Mmene Mulungu Amasamalila Anthu Amene Ali na Vuto Losamva
Masiku ano anthu pafupifupi 70 miliyoni padziko lonse ali na vuto losamva, ndipo anthu amenewa amagwilitsa nchito zinenelo zamanja zoposa 200. Comvetsa cisoni n’cakuti nthawi zambili anthu amene ali na vuto limeneli amacitidwa zopanda cilungamo. Mwacitsanzo, onani malipoti otsatilawa:
“Kuzungulila dziko lonse, anthu ogontha komanso amene amavutikila kumva nthawi zambili amanyalanyazidwa.”—National Association of the Deaf (U.S.).
“M’dzikoli anthu amene ali na vuto losamva ali m’gulu la anthu osauka kwambili. Ndipo zimakhala zovuta kwa iwo kulandila maphunzilo abwino, kupeza nchito yabwino, komanso kudziŵa nkhani zofunikila.”—World Federation of the Deaf.
Kodi Mulungu amaŵaona bwanji anthu amene ali na vuto losamva? Kodi Baibo imatipo ciyani za anthu osamva? Nanga a Mboni za Yehova akuŵathandiza bwanji anthu amene ali na vuto limeneli masiku ano?
Mmene Mulungu Amaonela Anthu Amene Ali na Vuto Losamva
Baibo imaonetsa kuti Yehovaa Mulungu amaŵakonda anthu amene ali na vuto losamva. Iye amafuna kuti azicitilidwa zinthu mwacilungamo komanso kuti akhale na mwayi wolandila maphunzilo amene iye amapeleka.
Lemba: “Musamatembelele munthu amene ali ndi vuto losamva.”—Levitiko 19:14.
Tanthauzo Lake: Malamulo amene Yehova anapeleka kwa Aisiraeli akale anali kuteteza ufulu wa anthu osamva.
Lemba: “Mulungu alibe tsankho.”—Machitidwe 10:34.
Tanthauzo Lake: Yehova amakonda anthu amitundu yonse komanso azinenelo zonse, kuphatikizapo anthu amene ali na vuto losamva.
Lemba: “Yesu anayamba ulendo . . . , [wolalikila] uthenga wabwino wa Ufumu.”—Mateyu 9:35.
Tanthauzo Lake: Yesu anabwela pa dziko lapansi kudzaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzacitila anthu onse, kuphatikizapo amene ali na vuto losamva.—Mateyu 6:10.
Lemba: Yesu anacititsa “ngakhale anthu amene anali ndi vuto losamva [kumva] komanso amene anali ndi vuto losalankhula [kulankhula].”—Maliko 7:37.
Tanthauzo Lake: Yesu anaonetsa zimene Ufumu wa Mulungu udzacititsa anthu amene ali na vuto losamva kuyamba kumva na kulankhula. Pa cocitika cimeneci, Yesu anaonetsa kukoma mtima mwa kugwilitsa nchito manja polankhula na munthu wosamva, asanamucilitse kuti ayambe kumva na kulankhula.—Maliko 7:31-35.
Lemba: “Makutu a anthu amene ali ndi vuto losamva adzayamba kumva.”—Yesaya 35:5.
Tanthauzo Lake: Yehova anakambilatu kuti anthu osamva adzayamba kumva.—Yesaya 29:18.
Mmene Mboni za Yehova Zikuthandizila Anthu Amene Ali na Vuto Losamva Masiku Ano
Mboni za Yehova zimalalikila uthenga wa Mulungu waciyembekezo kwa anthu amene ali na vuto losamva padziko lonse lapansi. Kodi timacita bwanji zimenezi? Timafalitsa Baibo na mavidiyo ophunzilila Baibo m’zinenelo zamanja zoposa 100. Komanso timaphunzitsa anthu Baibo na kucita misonkhano ya Cikhristu m’zinenelo zamanja. Timapeleka zinthu zonsezi kwaulele kwa aliyense amene afuna thandizo la Mulungu. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yesu analamula kuti: “Munalandila kwaulele, muzipeleka kwaulele.”—Mateyu 10:8.
