Anna Moneymaker/Getty Images
KHALANI MASO!
Asayansi Anafendezela Patsogolo Koloko ya Tsiku la Ciwonongeko—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Pa January 24, 2023, asayansi anafendeza muvi wa pa Koloko ya Tsiku la Ciwonongekoa n’kuuika pafupi na pakati pa usiku, poimilako kutha kwa dziko.
“‘Koloko ya Tsiku la Ciwonongeko,’ yoonetsa nthawi yatsalako kuti mtundu wonse wa anthu uwonongedwe, inafendezedwa pafupi na pakati pa usiku. Zimenezi zinacitika pa Ciŵili cifukwa ca nkhondo ya ku Ukraine, kuopsezana na zida zanyukiliya, komanso mavuto azanyengo.”—AFP International Text Wire.
“Pa Ciŵili, asayansi anaulula kuti muvi wa pa ‘Kololo ya Tsiku la Ciwonongeko anausunthila pa masekondi 90 kuti ufike pakati pa usiku—ciwonongeko cimeneci tisanaciyandikilepo conco cikhalile mtundu wa anthu.”—ABC News.
“Upo wa asayansi a kumaiko osiyana-siyana anacenjeza kuti, kuposa na kale lonse, mtundu wa anthu uli pa ciopsezo ca kufafanizika wonse.”—The Guardian.
Kodi mapeto a mtundu wa anthu komanso a dziko lathuli ali pafupidi? Kodi tiyenela kucita mantha na zili kutsogoloku? Nanga Baibo imati ciyani?
Zimene zili m’tsogolo
Malinga n’zimene Baibo imakamba, “dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.” Ndipo anthu “adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Mlaliki 1:4; Salimo 37:29) Conco n’zosatheka kuti anthu akawononge dziko lapansi, moti osathekanso zamoyo kukhalapo.
Komabe, Baibo imachuladi za mapeto. Mwacitsanzo, imati “dzikoli likupita.”—1 Yohane 2:17.
Kuti mudziŵe zimene Baibo imatanthauza ikamanena za mapeto a dzikoli, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Dzikoli Lidzatha? Kodi Baibulo Limanena Kuti Zinthu Zonse Zidzawonongedwa?”
Kuti mudziŵe zimene Baibo imakamba pa zocitika zakutsogoloku, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Mapeto a Dzikoli Adzafika Liti?”
Musataye mtima
Baibo ingatithandize kukhalabe na ciyembekezo ngakhale kuti m’dzikoli muli mavuto osaneneka. Kodi ingatithandize bwanji?
Baibo imatipatsa ulangizi wothandiza. (2 Timoteyo 3:16, 17) Mwacitsanzo, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri” kuti mudziŵe mmene Baibo ingakucotseleni nkhawa, ngakhale kuti moyo uli na mavuto ambili-mbili.
Baibo imalonjeza tsogolo lowala komanso lodalilika. (Aroma 15:4) Imatofotoza zocitika zimene tingaziyembekezele pali pano komanso m’tsogolo. N’zimene zimatipatsa cidalilo poyang’anizana na zotigwela m’dzikoli.
Kuti Baibo ikuthandizeni kwenikweni, conde yambani kuphunzila Baibo kwaulele na Mboni za Yehova.
a “Koloko ya Tsiku la Ciwonongeko imacenjeza anthu kuti mtundu wa anthu watsala pang’ono kudziwononga wokha na zinthu zaluso zoopsa zimene amapanga. Koloko imeneyi ni cizindikilo, kapena kuti cikumbutso, ca mavuto amene tiyenela kuwathetsa ngati tikufuna kukhalapobe pa dziko lapansi.”—Bulletin of the Atomic Scientists.