YURI LASHOV/AFP via Getty Images
KHALANI MASO!
Kodi Akhristu Ayenela Kumenya Nkhondo—Nanga Baibo Ikambapo Ciyani?
Monga tikuonela pa nkhondo ya ku Ukraine, atsogoleli acikhristu ambili akulimbikitsa anthu kumenya nkhondo. Onani mmene azibusa a mbali ziŵili zomenyana akulimbikitsila nkhondo.
“Ulemu waukulu na ciyamikilo cathu, zipite kwa asilikali athu omwe akumenya nkhondo yoteteza dziko lathu la Ukraine kwa adani otiukila . . . Mitima yathu, na mapemphelo athu ali nanu nthawi zonse.”—Anatelo mbusa wamkulu wa mzinda wa Kyiv wochedwa Epiphanius I, malinga n’kunena kwa The Jerusalem Post, ya March 16, 2022.
“Pa sondo, mtsogoleli wa Chalichi ca Russian Orthodox, anacititsa mapemphelo odalitsa asilikali a dzikolo la Russia. Anawalimbikitsa kuti acite camuna pa nkhondo yoteteza dziko lawo molimbana na dziko la Ukraine.”—Inatelo nyuzi ya Reuters, April 3, 2022.
Kodi Akhristu ayenela kumenya nkhondo? Nanga Baibo imati ciyani?
Kodi Baibo Imanena Ciyani Kwenikweni?
Baibo imaonetsa kuti otsatila Yesu Khristu oona satengako mbali pa nkhondo.
“Bwezela lupanga lako m’cimake, pakuti onse ogwila lupanga adzafa ndi lupanga.”—Mateyu 26:52.
Kodi munthu amene amavomeleza nkhondo, kapena kumenyako nkhondo tingati amamvela mawu a Yesu?
“Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana. Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:34, 35.
Kodi munthu wolimbikitsa nkhondo amaonetsa cikondi cimene Yesu anati cidzakhala cizindikilo ca ophunzila ake, kapena otsatila ake?
Kuti mumve zambili, ŵelengani nkhani yakuti, “Kodi Akhristu Ayenela Kumenya Nawo Nkhondo”?
Akhristu Kumenya Nkhondo
Kodi n’zothekadi Akhristu kusaloŵa m’nkhondo masiku ano? Inde, n’zotheka. Baibo inakambilatu kuti m’nthawi yathu ino, yochedwa “masiku otsiliza,” padzakhala anthu ocokela m’mitundu yonse amene “sadzaphunzilanso nkhondo,” ndipo zikugwilizana n’zimene Yesu anaphunzitsa.—Yesaya 2:2, 4.
Kuti mumve zowonjezela, ŵelengani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yakuti “Kodi Mulungu amagwilizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo?”
Posacedwa Yehova,a “Mulungu wamtendele,” adzagwilitsa nchito boma lake lakumwamba kuwombola anthu ku “cipsinjo ndi ciwawa.”—Afilipi 4:9; Salimo 72:14.
Kuti muone mmene zimenezi zidzacitikile, tambani vidiyo yakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
a Yehova ndilo dzina leni-leni la Mulungu.—Salimo 83:18.