Mungapeze zinthu zimenezi pa intaneti kapena kuzicita daunilodi pacipangizo canu poseŵenzetsa:
JW.ORG. Dinizani kacizindikilo ka zinenelo pamwamba pa tsamba lililonse pa webusaiti imeneyi kuti mupeze zinthu m’cinenelo camanja cimene mufuna.
App ya JW Library Sign Language. Citani daunilodi app yaulele imeneyi pacipangizo canu, ndipo mudzatha kucita daunilodi na kutamba mavidiyo a cinenelo camanja.
Kodi Tili na Zinthu Ziti Zothandiza Pophunzila Baibo?
Baibo ya cinenelo camanja. Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba Opatulika m’cinenelo camanja ca ku America, ndiyo inali Baibo yathunthu yoyamba kutulutsidwa m’cinenelo camanja padziko lonse. Baibo ya Dziko Latsopano yathunthu kapena mbali yake ikupezeka m’zinenelo zamanja zambili, ndipo caka ciliconse pamawonjezedwa zinenelo zina. (Kuti muone zinenelo zimene zilipo kapena kutamba Baibo pa intaneti, onani bokosi lakuti “Baibo ya Dziko Latsopano m’cinenelo camanja.”)
Onelelani vidiyo ya cingelezi yakuti The Complete New World Translation Is Available in ASL kuti mudziŵe nchito imene imakhalapo potulutsa Baibo m’cinenelo camanja.
Kuti mupindule kwambili na kuŵelenga Baibo, citani daunilodi app ya JW Library Sign Language. Pa app imeneyi mungatambe vesi imene mufuna m’Baibo ya cinenelo camanja.
Dmytro na Vita ni makolo amene ali na vuto losamva, koma ana awo amamva. Onani mmene banjali lapindulila cifukwa cotamba Baibo ya cinenelo camanja tsiku lililonse.
Mavidiyo ophunzitsa Baibo. Mboni za Yehova zatulutsa mavidiyo a cinenelo camanja othandiza anthu kumvetsa Baibo na kuŵathandiza kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo othandiza . . .
Maphunzilo a Baibo okambilana. Phunzilani uthenga wa m’Baibo m’cinenelo camanja mothandizidwa na munthu wina. Mungaphunzile pa nthawi imene mufuna ndipo mungasankhe kuculuka kwa zimene mufuna kuphunzila. Pemphani kuti akuonetseni mmene phunzilo la Baibo laulele limeneli limacitikila.
Onani mmene phunzilo la Baibo linathandizila Jeson Senajonon wa ku Philippines kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu.
Mario Antúnez anali m’busa wa chalichi cina ku Honduras. Onani mmene anapezela mayankho ku mafunso a m’Baibo amene anali nawo pamene muŵelenga mbili ya moyo wake yakuti “Ndinali Ndi Mafunso Ambiri.”
Misonkhano na zocitika zina. Tili na mipingo na tumagulu twa cinenelo camanja padziko lonse, kumene anthu amene ali na vuto losamva amakumana mlungu uliwonse kuti aphunzile na kulambila. Ndipo caka ciliconse timakhala na misonkhano ikulu-ikulu yophunzitsa Baibo m’cinenelo camanja. Pa misonkhano yathu komanso pa zocitika zinazi, pamakhalanso makonzedwe omasulila zimene zikulankhulidwa kwa anthu amene ni osaona komanso ali na vuto losamva. Timafalitsanso mabuku a anthu osaona kwaulele.
Pezani mpingo wa kufupi na kwanu.
Dziŵani za misonkhano yathu yapacaka ya cigawo na ya dela.
Mukapezekepo pa cikumbutso ca imfa ya Yesu. Cikumbutso ni msonkhano wathu wofunika kwambili m’caka.
José Luis Ayala wa ku Mexico, anabadwa na vuto losamva ndipo pambuyo pake analeka kuona. Dziŵani mmene a Mboni za Yehova anamuthandizila kukhala m’phunzitsi wa Baibo waluso.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”