LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 155
  • Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kupatsa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kupatsa?
  • Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Yankho la m’Baibo
  • Ni kupatsa kotani kumene Mulungu amakondwela nako?
  • Ni kupatsa kotani kumene Mulungu sakondwela nako?
  • Kupatsa Kumapindulitsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Opatsa Mowoloŵa Manja Amakhala Acimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kusakila Mphatso Yabwino Koposa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
ijwbq nkhani 155
Munthu wanyamula mphatso

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kupatsa?

Yankho la m’Baibo

Baibo imatilimbikitsa kukhala opatsa, ndipo imati tizicita zimenezi na zolinga zabwino komanso osati mokakamizika. Imaonetsa kuti kupatsa koteloko kumapindulitsa wolandila ngakhalenso kwa wopelekayo. (Miyambo 11:25; Luka 6:38) Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Machitidwe 20:35.

  • Ni kupatsa kotani kumene Mulungu amakondwela nako?

  • Ni kupatsa kotani kumene Mulungu sakondwela nako?

  • Mavesi a m’Baibo okamba za kupatsa

Ni kupatsa kotani kumene Mulungu amakondwela nako?

Mulungu amakondwela tikamapatsa ena zinthu mwa kufuna kwathu. Baibo imati: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”—2 Akorinto 9:7.

Kupatsa na mtima wonse ni mbali ya “kupembedza” kumene Mulungu amavomeleza. (Yakobo 1:27) Yehova amakondwela na munthu amene amathandiza anthu moolowa manja. . Iye amaona kuti ali na nkhongole kwa munthuyo amene wathandiza ena. (Miyambo 19:17) Ndipo Baibo imati Mulungu adzabweza yekha ngongoleyo.—Luka 14:12-14.

Ni kupatsa kotani kumene Mulungu sakondwela nako?

Ngati munthu akupeleka na colinga cadyela. Mwacitsanzo:

  • Pofuna kudzionetsela.—Mateyu 6:2.

  • Pofuna kuti nayenso adzapatsidwe kena kake.—Luka 14:12-14.

  • Pofuna kugula cipulumutso.—Salimo 49:6, 7.

Ngati akupeleka pofuna kuthandizila pa zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Mwacitsanzo, si nzelu kupatsa munthu ndalama kuti akachovele njuga, kapena kukagulila mankhwala osokoneza bongo komanso kuti akamwe mowa n’kuledzela. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1) Komanso, si canzelu kupatsa ndalama munthu amene angakwanitse kugwila nchito na kudzipezela yekha zinthu zofunika koma amacita ulesi.—2 Atesalonika 3:10.

Ngati zikupangitsa wopelekayo kunyalanyaza udindo wosamalila banja lake. Baibo imati amuna okwatila ayenela kusamalila mabanja awo. (1 Timoteyo 5:8) Conco, sicingakhale coyenela kuti mwamuna azipeleka zinthu zambili kwa anthu ena cakuti banja lake likusoŵa zinthu zina zofunikila. Yesu anadzudzula anthu amene anali kulephela kusamalila makolo awo okalamba pokamba kuti cuma cawo conse ni “mphatso yopelekedwa kwa Mulungu.”—Maliko 7:9-13.

Mavesi a m’Baibo okamba za kupatsa

Miyambo 11:25: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandila mphoto, ndipo wothilila ena mosaumila nayenso adzathililidwa mosaumila.”

Mfundo yake: Kupatsa kumapindulitsa onse, wolandila komanso wopeleka.

Miyambo 19:17: “Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.”

Mfundo yake: Yehova amaona kuti ali na nkhongole kwa anthu amene amathandiza anthu ovutika, ndipo akulonjeza kuti adzawabwezela zimene anacitazo.

Mateyu 6:2: “Pamene ukupeleka mphatso zacifundo, usalize lipenga muja amacitila onyenga . . . kuti anthu awatamande.”

Mfundo yake: Tisamapeleke mphatso ponfuna cabe kuti tidzionetsele kwa anthu.

Machitidwe 20:35: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”

Mfundo yake: Kupeleka mphatso na mtima wonse kumathandiza munthu kukhala wacimwemwe.

2 Akorinto 9:7: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”

Mfundo yake: Mulungu amakondwela tikamapeleka mwa kufuna kwathu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani