:10) Ndipo tikakhala oona mtima, Mulungu sangatisiye. Anauzila Mfumu Davide kulemba kuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha cakudya.”—Salimo 37:25.

Zimene zinacitikila munthu wokhulupilika Rute zikuonetsa kuti mfundo imeneyi ni yoona. Iye anakhalabe ndi apongozi ake, a Naomi, ngakhale kuti anali okalamba. Rute anapita nawo limodzi ku Isiraeli. Kumeneko anayamba kulambila Mulungu woona. (Rute 1:16, 17) Iye anali woona mtima, ndipo anagwila nchito yokunkha mwakhama potsatila makonzedwe a m’Cilamulo ca Mose othandiza anthu osauka. Monga mmene zinalili kwa Davide, Yehova sanasiye Rute ndi Naomi. (Rute 2:2-18) Mulungu anadalitsa Rute m’njila inanso kuonjezela pa zinthu za kuthupi zimene anam’patsa. Anasankha Rute kukhala mu mzele wa makolo a Mfumu Davide ndiponso Mesiya.—Rute 4:13-17; Mateyu 1:5, 16.

Zimakhala zovuta kwa atumiki a Yehova ena kupeza ndalama zokwanila zogulila zinthu zofunika pa umoyo. Ngakhale n’conco, iwo sacita zinthu mwacinyengo kuti apeze zimene afuna, koma amagwila nchito molimbikila. Akamacita zimenezi, amaonetsa kuti makhalidwe apamwamba a Yehova monga kukhala oona mtima ni ofunika kwambili kwa iwo kuposa zinthu za kuthupi.—Miyambo 12:24; Aefeso 4:28.

Mofanana ndi Rute, Akhiristu padziko lonse lapansi sakaikila zakuti Yehova adzawathandiza. Iwo amakhulupilila Mulungu amene analonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheberi 13:5) Mobwelezabweleza, Yehova anathandiza anthu oona mtima ndipo adzapitiliza kuthandiza amene amakhala oona mtima nthawi zonse. Iye nthawi zonse amasunga lonjezo lake lakuti adzatipatsa zosoŵa zathu.—Mateyu 6:33.

Anthu amaona kuti dayamondi ndiponso cuma n’zofunika kwambili. Koma ndife otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba amaona khalidwe lathu la kuona mtima ndi makhalidwe ena abwino kukhala amtengo wapatali kuposa zinthu zakuthupi zilizonse.

Mboni za Yehova zikulalikila mwamuna wina pafupi ndi shelufu ya zofalitsa

Ngati ndife oona mtima, tidzakhala ndi cikumbumtima coyela pamene tikambilana ndi anthu mu ulaliki

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani