KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBO
Yesaya 41:10—“Usacite Mantha, Pakuti Ndili Nawe”
“Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.”—Yesaya 41:10, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde ndidzakucilikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.”—Yesaya 41:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la Yesaya 41:10
Yehovaa Mulungu anatsimikizila anthu amene amamulambila mokhulupilika kuti adzawathandiza ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu kwambili.
“Ndili nawe.” Yehova anauza anthu omulambila kuti sayenela kuopa cifukwa sali okha. Popeza Yehova amaona mabvuto amene amakumana nao komanso amamva mapemphelo ao, zili ngati iye ali pamodzi nao.—Salimo 34:15; 1 Petulo 3:12.
“Ine ndine Mulungu wako.” Yehova amakhazikitsa mtima pansi anthu amene amamulambila powakumbutsa kuti iye amaonabe kuti ndi Mulungu wao ndiponso kuti io ndi anthu ake. Atumiki a Mulungu sayenela kukaikila kuti iye adzawathandiza zivute zitani.—Salimo 118:6; Aroma 8:32; Aheberi 13:6.
“Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.” Yehova anagwilitsa nchito mfundo zitatu pofuna kutsindika mfundo imodzi yakuti iye sangalephele ngakhale pang’ono kuthandiza anthu ake. Anagwilitsa nchito mawu ofanizila poonetsa zimene iye amacita anthu ake akafunikila thandizo. Munthu akagwa, Mulungu amatambasula dzanja lake lamanja kuti amudzutse.—Yesaya 41:13.
Njila yaikulu imene Mulungu amalimbitsila komanso kuthandizila anthu ake ndi mwa kugwilitsa nchito Mau ake, Baibo. (Yoswa 1:8; Aheberi 4:12) Mwacitsanzo, m’Baibo muli malangizo anzelu othandiza anthu amene akukumana ndi mavuto monga umphawi, matenda kapena kufeledwa. (Miyambo 2:6, 7) Mulungu angagwilitsenso nchito mzimu wake woyela, kapena kuti mphamvu yake yogwila nchito, kuti apatse anthu ake mphamvu zopilila mavuto.—Yesaya 40:29; Luka 11:13.
Nkhani yonse ya Yesaya 41:10
Mauwa analimbikitsa Ayuda okhulupilika omwe m’kupita kwa nthawi anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Yehova ananenelatu kuti cakumapeto kwa ukapolowo, kudzakhala malipoti okhudza mdani amene adzabwela kudzaononga mitundu yowazungulila komanso kuopseza Babulo. (Yesaya 41:2-4; 44:1-4) Ababulo ndi mitundu yoyandikana nao anali kudzachita mantha kwambili ndi malipotiwa, koma Ayuda sanayenele kuda nkhawa cifukwa Yehova analonjeza kuti adzawateteza. Iye anawatsimikizila zimenezi katatu powauza kuti: “Usachite mantha.”—Yesaya 41:5, 6, 10, 13, 14.
N’zoona kuti poyamba Yehova Mulungu ananena mauwa kuti alimbikitse Ayuda okhulupilika omwe anali kudzapita ku ukapolo ku Babulo. Koma anacititsa kuti mau a pa Yesaya 41:10 alembedwe m’Baibo n’colinga coti azilimbikitsa anthu ake onse. (Yesaya 40:8; Aroma 15:4) Masiku ano iye amathandiza anthu ake mofanana ndi mmene anali kucitila m’mbuyomu.
Welengani Yesaya caputala 41, mau am’munsi ndi malifalensi ake.
a Yehova ndilo dzina leni-leni la Mulungu.—Salimo 83:18.