Kodi Baibo Imatipo Ciyani pa Vuto la Madzi Padziko Lonse?
Tonsefe timafunikila madzi aukhondo kuti tikhale na moyo. Kalembela Wamkulu wa Bungwe la United Nations, António Guterres, anati “popeza ciŵelengelo ca anthu cikuwonjezeka padziko lonse, tikukumana na vuto lalikulu la madzi.” Anthu mabiliyoni zungulile dziko lonse akuvutikila kale kupeza madzi abwino akumwa.
Strdel/AFP via Getty Images
Kodi tidzakhalapo na madzi okwanila kwa anthu onse? Kapena nthawi zonse tizingovutikila kupeza madzi? Nanga Baibo ikutipo ciyani?
Malonjezo a m’Baibo ponena za madzi
Baibo imakamba kuti tsiku lina vuto la kucepekela kwa madzi lidzatha. Ndipo imanenetsa kuti padziko lapansi padzakhala madzi oculuka aukhondo komanso abwino.
“Mʼcipululu mudzatumphuka madzi, ndipo mʼdela lacipululu mudzayenda mitsinje. Malo ouma cifukwa ca kutentha adzakhala dambo la madzi. Ndipo malo aludzu adzakhala ndi akasupe amadzi.”—Yesaya 35:6, 7.
N’cifukwa ciyani tiyenela kulikhulupilila lonjezo limeneli la m’Baibo? Onani zimene Baibo imakamba za mmene dzikoli analipangila.
Zimene Baibo imakamba zokhudza dziko lapansi na zungulile wake wa madzi
“[Mulungu] sanalilenge popanda colinga [dziko lapansi], koma analiumba kuti anthu akhalemo.”—Yesaya 45:18.
Popeza Mulungu analenga dziko lapansi kuti pakhale zamoyo, anapanganso njila zacilengedwe kuti padziko pazikhala madzi abwino oculuka.
“[Mulungu] amakoka madontho a madzi. Madonthowo amasintha nʼkukhala nkhungu imene imapanga mvula, kenako mitambo imagwetsa mvula, imagwetsela aliyense madzi.”—Yobu 36:27, 28.
M’mawu osavuta, vesiyi ifotokoza njila yacilengedwe komanso yodalilika imene Mulungu anapanga kuti nthawi zonse padziko pazikhala madzi. Madzi amakamuka panthaka komanso panyanja ngati nkhungu n’kupita kumwamba. Kumwambako amaungana kenako amagwanso pansi ngati mvula. Izi zimapangitsa kuti anthu na nyama azikhala na madzi abwino komanso aukhondo nthawi zonse.—Mlaliki 1:7; Amosi 5:8.
“Ndidzakugwetselani mvula pa nthawi yake. Nthaka idzakupatsani cakudya, ndipo mitengo yamʼmunda idzakupatsani zipatso zake.”—Levitiko 26:4.
Mulungu analonjeza kuti adzaculukitsa zokolola za Aisiraeli akale, amene anali alimi, powapatsa madzi pa nthawi yake. Iye amadziŵa kuti tifunikila mvula yokwanila pa nthawi yake kuti tikwanitse kubyala na kukolola cakudya.
Zimene Yehova anacitila Aisiraeli akale n’zimenenso adzacita posacedwapa pa dziko lonse lapansi. (Yesaya 30:23) Pali pano, m’maiko ambili vuto la madzi likuwonjezeka, ndipo kusoŵa kwa mvula ni vuto linanso. N’ciyaninso cina cimene Baibo imakamba za mmene vuto la madzi lidzathela?
Mmene vuto la madzi lidzathela
Baibo imaonetsa kuti Mulungu adzagwilitsa nchito Ufumu wake kuthetsa mavuto omwe ali padziko lapansi, kuphatikizapo vuto la madzi lomwe lilipo masiku ano. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu ni boma la kumwamba limene lidzalamulila dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15) Ndipo Ufumu wa Mulunguwo udzacita zimene maboma a anthu alephela kucita, udzacotsapo zonse zimene zimayambitsa mavuto a madzi amene tili nawo.
Vuto: Kusintha kwa nyengo kwacititsa kuti zungulile-zungilile wa madzi asokonezeke. Zotulukapo zake n’zakuti m’madela ambili mukucitika zilala zoopsa komanso kusefukila kwa madzi kowononga. Kusefukila kwa madzi kumeneku kukucitika cifukwa ca cimvula camphamvu kapena kuwonjezeka kwa madzi m’nyanja.
Mankhwala ake: Ufumu wa Mulungu udzakonza mbali zonse zowonongeka za cilengedwe kuti dziko lapansi likhalenso labwino. Mulungu analonjeza kuti: “Tawonani, ndicita zonse zikhale zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5, Buku Lopatulika) M’madela onse ouma mudzatumphuka madzi abwino oculuka. Izi zidzapangitsa ngakhale kumalo osakhalidwa pali pano komanso kumene sikumela kanthu kuphuka na zomela zobiliŵila bwino. (Yesaya 41:17-20) Ufumu wa Mulungu, umene ukulamulidwa na Yesu Khristu, udzalamulilanso mphamvu zacilengedwe.
Yesu ali pa dziko lapansi anakhalitsa bata namondwe woopsa. Mwa kutelo, anaonetsa zimene adzakwanitsa kucita mwa mphamvu zimene Mulungu anam’patsa. (Maliko 4:39, 41) Mu ulamulilo wa Khristu, matsoka a zacilengedwe adzatha. Anthu adzakondwela na mtendele weniweni komanso citetezo. Sadzaopa matsoka a mtundu uliwonse.
Vuto: Anthu komanso makampani aumbombo amawononga mitsinje, madamu, komanso akasupe ena a madzi. Izi zimawonjezela vuto la kucepekela kwa madzi abwino.
Mankhwala ake: Mulungu adzayeletsa dziko lapansi na kukonzanso mitsinje, madamu, nyanja, komanso nthaka. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Mwa ndakatulo, Baibo imati: “Cipululu ndi dziko louma zidzasangalala, dela lacipululu lidzakondwa ndipo lidzacita maluŵa ambili.”—Yesaya 35:1.
Kodi n’ciyani cidzacitikila anthu amene sasamala za cilengedwe ngakhale anthu anzawo? Mulungu analonjeza kuti “[adzawononga] amene akuwononga dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:18; Miyambo 2:21, 22.
Vuto: Akasupe a madzi sakusamalidwa. Izi zacititsa kuti madzi ambili aziwonongedwa kuposa amene dziko lapansi limatulutsa.
Mankhwala ake: N’zokondweletsa kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzapangitsa kuti zofuna za Mulungu, osati za anthu adyela “zicitike padziko lapansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu udzapeleka maphunzilo abwino koposa kwa nzika zake. Yesaya 11:9 imati “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.”a Motsogoleledwa na nzelu yapamwamba imeneyi, limodzi na cikondi cacikulu pa Mulungu komanso pa zonse zimene analenga, anthu adzasamalila bwino dziko lapansi lokongolali na zonse zili mmenemo.
Kuti mudziŵe zambili zimene Ufumu wa Mulungu udzacita onani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacita Ciyani?”
Ŵelengani Yesaya caputala 35 m’Baibo kuti muone mmene dziko lapansi lidzasinthila kukhala paradaiso.
Tambani vidiyo ya Chichewa yakuti, N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? kuti mudziŵe zambili za colinga ca Mulungu pa anthu komanso dziko lapansi.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”